[160] Ndime iyi ikusonyeza kupatukana komwe kuli pakati pawo kotero kuti mpingo wina umayesa unzake monga wakunja. Monga mpingo wa Roman Catholic umaiona mipingo ina monga ya Protestant, Orthodox ndi yambiri ngati mipingo ya chikunja. Zonsezi nchifukwa cha kusatsatira zophunzitsa zenizeni za Chikhrisitu.
[161] Mndime iyi atchula zoyankhula zawo za machimo zoti Isa (Yesu) ndi mwana wa Mulungu, kapena ndi Mulungu amene, kapena ndi mmodzi mmilungu itatu. Ndipo akunenetsa za kufooka kwa mneneri Isa (Yesu) pamaso pa Allah monga kulili kufookanso kwa zolengedwa zina.
Ndimeyi ikunenetsanso kuti Allah monga amalenga mkalengedwe kamene Iye wafuna, mchosadabwitsa kwa Iye kulenga Isa (Yesu) popanda tate. Ndipo nchosadabwitsanso kwa Iye kulenga Adam popanda tate ndi mayi. Nanga nchotani kuti Akhrisitu azimuyesa Mneneri Isa (Yesu) kuti ndi mwana wa Mulungu kamba koti alibe tate? Bwanji nanga Adam naye sakumuyesa mwana wa Mulungu poti nayenso alibe tate ndi mayi? Ndibwino kutsata choonadi ngakhale choonadicho chikuchokera kwa mdani. Choonadi ndi choonadi.