আল-কোৰআনুল কাৰীমৰ অৰ্থানুবাদ - চিচেৱা অনুবাদ- খালিদ ইব্ৰাহীম বেতালা

Al-Hijr

external-link copy
1 : 15

الٓرۚ تِلۡكَ ءَايَٰتُ ٱلۡكِتَٰبِ وَقُرۡءَانٖ مُّبِينٖ

۞ Alif-Lâm-Râ. Izi ndi Aaya (ndime) za m’buku (lomwe lasonkhanitsa chilichonse chofunika,) ndi Qur’an yomveka bwino. info
التفاسير:

external-link copy
2 : 15

رُّبَمَا يَوَدُّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لَوۡ كَانُواْ مُسۡلِمِينَ

Nthawi zambiri omwe sadakhulupirire (pamene adzakhala m’Moto) adzalakalaka kuti akadakhala okhulupirira (pamoyo wa pa dziko lapansi). info
التفاسير:

external-link copy
3 : 15

ذَرۡهُمۡ يَأۡكُلُواْ وَيَتَمَتَّعُواْ وَيُلۡهِهِمُ ٱلۡأَمَلُۖ فَسَوۡفَ يَعۡلَمُونَ

Asiye azidya (chakudya monga momwe zidyera nyama) ndi kusangalala; ndipo chiyembekezo chiziwatangwanitsa ndi kuwanyenga; posachedwa adziwa (kuti zimene amaziyembekezerazo nzabodza). info
التفاسير:

external-link copy
4 : 15

وَمَآ أَهۡلَكۡنَا مِن قَرۡيَةٍ إِلَّا وَلَهَا كِتَابٞ مَّعۡلُومٞ

Ndipo sitidaononge mudzi uliwonse (m’midzi yochita zoipa) koma udali ndi nthawi yake (youwonongera) yodziwika. info
التفاسير:

external-link copy
5 : 15

مَّا تَسۡبِقُ مِنۡ أُمَّةٍ أَجَلَهَا وَمَا يَسۡتَـٔۡخِرُونَ

Ndipo palibe mtundu wa anthu umene ungaitsogolere nthawi yake (yofera) kapena kuichedwetsa (itakwana kale). info
التفاسير:

external-link copy
6 : 15

وَقَالُواْ يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِي نُزِّلَ عَلَيۡهِ ٱلذِّكۡرُ إِنَّكَ لَمَجۡنُونٞ

Ndipo (osakhulupirira) akunena (mwachipongwe) “E iwe amene wavumbulutsiridwa ulaliki! Ndithudi ndiwe wamisala.” info
التفاسير:

external-link copy
7 : 15

لَّوۡمَا تَأۡتِينَا بِٱلۡمَلَٰٓئِكَةِ إِن كُنتَ مِنَ ٱلصَّٰدِقِينَ

“Bwanji iwe osatibweretsera angelo (kuti akuchitire umboni) ngati uli mmodzi waonena zoona?” info
التفاسير:

external-link copy
8 : 15

مَا نُنَزِّلُ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةَ إِلَّا بِٱلۡحَقِّ وَمَا كَانُوٓاْ إِذٗا مُّنظَرِينَ

(Allah akuwauza:) “Ife sititsitsa angelo pokhapokha kutatsimikizika (tikawatuma kukapereka chilango kwa anthu). Ndipo pamenepo sangapatsidwe nthawi.” info
التفاسير:

external-link copy
9 : 15

إِنَّا نَحۡنُ نَزَّلۡنَا ٱلذِّكۡرَ وَإِنَّا لَهُۥ لَحَٰفِظُونَ

Ndithu Ife ndife omwe tavumbulutsa Qur’an, ndipo ndithudi, tiisunga.[244] info

[244] Omasulira Qur’an adati Allah Mwini wake adalonjeza udindo woisunga Qur’an ndi kuiteteza kuti anthu asathe kuikapo manja awo posintha ndondomeko ya mawu ake kapena matanthandauzo ake, poonjezerapo malembo ena kapena kuchepetsa monga momwe zidachitikira ndi mabuku ena omwe Allah adawasiira anthu kuti awasunge ndi kuwateteza.
Qur’an yomwe tikuwerenga lero ndi yomweyo imene idalinso kuwerengedwa m’nthawi ya Mtumiki Muhammad (s.a.w). Palibe mawu oonjeza kapena kuchotsa.

التفاسير:

external-link copy
10 : 15

وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا مِن قَبۡلِكَ فِي شِيَعِ ٱلۡأَوَّلِينَ

Ndithudi tidatuma (atumiki) patsogolo pako m’magulu (a anthu) akale, oyamba. info
التفاسير:

external-link copy
11 : 15

وَمَا يَأۡتِيهِم مِّن رَّسُولٍ إِلَّا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ

Ndipo sadali kuwadzera mtumiki aliyense, koma ankamchitira chipongwe. info
التفاسير:

external-link copy
12 : 15

كَذَٰلِكَ نَسۡلُكُهُۥ فِي قُلُوبِ ٱلۡمُجۡرِمِينَ

Momwemo tikuupititsa (mkhalidwe wachipongwewu) m’mitima mwa oipa. info
التفاسير:

external-link copy
13 : 15

لَا يُؤۡمِنُونَ بِهِۦ وَقَدۡ خَلَتۡ سُنَّةُ ٱلۡأَوَّلِينَ

Koma saikhulupirira Qur’aniyi chikhalirecho mafanizo a anthu oyamba awadutsa (ndipo aona momwe tidawaonongera). info
التفاسير:

external-link copy
14 : 15

وَلَوۡ فَتَحۡنَا عَلَيۡهِم بَابٗا مِّنَ ٱلسَّمَآءِ فَظَلُّواْ فِيهِ يَعۡرُجُونَ

Ndipo tikadawatsekulira (awa osakhulupirira) khomo lakumwamba ndipo nkukhala akukwera m’menemo (ndi kutsika monga momwe amafunira kuti zimenezo zikhale chozizwitsa cha Mtumiki), info
التفاسير:

external-link copy
15 : 15

لَقَالُوٓاْ إِنَّمَا سُكِّرَتۡ أَبۡصَٰرُنَا بَلۡ نَحۡنُ قَوۡمٞ مَّسۡحُورُونَ

Akadati: “Ndithu maso athu aledzera; (iyayi) koma ndife anthu olodzedwa (tikuona zomwe sindizo).”[245] info

[245] Allah akuti akadawatsekulira makomo akumwamba monga momwe adafunira nakwerako nkuona ufumu wa Allah ndi angelo ali yakaliyakali, sakadakhulupilirabe chifukwa chakuuma kwa mitima yawo. Chimene akadanena nkuti mitu yazungulira.

التفاسير: