[25] Tanthauzo lake nkuti alipo ena mwa anthu omwe angakukometsere zoyankhula zawo ndi kuthwa kwa lirime lawo pomwe iwo chikhalirecho akungoyankhula kuti apeze zinthu za m’dziko.
Ndimeyi ikufotokoza za Al-Akhnas bun Sharik yemwe amati akakumana ndi Mtumiki (s.a.w), amatamanda ndi kusonyeza chikhulupiliro chabodza. Koma akachoka pamaso pa mtumiki (s.a.w) amayenda pa dziko ncholinga choononga.
Umo ndi momwe alili makhalidwe a anthu ena, amangokometsa mawu pomwe zochita zawo nzauve. Tero tichenjere ndi anthu otere.
[26] Ndimeyi idavumbulutsidwa pankhani yokhudzana ndi wophunzira wina wa Mtumiki (s.a.w) dzina lake Suhaib Al-Rumi. Iyeyu pamene anafuna kusamuka ku Makka kupita ku Madina ma Quraish anamutsekereza, ndipo adamuuza kuti ngati akufuna kusamuka asiye chuma chake chonse, kupanda kutero sangasamuke. Choncho adalolera kusiya chuma chake chonse pofuna kudzipulumutsa yekha kuti asamukire ku Madina. Allah anakondwera nayo nkhaniyi ndipo adavumbulutsa ndimeyi.
[27] E inu amene mwakhulupilira! Inu eni mabuku, gonjerani Allah. Ndipo lowani m’Chisilamu kwathunthu posachisokoneza ndi chinachache. Mawuwa adanenedwa pamene Abdullahi bun Salaami adalowa m’Chisilamu yemwe adali mkulu wachiyuda. lye adapempha chilolezo kwa mtumiki (s.a.w) kuti aziliremekezabe tsiku la Sabata (la chiweru) ndi kuti aziwerenga mawu a m’Taurati mu Swala zake zausiku.