Kilniojo Korano reikšmių vertimas - Vertimas į čevų k. - Khalid Ibrahim Bitala

Al-Ma’ârij

external-link copy
1 : 70

سَأَلَ سَآئِلُۢ بِعَذَابٖ وَاقِعٖ

Wopempha adapempha kuti chiwadzere msanga chilango chopezekacho, (m’kupempha kwa chipongwe ndi kotsutsa). info
التفاسير:

external-link copy
2 : 70

لِّلۡكَٰفِرِينَ لَيۡسَ لَهُۥ دَافِعٞ

Kwa okanira palibe angachitsekereze. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 70

مِّنَ ٱللَّهِ ذِي ٱلۡمَعَارِجِ

Chochokera kwa Allah Mwini makwelero. info
التفاسير:

external-link copy
4 : 70

تَعۡرُجُ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ وَٱلرُّوحُ إِلَيۡهِ فِي يَوۡمٖ كَانَ مِقۡدَارُهُۥ خَمۡسِينَ أَلۡفَ سَنَةٖ

Angelo ndi Jiburil amakwera kwa Iye (Allah) m’tsiku lomwe kutalika kwake kuli ngati zaka zikwi makumi asanu (50 000). info
التفاسير:

external-link copy
5 : 70

فَٱصۡبِرۡ صَبۡرٗا جَمِيلًا

Choncho, pirira (iwe Mtumiki (s.a.w) kupirira kwabwino, info
التفاسير:

external-link copy
6 : 70

إِنَّهُمۡ يَرَوۡنَهُۥ بَعِيدٗا

Ndithu iwo akuliona (tsiku la Qiyâma) kuti lili kutali (silingachitike). info
التفاسير:

external-link copy
7 : 70

وَنَرَىٰهُ قَرِيبٗا

Koma Ife tikuliona kuti lilipafupi (ndilochitika). info
التفاسير:

external-link copy
8 : 70

يَوۡمَ تَكُونُ ٱلسَّمَآءُ كَٱلۡمُهۡلِ

Tsiku limene thambo lidzakhala ngati mtovu wosungunuka. info
التفاسير:

external-link copy
9 : 70

وَتَكُونُ ٱلۡجِبَالُ كَٱلۡعِهۡنِ

Ndipo mapiri adzakhala ngati ubweya (wongouluka wokha). info
التفاسير:

external-link copy
10 : 70

وَلَا يَسۡـَٔلُ حَمِيمٌ حَمِيمٗا

Ndipo m’bale sadzafunsa za m’bale wake. info
التفاسير:

external-link copy
11 : 70

يُبَصَّرُونَهُمۡۚ يَوَدُّ ٱلۡمُجۡرِمُ لَوۡ يَفۡتَدِي مِنۡ عَذَابِ يَوۡمِئِذِۭ بِبَنِيهِ

Ngakhale adzawalole kuti aonane ndi kudziwana pakati pawo (sadzafunsana). Wochimwa adzalakalaka kuti akadaziwombola ku chilango cha tsiku limenelo ndi ana ake. info
التفاسير:

external-link copy
12 : 70

وَصَٰحِبَتِهِۦ وَأَخِيهِ

Ndi mkazi wake, ndi m’bale wake. info
التفاسير:

external-link copy
13 : 70

وَفَصِيلَتِهِ ٱلَّتِي تُـٔۡوِيهِ

Ndi akumtundu wake amene amamsunga. info
التفاسير:

external-link copy
14 : 70

وَمَن فِي ٱلۡأَرۡضِ جَمِيعٗا ثُمَّ يُنجِيهِ

Ndi (kulipira) zonse za m’dziko, kuti zimpulumutse. info
التفاسير:

external-link copy
15 : 70

كَلَّآۖ إِنَّهَا لَظَىٰ

Iyayi, (siya iwe wamachimo zimene ukulakalakazo)! Ndithu umenewu ndi Moto wa malawi. info
التفاسير:

external-link copy
16 : 70

نَزَّاعَةٗ لِّلشَّوَىٰ

Wosupula mwamphamvu khungu. info
التفاسير:

external-link copy
17 : 70

تَدۡعُواْ مَنۡ أَدۡبَرَ وَتَوَلَّىٰ

Udzaitana (potchula dzina la aliyense) amene adachitembenuzira msana choona ndi kunyoza. info
التفاسير:

external-link copy
18 : 70

وَجَمَعَ فَأَوۡعَىٰٓ

Adasonkhanitsa (chuma) ndi kusunga (m’nkhokwe zake popanda kuperekera chopereka cha Allah). info
التفاسير:

external-link copy
19 : 70

۞ إِنَّ ٱلۡإِنسَٰنَ خُلِقَ هَلُوعًا

Ndithu munthu walengedwa kukhala wosapirira. info
التفاسير:

external-link copy
20 : 70

إِذَا مَسَّهُ ٱلشَّرُّ جَزُوعٗا

Mavuto akamkhudza amada nkhawa. info
التفاسير:

external-link copy
21 : 70

وَإِذَا مَسَّهُ ٱلۡخَيۡرُ مَنُوعًا

Koma zabwino zikamkhudza amamana (ena ndi kuiwala mavuto amene adali nawo). info
التفاسير:

external-link copy
22 : 70

إِلَّا ٱلۡمُصَلِّينَ

Kupatula opemphera Swala, (iwo alibe mbiri zoipazi). info
التفاسير:

external-link copy
23 : 70

ٱلَّذِينَ هُمۡ عَلَىٰ صَلَاتِهِمۡ دَآئِمُونَ

Iwo amene sadukiza mapemphero awo a swala; (sakuwaleka ngakhale zivute chotani). info
التفاسير:

external-link copy
24 : 70

وَٱلَّذِينَ فِيٓ أَمۡوَٰلِهِمۡ حَقّٞ مَّعۡلُومٞ

Ndi amene mchuma chawo muli gawo lodziwika (Zakaat), info
التفاسير:

external-link copy
25 : 70

لِّلسَّآئِلِ وَٱلۡمَحۡرُومِ

La wopempha ndi wosapempha. info
التفاسير:

external-link copy
26 : 70

وَٱلَّذِينَ يُصَدِّقُونَ بِيَوۡمِ ٱلدِّينِ

Ndi amene akuvomereza za tsiku la malipiro (ndi kumalikonzekera.) info
التفاسير:

external-link copy
27 : 70

وَٱلَّذِينَ هُم مِّنۡ عَذَابِ رَبِّهِم مُّشۡفِقُونَ

Ndi iwo amene akuopa chilango chochokera kwa Mbuye wawo. info
التفاسير:

external-link copy
28 : 70

إِنَّ عَذَابَ رَبِّهِمۡ غَيۡرُ مَأۡمُونٖ

Ndithu chilango cha Mbuye wawo nchosapulumuka nacho (munthu woipa). info
التفاسير:

external-link copy
29 : 70

وَٱلَّذِينَ هُمۡ لِفُرُوجِهِمۡ حَٰفِظُونَ

Ndiponso iwo amene akusunga umaliseche wawo (posachita chiwerewere), info
التفاسير:

external-link copy
30 : 70

إِلَّا عَلَىٰٓ أَزۡوَٰجِهِمۡ أَوۡ مَا مَلَكَتۡ أَيۡمَٰنُهُمۡ فَإِنَّهُمۡ غَيۡرُ مَلُومِينَ

Kupatula kwa akazi awo ndi amene manja awo akumanja apeza; ndithu pazimenezo iwo sangadzudzulidwe. info
التفاسير:

external-link copy
31 : 70

فَمَنِ ٱبۡتَغَىٰ وَرَآءَ ذَٰلِكَ فَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡعَادُونَ

Koma amene angafune (zina) kusiya zimenezi iwowo ndiwo olumpha malire. info
التفاسير:

external-link copy
32 : 70

وَٱلَّذِينَ هُمۡ لِأَمَٰنَٰتِهِمۡ وَعَهۡدِهِمۡ رَٰعُونَ

Ndi iwo amene amasunga mwaubwino zimene amasungitsidwa ndi zimene alonjeza. info
التفاسير:

external-link copy
33 : 70

وَٱلَّذِينَ هُم بِشَهَٰدَٰتِهِمۡ قَآئِمُونَ

Ndi iwo amene amaima molungama popereka umboni wawo. info
التفاسير:

external-link copy
34 : 70

وَٱلَّذِينَ هُمۡ عَلَىٰ صَلَاتِهِمۡ يُحَافِظُونَ

Ndiponso iwo amene amasunga (mwaubwino) mapemphero awo a swala. info
التفاسير:

external-link copy
35 : 70

أُوْلَٰٓئِكَ فِي جَنَّٰتٖ مُّكۡرَمُونَ

Amene ali ndi mbiri zimenezi adzakhala m’Minda (yamtendere) ali olemekezedwa. info
التفاسير:

external-link copy
36 : 70

فَمَالِ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ قِبَلَكَ مُهۡطِعِينَ

Kodi kuli chiyani kwa amene akana (chikhulupiliro) akuthamangira kwa iwe (maso ali pamtunda)? info
التفاسير:

external-link copy
37 : 70

عَنِ ٱلۡيَمِينِ وَعَنِ ٱلشِّمَالِ عِزِينَ

Atakuzungulira ena chakumanja ena chakumanzere. info
التفاسير:

external-link copy
38 : 70

أَيَطۡمَعُ كُلُّ ٱمۡرِيٕٖ مِّنۡهُمۡ أَن يُدۡخَلَ جَنَّةَ نَعِيمٖ

Kodi akulakalaka aliyense mwa iwo kuti akalowetsedwe ku Munda wamtendere? info
التفاسير:

external-link copy
39 : 70

كَلَّآۖ إِنَّا خَلَقۡنَٰهُم مِّمَّا يَعۡلَمُونَ

Asiye (kukhumba kwawo kokalowa ku Munda wamtendere)! Ndithu Ife tidawalenga kuchokera m’zimene akudziwa (madzi opanda pake). info
التفاسير:

external-link copy
40 : 70

فَلَآ أُقۡسِمُ بِرَبِّ ٱلۡمَشَٰرِقِ وَٱلۡمَغَٰرِبِ إِنَّا لَقَٰدِرُونَ

Ndikulumbilira Mbuye wa kuvuma ndi kuzambwe konse ndithu Ndife Wokhoza. info
التفاسير:

external-link copy
41 : 70

عَلَىٰٓ أَن نُّبَدِّلَ خَيۡرٗا مِّنۡهُمۡ وَمَا نَحۡنُ بِمَسۡبُوقِينَ

Kuwasintha ndi kudzetsa abwino kuposa iwo; Ife palibe (chilichonse) chotipambana. info
التفاسير:

external-link copy
42 : 70

فَذَرۡهُمۡ يَخُوضُواْ وَيَلۡعَبُواْ حَتَّىٰ يُلَٰقُواْ يَوۡمَهُمُ ٱلَّذِي يُوعَدُونَ

Asiye azingolankhula zopanda pake ndi kumangosewera mpaka adzakumane ndi tsiku lawo limene akulonjezedwa. info
التفاسير:

external-link copy
43 : 70

يَوۡمَ يَخۡرُجُونَ مِنَ ٱلۡأَجۡدَاثِ سِرَاعٗا كَأَنَّهُمۡ إِلَىٰ نُصُبٖ يُوفِضُونَ

Tsiku limene adzatuluke m’manda uku akuthamanga (kudza kwa woitana) ngati kuti akuthamangira kumafano awo (amene adali kuwapembedza). info
التفاسير:

external-link copy
44 : 70

خَٰشِعَةً أَبۡصَٰرُهُمۡ تَرۡهَقُهُمۡ ذِلَّةٞۚ ذَٰلِكَ ٱلۡيَوۡمُ ٱلَّذِي كَانُواْ يُوعَدُونَ

Maso awo ali zyoli, (osatha kuwakweza); kuyaluka kutawaphimba! Limenelo ndilo tsiku lomwe adali kulonjezedwa (pomwe adali padziko lapansi. info
التفاسير: