വിശുദ്ധ ഖുർആൻ പരിഭാഷ - ചെവ്വ വിവർത്തനം - ഖാലിദ് ഇബ്രാഹിം ബറ്റിയാലാ

പേജ് നമ്പർ:close

external-link copy
234 : 2

وَٱلَّذِينَ يُتَوَفَّوۡنَ مِنكُمۡ وَيَذَرُونَ أَزۡوَٰجٗا يَتَرَبَّصۡنَ بِأَنفُسِهِنَّ أَرۡبَعَةَ أَشۡهُرٖ وَعَشۡرٗاۖ فَإِذَا بَلَغۡنَ أَجَلَهُنَّ فَلَا جُنَاحَ عَلَيۡكُمۡ فِيمَا فَعَلۡنَ فِيٓ أَنفُسِهِنَّ بِٱلۡمَعۡرُوفِۗ وَٱللَّهُ بِمَا تَعۡمَلُونَ خَبِيرٞ

234, Ndipo mwa inu amene amwalira nasiya akazi, choncho (akaziwo) ayembekezere (asakwatiwe) miyezi inayi ndi masiku khumi. Ndipo akakwanitsa nyengo ya chiyembekezero chawo cha edda, sitchimo kwa inu pazimene akaziwo adzichitira okha (monga kudzikongoletsa ndi kudziwonetsa kwa ofunsira ukwati); motsatira malamulo a Shariya. Ndipo Allah Ngodziwa zonse zimene mukuchita. info
التفاسير:

external-link copy
235 : 2

وَلَا جُنَاحَ عَلَيۡكُمۡ فِيمَا عَرَّضۡتُم بِهِۦ مِنۡ خِطۡبَةِ ٱلنِّسَآءِ أَوۡ أَكۡنَنتُمۡ فِيٓ أَنفُسِكُمۡۚ عَلِمَ ٱللَّهُ أَنَّكُمۡ سَتَذۡكُرُونَهُنَّ وَلَٰكِن لَّا تُوَاعِدُوهُنَّ سِرًّا إِلَّآ أَن تَقُولُواْ قَوۡلٗا مَّعۡرُوفٗاۚ وَلَا تَعۡزِمُواْ عُقۡدَةَ ٱلنِّكَاحِ حَتَّىٰ يَبۡلُغَ ٱلۡكِتَٰبُ أَجَلَهُۥۚ وَٱعۡلَمُوٓاْ أَنَّ ٱللَّهَ يَعۡلَمُ مَا فِيٓ أَنفُسِكُمۡ فَٱحۡذَرُوهُۚ وَٱعۡلَمُوٓاْ أَنَّ ٱللَّهَ غَفُورٌ حَلِيمٞ

Ndipo sitchimo kwa inu kupereka mawu okuluwika ofunsira ukwati kwa akaziwo (pamene chiyembekezero cha edda yawo chisanathe. Ndiponso palibe uchimo) kapena kubisa mu mtima mwanu, kuwakwatira (chiyembekezo chawo chikadzatha). Allah wadziwa kuti mukhala mukuwakumbukira akaziwo. Koma musawalonjeze mobisa (kuti: “Ikatha edda ndidzakukwatira).” Koma nenani mawu abwino. Ndipo musatsimikize kumanga ukwati mpaka nyengo yolembedwayo ikwanire. Ndipo dziwani kuti Allah akudziwa zomwe zili m’mitima mwanu. Tero muopeni (Allah), dziwaninso kuti Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngoleza. info
التفاسير:

external-link copy
236 : 2

لَّا جُنَاحَ عَلَيۡكُمۡ إِن طَلَّقۡتُمُ ٱلنِّسَآءَ مَا لَمۡ تَمَسُّوهُنَّ أَوۡ تَفۡرِضُواْ لَهُنَّ فَرِيضَةٗۚ وَمَتِّعُوهُنَّ عَلَى ٱلۡمُوسِعِ قَدَرُهُۥ وَعَلَى ٱلۡمُقۡتِرِ قَدَرُهُۥ مَتَٰعَۢا بِٱلۡمَعۡرُوفِۖ حَقًّا عَلَى ٱلۡمُحۡسِنِينَ

Palibe tchimo pa inu mutawapatsa akazi mawu achilekaniro pomwe simudakhudzane nawo; pomwenso simudawadziwitse gawo la chiwongo chawo; koma asangalatseni (powapatsa chilekaniro). Wopeza bwino apereke malinga ndikupeza bwino kwake; wochepekedwa apereke malingana ndikuchepekedwa kwake. Chilekaniro chosangalatsacho chikhale molingana ndi malamulo a Shariya, ndipo ndilamulo kwa ochita zabwino.[39] info

[39] Kuthetsa ukwati nkololedwa m’Chisilamu. Koma ngakhale nkololedwa, Shariya ya Chisilamu imanyansidwa ndimachitidwe othetsa ukwati pokhapokha pakhale zifukwa zovomerezeka ndi Shariya.
Ngati patapezeka zifukwa zochititsa kuti ukwati uthe nkofunika kuti mkwati amchitire mkwatibwi zabwino monga izi:
a) ampatse chiwongo (mahar) chimene chinatsalira ngati sadamalize kupereka.
b) ampatse ndalama zina zapadera zomtulutsira mkaziyo m’nyumba.
c) ampatse chovala, malo okhala, chakudya patsiku lililonse kufikira edda yake itatha ngakhale eddayo itatenga nthawi yaitali.
d) amsiire zinthu zake kuti atenge pamodzi ndi zimene adampatsa. Nkosaloledwa kumlanda chilichonse mwa zimenezi.

التفاسير:

external-link copy
237 : 2

وَإِن طَلَّقۡتُمُوهُنَّ مِن قَبۡلِ أَن تَمَسُّوهُنَّ وَقَدۡ فَرَضۡتُمۡ لَهُنَّ فَرِيضَةٗ فَنِصۡفُ مَا فَرَضۡتُمۡ إِلَّآ أَن يَعۡفُونَ أَوۡ يَعۡفُوَاْ ٱلَّذِي بِيَدِهِۦ عُقۡدَةُ ٱلنِّكَاحِۚ وَأَن تَعۡفُوٓاْ أَقۡرَبُ لِلتَّقۡوَىٰۚ وَلَا تَنسَوُاْ ٱلۡفَضۡلَ بَيۡنَكُمۡۚ إِنَّ ٱللَّهَ بِمَا تَعۡمَلُونَ بَصِيرٌ

Ndipo ngati mwalekana nawo (akaziwo) musanakhudzane nawo mutawadziwitsa gawo la chiwongo chawo, apatseni theka la chimene mudagwirizana kuwapatsa pokhapokha ngati akaziwo atakana okha (theka la chiwongocho), kapena (mwamuna) uja yemwe kumangitsa kwa ukwati kuli m’manja mwake amusiire (chiwongo chonsecho mkaziyo). Ndipo ngati mutasiirana (zimenezo) zingakuyandikitseni kumbali yoopa Allah. Ndipo musaiwale kuchitirana zabwino pakati panu (ngakhale kuti mukulekana). Ndithudi Allah akuona zonse zimene mukuchita.[40] info

[40] Ngati udamkwatira mkazi ndipo nkulekana naye usanalowane naye, umpatse theka lachiwongo chomwe chidatchulidwa. Ngati udampatsa chiwongo chonse, ndiye kuti akubwezere theka lake. Koma ndibwino kwa mwamuna kumpatsa mkazi chiwongo chonse ngati anali asanampatse. Ngati anampatsa asaitanitsenso chiwongocho. Ndibwinonso kwa mkazi kubweza chiwongo chonse ngati adampatsa chonse, kapena kukana kuti asampatse ngati anali asanapatsidwe. Aliyense mwa awiriwa asakhale ndi chibaba chofuna kupeza ndalama pakutha pa ukwatiwo. Malamulo tanenawa amagwira ntchito ngati chiwongo chidatchulidwa kuchuluka kwake pomwe ankafunsira ukwati. Koma ngati chiwongocho sanachitchule kuchuluka kwake kotero kuti sadagwirizane za chiwongocho kuti adzapereka mwakutimwakuti, pamenepa ndiye kuti ampatse chinthu cholekanira choti chimsangalatse. Ili ndilo tanthauzo la zomwe zatchulidwa m’ndime ya 236.
Ndithudi apa akutilangiza mwamphamvu kuti tizichitirana zabwino ngakhale panthawi yolekana ukwati. Anthu asaiwale ubwino ndi chikondi zomwe ankachitirana pakati pawo.

التفاسير: