വിശുദ്ധ ഖുർആൻ പരിഭാഷ - ചെവ്വ വിവർത്തനം - ഖാലിദ് ഇബ്രാഹിം ബറ്റിയാലാ

പേജ് നമ്പർ:close

external-link copy
22 : 28

وَلَمَّا تَوَجَّهَ تِلۡقَآءَ مَدۡيَنَ قَالَ عَسَىٰ رَبِّيٓ أَن يَهۡدِيَنِي سَوَآءَ ٱلسَّبِيلِ

Ndipo pamene adalunjika (kumka) ku Madiyan adati: “Mwina Mbuye wanga andiongolera kunjira yoyenera.” info
التفاسير:

external-link copy
23 : 28

وَلَمَّا وَرَدَ مَآءَ مَدۡيَنَ وَجَدَ عَلَيۡهِ أُمَّةٗ مِّنَ ٱلنَّاسِ يَسۡقُونَ وَوَجَدَ مِن دُونِهِمُ ٱمۡرَأَتَيۡنِ تَذُودَانِۖ قَالَ مَا خَطۡبُكُمَاۖ قَالَتَا لَا نَسۡقِي حَتَّىٰ يُصۡدِرَ ٱلرِّعَآءُۖ وَأَبُونَا شَيۡخٞ كَبِيرٞ

Ndipo pamene adawafika madzi a ku Madiyan (pomwe anthu kumeneko ankatungapo madzi), adapeza gulu la anthu likumwetsa (ziweto zawo), ndipo pambali (pa gululo) adapeza akazi awiri akuletsa (ziweto zawo kuti zisapite kukamwa ndi ziweto zinazo). (Mûsa) adati: “Kodi mwatani? (Bwanji simukuzimwetsa ziweto zanu?)” Iwo Adati: “Sitingamwetse (ziweto zathu) mpaka abusa atachotsa (ziweto zawo, chifukwa sitingathe kulimbana nawo). Ndipo bambo wathu ndinkhalamba yaikulu kwabasi.” info
التفاسير:

external-link copy
24 : 28

فَسَقَىٰ لَهُمَا ثُمَّ تَوَلَّىٰٓ إِلَى ٱلظِّلِّ فَقَالَ رَبِّ إِنِّي لِمَآ أَنزَلۡتَ إِلَيَّ مِنۡ خَيۡرٖ فَقِيرٞ

Choncho (Mûsa) adawamwetsera (ziweto zawo); kenako adapita pamthunzi, ndipo adati: “E Mbuye wanga! Ndithu ine ndiwosaukira chabwino chimene munditsitsire.” info
التفاسير:

external-link copy
25 : 28

فَجَآءَتۡهُ إِحۡدَىٰهُمَا تَمۡشِي عَلَى ٱسۡتِحۡيَآءٖ قَالَتۡ إِنَّ أَبِي يَدۡعُوكَ لِيَجۡزِيَكَ أَجۡرَ مَا سَقَيۡتَ لَنَاۚ فَلَمَّا جَآءَهُۥ وَقَصَّ عَلَيۡهِ ٱلۡقَصَصَ قَالَ لَا تَخَفۡۖ نَجَوۡتَ مِنَ ٱلۡقَوۡمِ ٱلظَّٰلِمِينَ

Kenako mmodzi mwa asungwana aja adadza kwa iye uku akuyenda mwa manyazi. (Msungwanayo) adati: “Ndithu tate wanga akukuitana kuti akakupatse malipiro pakutimwetsera (ziweto zathu).” Choncho pamene adamdzera, (mneneri Shuaib) ndikumulongosolera nkhani, adati: “Usaope; wapulumuka kwa anthu oipa.” info
التفاسير:

external-link copy
26 : 28

قَالَتۡ إِحۡدَىٰهُمَا يَٰٓأَبَتِ ٱسۡتَـٔۡجِرۡهُۖ إِنَّ خَيۡرَ مَنِ ٱسۡتَـٔۡجَرۡتَ ٱلۡقَوِيُّ ٱلۡأَمِينُ

Mmodzi wa iwo (asungwana aja) adanena: “E bambo wanga mulembeni ntchito (kuti akhale woweta ziweto m’malo mwa ife). Ndithu amene alibwino kuti mumulembe ntchito ndi yemwe ali wamphamvu wokhulupirika (zonse ziwiri mwa iyeyu zirimo.) info
التفاسير:

external-link copy
27 : 28

قَالَ إِنِّيٓ أُرِيدُ أَنۡ أُنكِحَكَ إِحۡدَى ٱبۡنَتَيَّ هَٰتَيۡنِ عَلَىٰٓ أَن تَأۡجُرَنِي ثَمَٰنِيَ حِجَجٖۖ فَإِنۡ أَتۡمَمۡتَ عَشۡرٗا فَمِنۡ عِندِكَۖ وَمَآ أُرِيدُ أَنۡ أَشُقَّ عَلَيۡكَۚ سَتَجِدُنِيٓ إِن شَآءَ ٱللَّهُ مِنَ ٱلصَّٰلِحِينَ

(Shuaib) adati (kwa iye): “Ine ndikufuna kukukwatitsa mmodzi mwa asungwana anga awiriwa, chiongo chake ndikundigwilira ntchito zaka zisanu ndi zitatu; ngati utakwaniritsa zaka khumi ndiye kuti nkufuna kwako. Sindikufuna kukuvutitsa (pokuchulukitsira zaka); undipeza, Allah akafuna, kuti ndine mmodzi wa anthu abwino, (wokwaniritsa lonjezo).” info
التفاسير:

external-link copy
28 : 28

قَالَ ذَٰلِكَ بَيۡنِي وَبَيۡنَكَۖ أَيَّمَا ٱلۡأَجَلَيۡنِ قَضَيۡتُ فَلَا عُدۡوَٰنَ عَلَيَّۖ وَٱللَّهُ عَلَىٰ مَا نَقُولُ وَكِيلٞ

(Mûsa) adati: “Zimene mwandilonjezazi zili pakati pa ine ndi inu. Nyengo iriyonse imene ndikwaniritse pa ziwirizi (pogwira ntchitoyo, ndiye kuti ndakwaniritsa lonjezo lanu) musandichitire mtopola. Ndipo Allah ndiye Muyang’aniri pa zomwe tikukambazi.” info
التفاسير: