വിശുദ്ധ ഖുർആൻ പരിഭാഷ - ചെവ്വ വിവർത്തനം - ഖാലിദ് ഇബ്രാഹിം ബറ്റിയാലാ

പേജ് നമ്പർ:close

external-link copy
36 : 28

فَلَمَّا جَآءَهُم مُّوسَىٰ بِـَٔايَٰتِنَا بَيِّنَٰتٖ قَالُواْ مَا هَٰذَآ إِلَّا سِحۡرٞ مُّفۡتَرٗى وَمَا سَمِعۡنَا بِهَٰذَا فِيٓ ءَابَآئِنَا ٱلۡأَوَّلِينَ

Pamene Mûsa adawadzera ndi zizindikiro zathu zoonekera poyera, adati: “Ichi sichina koma ndi matsenga wopeka; sitidamvepo zimenezi kumakolo athu akale.” info
التفاسير:

external-link copy
37 : 28

وَقَالَ مُوسَىٰ رَبِّيٓ أَعۡلَمُ بِمَن جَآءَ بِٱلۡهُدَىٰ مِنۡ عِندِهِۦ وَمَن تَكُونُ لَهُۥ عَٰقِبَةُ ٱلدَّارِۚ إِنَّهُۥ لَا يُفۡلِحُ ٱلظَّٰلِمُونَ

Ndipo Mûsa adanena: “Mbuye wanga akumudziwa yemwe wadza ndi chiongoko kuchokera kwa Iye ndi yemwe adzakhala ndi mathero a pokhala pabwino. Ndithu ochita zoipa sakapambana.” info
التفاسير:

external-link copy
38 : 28

وَقَالَ فِرۡعَوۡنُ يَٰٓأَيُّهَا ٱلۡمَلَأُ مَا عَلِمۡتُ لَكُم مِّنۡ إِلَٰهٍ غَيۡرِي فَأَوۡقِدۡ لِي يَٰهَٰمَٰنُ عَلَى ٱلطِّينِ فَٱجۡعَل لِّي صَرۡحٗا لَّعَلِّيٓ أَطَّلِعُ إِلَىٰٓ إِلَٰهِ مُوسَىٰ وَإِنِّي لَأَظُنُّهُۥ مِنَ ٱلۡكَٰذِبِينَ

Ndipo Farawo adati: “E inu nduna (zanga)! Sindidziwa kuti inu muli ndi mulungu (wina) kupatula ine. Choncho, iwe Haamana! Ndiwotchere njerwa tero undimangire chipilala kuti mwina mwake ndingamsuzumire Mulungu wa Mûsa. Ndithu ine ndikumganizira kuti ndi mmodzi wa abodza.” info
التفاسير:

external-link copy
39 : 28

وَٱسۡتَكۡبَرَ هُوَ وَجُنُودُهُۥ فِي ٱلۡأَرۡضِ بِغَيۡرِ ٱلۡحَقِّ وَظَنُّوٓاْ أَنَّهُمۡ إِلَيۡنَا لَا يُرۡجَعُونَ

Ndipo iye pamodzi ndi makamu ake ankhondo adadzitukumula pa dziko popanda chilungamo ndipo ankaganiza kuti iwo sadzabwelere kwa Ife. info
التفاسير:

external-link copy
40 : 28

فَأَخَذۡنَٰهُ وَجُنُودَهُۥ فَنَبَذۡنَٰهُمۡ فِي ٱلۡيَمِّۖ فَٱنظُرۡ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلظَّٰلِمِينَ

Koma tidamulanga ndi magulu ake ankhondo ndi kuwaponya m’nyanja; yang’ana, kodi adali bwanji mathero a ochita zoipa. info
التفاسير:

external-link copy
41 : 28

وَجَعَلۡنَٰهُمۡ أَئِمَّةٗ يَدۡعُونَ إِلَى ٱلنَّارِۖ وَيَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ لَا يُنصَرُونَ

Ndipo tidawachita kukhala atsogoleri oitanira (anthu) ku Moto; ndipo tsiku la chiweruziro (Qiyâma) sadzathandizidwa. info
التفاسير:

external-link copy
42 : 28

وَأَتۡبَعۡنَٰهُمۡ فِي هَٰذِهِ ٱلدُّنۡيَا لَعۡنَةٗۖ وَيَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ هُم مِّنَ ٱلۡمَقۡبُوحِينَ

Tidawatsatiziranso matembelero padziko lino lapansi. Ndipo tsiku la chimaliziro iwo adzakhala oyipitsitsa (ndi kuthamangitsidwa ku chifundo cha Allah). info
التفاسير:

external-link copy
43 : 28

وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَا مُوسَى ٱلۡكِتَٰبَ مِنۢ بَعۡدِ مَآ أَهۡلَكۡنَا ٱلۡقُرُونَ ٱلۡأُولَىٰ بَصَآئِرَ لِلنَّاسِ وَهُدٗى وَرَحۡمَةٗ لَّعَلَّهُمۡ يَتَذَكَّرُونَ

Ndipo ndithu Mûsa tidampatsa buku pambuyo powononga mibadwo yoyamba kuti likhale chiphanulamaso cha anthu (kuti liwaunikire ku njira yolungama), ndi kuti likhale chiongoko ndi chifundo kuti iwo akumbukire. info
التفاسير: