വിശുദ്ധ ഖുർആൻ പരിഭാഷ - ചെവ്വ വിവർത്തനം - ഖാലിദ് ഇബ്രാഹിം ബറ്റിയാലാ

പേജ് നമ്പർ:close

external-link copy
36 : 21

وَإِذَا رَءَاكَ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ إِن يَتَّخِذُونَكَ إِلَّا هُزُوًا أَهَٰذَا ٱلَّذِي يَذۡكُرُ ءَالِهَتَكُمۡ وَهُم بِذِكۡرِ ٱلرَّحۡمَٰنِ هُمۡ كَٰفِرُونَ

Ndipo amene sadakhulupirire akakuona, akungokuchitira chipongwe. “Kodi ndi uyu yemwe akutchula milungu yanu (mwachipongwe)?” Pomwe iwo ndi amene akukana zakutchula (Allah) Wachifundo chambiri. info
التفاسير:

external-link copy
37 : 21

خُلِقَ ٱلۡإِنسَٰنُ مِنۡ عَجَلٖۚ سَأُوْرِيكُمۡ ءَايَٰتِي فَلَا تَسۡتَعۡجِلُونِ

Munthu walengedwa ndi chikhalidwe chokonda zinthu (zake zonse) mwachangu. Posachedwapa ndikusonyezani zisonyezo Zanga; choncho musandifulumizitse (kukubweretserani chilango changa). info
التفاسير:

external-link copy
38 : 21

وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هَٰذَا ٱلۡوَعۡدُ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ

Ndipo (osakhulupirira) akuti: “Kodi malonjezo awa adzakwaniritsidwa liti, ngati mukunena zoona?” info
التفاسير:

external-link copy
39 : 21

لَوۡ يَعۡلَمُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ حِينَ لَا يَكُفُّونَ عَن وُجُوهِهِمُ ٱلنَّارَ وَلَا عَن ظُهُورِهِمۡ وَلَا هُمۡ يُنصَرُونَ

Chikhala kuti amene sadakhulupirire akudziwa chilango chimene chidzawapeza panthawi yomwe sangathe kutchinjiriza Moto kunkhope zawo ndi kumisana yawo ndipo kuti sadzathandizidwa, (sakadanena zimenezi.) info
التفاسير:

external-link copy
40 : 21

بَلۡ تَأۡتِيهِم بَغۡتَةٗ فَتَبۡهَتُهُمۡ فَلَا يَسۡتَطِيعُونَ رَدَّهَا وَلَا هُمۡ يُنظَرُونَ

Koma (Qiyâma) idzawadzera mwadzidzidzi ndi kuwadzidzimutsa; kenako sadzatha kuibweza kapena kupatsidwa danga (kuti achite zomwe sadachite.) info
التفاسير:

external-link copy
41 : 21

وَلَقَدِ ٱسۡتُهۡزِئَ بِرُسُلٖ مِّن قَبۡلِكَ فَحَاقَ بِٱلَّذِينَ سَخِرُواْ مِنۡهُم مَّا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ

Ndipo ndithu atumiki adachitidwa chipongwe patsogolo pako; choncho amene adachita chipongwe mwa iwo, zidawadzera zomwe adali kuzichita chipongwe. info
التفاسير:

external-link copy
42 : 21

قُلۡ مَن يَكۡلَؤُكُم بِٱلَّيۡلِ وَٱلنَّهَارِ مِنَ ٱلرَّحۡمَٰنِۚ بَلۡ هُمۡ عَن ذِكۡرِ رَبِّهِم مُّعۡرِضُونَ

Nena: “Kodi ndani angakutetezeni usiku ndi usana ku masautso a (Allah) Wachifundo Chambiri?” Koma iwo akunyozera kukumbuka Mbuye wawo. info
التفاسير:

external-link copy
43 : 21

أَمۡ لَهُمۡ ءَالِهَةٞ تَمۡنَعُهُم مِّن دُونِنَاۚ لَا يَسۡتَطِيعُونَ نَصۡرَ أَنفُسِهِمۡ وَلَا هُم مِّنَّا يُصۡحَبُونَ

Kapena ali nayo milungu yowatchinjiriza m’malo mwa Ife? (Milunguyo) siingathe kudzithandiza yokha (nanga ndiye ingathe kuthandiza ena?) Ndipo (milungu) imeneyo siidzasamalidwa ndi Ife. info
التفاسير:

external-link copy
44 : 21

بَلۡ مَتَّعۡنَا هَٰٓؤُلَآءِ وَءَابَآءَهُمۡ حَتَّىٰ طَالَ عَلَيۡهِمُ ٱلۡعُمُرُۗ أَفَلَا يَرَوۡنَ أَنَّا نَأۡتِي ٱلۡأَرۡضَ نَنقُصُهَا مِنۡ أَطۡرَافِهَآۚ أَفَهُمُ ٱلۡغَٰلِبُونَ

Koma awa (osakhulupirira) tidawasangalatsa ndi makolo awo kufikira nthawi ya moyo wawo idatalika; kodi saona kuti tikulidzera dziko lawo ndikulichepetsa malire ake?. Nanga kodi iwo ndiwo opambana? info
التفاسير: