വിശുദ്ധ ഖുർആൻ പരിഭാഷ - ചെവ്വ വിവർത്തനം - ഖാലിദ് ഇബ്രാഹിം ബറ്റിയാലാ

പേജ് നമ്പർ:close

external-link copy
64 : 12

قَالَ هَلۡ ءَامَنُكُمۡ عَلَيۡهِ إِلَّا كَمَآ أَمِنتُكُمۡ عَلَىٰٓ أَخِيهِ مِن قَبۡلُ فَٱللَّهُ خَيۡرٌ حَٰفِظٗاۖ وَهُوَ أَرۡحَمُ ٱلرَّٰحِمِينَ

(Ya’qub) adati: “Kodi ndingakukhulupirireni pa iye kuposa momwe ndidakukhulupirirani pa m’bale wake kale (yemwe mudamsokeretsa)? Koma Allah ndi Yemwe ali Wabwino posunga, Ndipo Iye Ngwachifundo zedi kuposa achifundo onse.” info
التفاسير:

external-link copy
65 : 12

وَلَمَّا فَتَحُواْ مَتَٰعَهُمۡ وَجَدُواْ بِضَٰعَتَهُمۡ رُدَّتۡ إِلَيۡهِمۡۖ قَالُواْ يَٰٓأَبَانَا مَا نَبۡغِيۖ هَٰذِهِۦ بِضَٰعَتُنَا رُدَّتۡ إِلَيۡنَاۖ وَنَمِيرُ أَهۡلَنَا وَنَحۡفَظُ أَخَانَا وَنَزۡدَادُ كَيۡلَ بَعِيرٖۖ ذَٰلِكَ كَيۡلٞ يَسِيرٞ

Ndipo pamene adatsekula katundu wawo, adapeza chuma chawo chabwezedwa kwa iwo. Adati: “E bambo wathu! Tingafunenso chiyani (kwa munthu waufuluyu)? Ichi chuma chathu chabwezedwa kwa ife; ndipo tikabweretsa chakudya chothandizira mawanja athu; ndipo m’bale wathu tikamsunga; tikapezanso muyeso wangamira imodzi yoonjezera. Umenewu ndi mlingo wochepa (kwa mfumu ya ufuluyo).” info
التفاسير:

external-link copy
66 : 12

قَالَ لَنۡ أُرۡسِلَهُۥ مَعَكُمۡ حَتَّىٰ تُؤۡتُونِ مَوۡثِقٗا مِّنَ ٱللَّهِ لَتَأۡتُنَّنِي بِهِۦٓ إِلَّآ أَن يُحَاطَ بِكُمۡۖ فَلَمَّآ ءَاتَوۡهُ مَوۡثِقَهُمۡ قَالَ ٱللَّهُ عَلَىٰ مَا نَقُولُ وَكِيلٞ

(Ya’qub) adati: “Sindingamtumize pamodzi ndi inu pokhapokha mundipatse lonjezo m’dzina la Allah kuti ndithudi mudzambweza kwa ine pokhapokha nonsenu mutazingidwa (ndi zoopsa).” Ndipo pamene adapereka lonjezo lawo, (iye) adati: “Allah ndiye Muyang’aniri (mboni) pa zimene tikunenazi.” info
التفاسير:

external-link copy
67 : 12

وَقَالَ يَٰبَنِيَّ لَا تَدۡخُلُواْ مِنۢ بَابٖ وَٰحِدٖ وَٱدۡخُلُواْ مِنۡ أَبۡوَٰبٖ مُّتَفَرِّقَةٖۖ وَمَآ أُغۡنِي عَنكُم مِّنَ ٱللَّهِ مِن شَيۡءٍۖ إِنِ ٱلۡحُكۡمُ إِلَّا لِلَّهِۖ عَلَيۡهِ تَوَكَّلۡتُۖ وَعَلَيۡهِ فَلۡيَتَوَكَّلِ ٱلۡمُتَوَكِّلُونَ

Adatinso: “E inu ana anga! Musakalowe (mu Iguputo) pachipata chimodzi koma kaloweni pa zipata zosiyanasiyana. Ndipo sindingakuthandizeni chilichonse kwa Allah. Lamulo ndi la Allah basi; kwa Iye ndiko ndatsamira; ndipo otsamira atsamire kwa Iye.” info
التفاسير:

external-link copy
68 : 12

وَلَمَّا دَخَلُواْ مِنۡ حَيۡثُ أَمَرَهُمۡ أَبُوهُم مَّا كَانَ يُغۡنِي عَنۡهُم مِّنَ ٱللَّهِ مِن شَيۡءٍ إِلَّا حَاجَةٗ فِي نَفۡسِ يَعۡقُوبَ قَضَىٰهَاۚ وَإِنَّهُۥ لَذُو عِلۡمٖ لِّمَا عَلَّمۡنَٰهُ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَ ٱلنَّاسِ لَا يَعۡلَمُونَ

Ndipo pamene adalowa monga momwe bambo wawo adawalamulira, sikudawathandize chilichonse kwa Allah kupatula khumbo lomwe lidali mu mtima mwa Ya’qub (ndilomwe) adalikwaniritsa, (Ya’qub adali kufuna Yûsuf ndi m’bale wake akumane mwamseri; ndipo adakumanadi). Ndithu iye (Ya’qub) adali wanzeru chifukwa chakuti tidamphunzitsa. Koma anthu ambiri sadziwa. info
التفاسير:

external-link copy
69 : 12

وَلَمَّا دَخَلُواْ عَلَىٰ يُوسُفَ ءَاوَىٰٓ إِلَيۡهِ أَخَاهُۖ قَالَ إِنِّيٓ أَنَا۠ أَخُوكَ فَلَا تَبۡتَئِسۡ بِمَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ

Ndipo pamene adalowa kwa Yûsuf (ndikumuona m’bale wake atalowa payekha), adamkumbatira m’bale wakeyo nati: “Ndithu ine ndine m’bale wako; choncho usadandaule pa zimene (abale athu) akhala akuchita.” info
التفاسير: