[233] Apa tanthauzo lake nkuti zilipo zisonyezo zambiri zosonyeza kuti Allah alipo zomwe iwo akuziona ali pamudzi ndiponso akuzidutsa akakhala pa maulendo awo monga thambo, nthaka, dzuwa, mwezi, nyenyezi, mapiri ndi zina zambiri zododometsa zimene zikupezeka kumwamba ndi pansi. Akuziona m’mawa ndi madzulo koma iwo saziganizira.
[234] Apa akutanthauza kuti ambiri a iwo amamphatikiza Allah ndi milungu yabodza. Iwo amavomereza kuti Allah ndiye Mlengi wopatsa zonse. Koma kuonjezera pachikhulupiliro choterechi, amapembedzanso mafano. Ndipo zoterezi masiku ano zikumachitika ndi Asilamu ena amene amafuulira mizimu ya anthu akufa kuti iwathangate pa mavuto amene awagwera, komwe nkumuphatikiza Allah ndi mizimu ya anthu akufa.
[235] Apa Mtumiki (s.a.w) akuuzidwa kuti awauze anthu kuti iye pamodzi ndi amene akumutsata kuti amalalikira Chisilamu kwa anthu popereka kwa anthuwo mitsutso yanzeru, ndikuperekanso zisonyezo ndi maumboni amphamvu. Sibwino Msilamu kutsatira chinthu popanda kuchidziwa bwinobwino. Qur’an ikunenetsa kuti osatsatira chinthu popanda kuchidziwa bwinobwino pokhapokha chinthucho chitanenedwa ndi Allah kapena Mtumiki Wake.