വിശുദ്ധ ഖുർആൻ പരിഭാഷ - ചെവ്വ വിവർത്തനം - ഖാലിദ് ഇബ്രാഹിം ബറ്റിയാലാ

പേജ് നമ്പർ:close

external-link copy
91 : 21

وَٱلَّتِيٓ أَحۡصَنَتۡ فَرۡجَهَا فَنَفَخۡنَا فِيهَا مِن رُّوحِنَا وَجَعَلۡنَٰهَا وَٱبۡنَهَآ ءَايَةٗ لِّلۡعَٰلَمِينَ

Ndipo (atchulire za Mariya) yemwe adauteteza umaliseche wake (podzisunga); ndipo tidauzira mwa iye Mzimu Wathu, ndipo tidamchita iye ndi mwana wake kukhala chizizwa (cha Allah) kwa zolengedwa zonse. info
التفاسير:

external-link copy
92 : 21

إِنَّ هَٰذِهِۦٓ أُمَّتُكُمۡ أُمَّةٗ وَٰحِدَةٗ وَأَنَا۠ رَبُّكُمۡ فَٱعۡبُدُونِ

Ndithu uwu mpingo wanu, ndimpingo umodzi, ndipo Ine ndine Mbuye wanu; choncho ndipembedzeni. info
التفاسير:

external-link copy
93 : 21

وَتَقَطَّعُوٓاْ أَمۡرَهُم بَيۡنَهُمۡۖ كُلٌّ إِلَيۡنَا رَٰجِعُونَ

Koma iwo adaswa chinthu chawochi pakati pawo (tero adakhala mipingo yosiyanasiyana). Onse adzabwerera kwa Ife. info
التفاسير:

external-link copy
94 : 21

فَمَن يَعۡمَلۡ مِنَ ٱلصَّٰلِحَٰتِ وَهُوَ مُؤۡمِنٞ فَلَا كُفۡرَانَ لِسَعۡيِهِۦ وَإِنَّا لَهُۥ كَٰتِبُونَ

Ndipo amene achite ntchito zabwino uku ali wokhulupirira, khama lake silidzakanidwa; ndithunso Ife tikumlembera zonse zimene akuchita. info
التفاسير:

external-link copy
95 : 21

وَحَرَٰمٌ عَلَىٰ قَرۡيَةٍ أَهۡلَكۡنَٰهَآ أَنَّهُمۡ لَا يَرۡجِعُونَ

Ndipo nkosatheka kwa eni mudzi umene tidauononga chifukwa cha machimo awo kuti asabwelere kwa Ife; (koma ndithu abwerera). info
التفاسير:

external-link copy
96 : 21

حَتَّىٰٓ إِذَا فُتِحَتۡ يَأۡجُوجُ وَمَأۡجُوجُ وَهُم مِّن كُلِّ حَدَبٖ يَنسِلُونَ

Kufikira pamene Yaajuju ndi Maajuju adzatsekulilidwa (mpanda wawo), ndipo iwo adzakhala akuthamanga kuchokera m’phiri lililonse. info
التفاسير:

external-link copy
97 : 21

وَٱقۡتَرَبَ ٱلۡوَعۡدُ ٱلۡحَقُّ فَإِذَا هِيَ شَٰخِصَةٌ أَبۡصَٰرُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ يَٰوَيۡلَنَا قَدۡ كُنَّا فِي غَفۡلَةٖ مِّنۡ هَٰذَا بَلۡ كُنَّا ظَٰلِمِينَ

Ndipo lonjezo la choonadi lidzafika; pamenepo maso a omwe sadakhulupirire, adzatong’oka uku akunena: “Tsoka pa ife! Ndithu tidali osalabadira (za chinthu) ichi; koma tidali oipa, (odzichitira tokha zoipa.)” info
التفاسير:

external-link copy
98 : 21

إِنَّكُمۡ وَمَا تَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ حَصَبُ جَهَنَّمَ أَنتُمۡ لَهَا وَٰرِدُونَ

Ndithu inu ndi amene mukuwapembedza kusiya Allah, ndinu nkhuni za ku Jahannam. Ndipo inu (Jahannamyo) mudzalowa. info
التفاسير:

external-link copy
99 : 21

لَوۡ كَانَ هَٰٓؤُلَآءِ ءَالِهَةٗ مَّا وَرَدُوهَاۖ وَكُلّٞ فِيهَا خَٰلِدُونَ

Ngati awa akadakhala milungu yeniyeni, ndiye kuti sakadailowa, mmenemo onse adzakhala nthawi yaitali. info
التفاسير:

external-link copy
100 : 21

لَهُمۡ فِيهَا زَفِيرٞ وَهُمۡ فِيهَا لَا يَسۡمَعُونَ

Mmenemo iwo adzakhala akubuula ndipo iwo mmenemo sadzamva (chifukwa makutu adzagontha). info
التفاسير:

external-link copy
101 : 21

إِنَّ ٱلَّذِينَ سَبَقَتۡ لَهُم مِّنَّا ٱلۡحُسۡنَىٰٓ أُوْلَٰٓئِكَ عَنۡهَا مُبۡعَدُونَ

Ndithu amene ubwino wathu udawafika, iwo adzatalikitsidwa nawo (motowo). info
التفاسير: