Kilniojo Korano reikšmių vertimas - Vertimas į čevų k. - Khalid Ibrahim Bitala

Puslapio numeris:close

external-link copy
11 : 43

وَٱلَّذِي نَزَّلَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءَۢ بِقَدَرٖ فَأَنشَرۡنَا بِهِۦ بَلۡدَةٗ مَّيۡتٗاۚ كَذَٰلِكَ تُخۡرَجُونَ

Ndiponso amene watsitsa madzi kuchokera kumwamba mwamuyeso; chifukwa cha madziwo tidaukitsa mudzi wakufa. Momwemonso inu mudzatulutsidwa (mmanda); info
التفاسير:

external-link copy
12 : 43

وَٱلَّذِي خَلَقَ ٱلۡأَزۡوَٰجَ كُلَّهَا وَجَعَلَ لَكُم مِّنَ ٱلۡفُلۡكِ وَٱلۡأَنۡعَٰمِ مَا تَرۡكَبُونَ

Ndiponso amene walenga zinthu zonse ziwiriziwiri (chachimuna ndi chachikazi). Ndipo adakupangirani zombo ndi ziweto zimene mukukwera, info
التفاسير:

external-link copy
13 : 43

لِتَسۡتَوُۥاْ عَلَىٰ ظُهُورِهِۦ ثُمَّ تَذۡكُرُواْ نِعۡمَةَ رَبِّكُمۡ إِذَا ٱسۡتَوَيۡتُمۡ عَلَيۡهِ وَتَقُولُواْ سُبۡحَٰنَ ٱلَّذِي سَخَّرَ لَنَا هَٰذَا وَمَا كُنَّا لَهُۥ مُقۡرِنِينَ

Kuti mukhazikike mwaubwino pamisana paizo, kenako mukumbukire mtendere wa Mbuye wanu mukakhazikika pamenepo, ndipo munene: “Walemekezeka Amene watifewetsera ichi; ndipo sitikadatha kuchifewetsa ndi kuchigwiritsa ntchito.” info
التفاسير:

external-link copy
14 : 43

وَإِنَّآ إِلَىٰ رَبِّنَا لَمُنقَلِبُونَ

“Ndipo ndithu ife kwa Mbuye wathu ndiko kobwerera.” info
التفاسير:

external-link copy
15 : 43

وَجَعَلُواْ لَهُۥ مِنۡ عِبَادِهِۦ جُزۡءًاۚ إِنَّ ٱلۡإِنسَٰنَ لَكَفُورٞ مُّبِينٌ

Ndipo amuikira gawo mwa akapolo Ake. (Kuti ndi ana a Allah.) Ndithu munthu, ngwamsulizo woonekera poyera! info
التفاسير:

external-link copy
16 : 43

أَمِ ٱتَّخَذَ مِمَّا يَخۡلُقُ بَنَاتٖ وَأَصۡفَىٰكُم بِٱلۡبَنِينَ

Kodi wadzichitira ana achikazi mzimene wazilenga ndipo wakusankhirani inu ana achimuna? info
التفاسير:

external-link copy
17 : 43

وَإِذَا بُشِّرَ أَحَدُهُم بِمَا ضَرَبَ لِلرَّحۡمَٰنِ مَثَلٗا ظَلَّ وَجۡهُهُۥ مُسۡوَدّٗا وَهُوَ كَظِيمٌ

Koma akauzidwa (kuti wabereka mwana wamkazi) mmodzi wa iwo chomwe amamfanizira (Allah) Wachifundo chambiri, nkhope yake imakhala yakuda ndi kudandaula kwambiri! info
التفاسير:

external-link copy
18 : 43

أَوَمَن يُنَشَّؤُاْ فِي ٱلۡحِلۡيَةِ وَهُوَ فِي ٱلۡخِصَامِ غَيۡرُ مُبِينٖ

Ha! Kodi amene waleredwa monga chokongoletsa, potsutsana iye sangathe kunena momveka? (Ameneyo ndiye mwampatsa Allah; omwe ndi ana aakazi). info
التفاسير:

external-link copy
19 : 43

وَجَعَلُواْ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةَ ٱلَّذِينَ هُمۡ عِبَٰدُ ٱلرَّحۡمَٰنِ إِنَٰثًاۚ أَشَهِدُواْ خَلۡقَهُمۡۚ سَتُكۡتَبُ شَهَٰدَتُهُمۡ وَيُسۡـَٔلُونَ

Ndipo angelo omwe ndi akapolo a (Allah) Wachifundo chambiri akuwatcha akazi. Kodi adaona kalengedwe kawo? Umboni wawo ulembedwa ndipo adzafunsidwa (pazimenezo)! info
التفاسير:

external-link copy
20 : 43

وَقَالُواْ لَوۡ شَآءَ ٱلرَّحۡمَٰنُ مَا عَبَدۡنَٰهُمۗ مَّا لَهُم بِذَٰلِكَ مِنۡ عِلۡمٍۖ إِنۡ هُمۡ إِلَّا يَخۡرُصُونَ

Ndipo (otsutsa) akunena: “Akadafuna (Allah) Wachifundo chambiri (kuti tisamapembedze mafano awa), sitikadawapembedza!” Iwo alibe kudziwa pa zimenezi (zomwe akunenazi). Koma akungonena mawu opeka. info
التفاسير:

external-link copy
21 : 43

أَمۡ ءَاتَيۡنَٰهُمۡ كِتَٰبٗا مِّن قَبۡلِهِۦ فَهُم بِهِۦ مُسۡتَمۡسِكُونَ

Kapena tidawapatsa buku lina tisadapereke ili, kotero kuti iwo agwiritsitsa limenelo (ndi kugwirizana nazo zili mmenemo)? info
التفاسير:

external-link copy
22 : 43

بَلۡ قَالُوٓاْ إِنَّا وَجَدۡنَآ ءَابَآءَنَا عَلَىٰٓ أُمَّةٖ وَإِنَّا عَلَىٰٓ ءَاثَٰرِهِم مُّهۡتَدُونَ

Koma akunena: “Ndithu ife tidawapeza makolo athu pa chipembedzo chimenechi, ndipo ife tikutsatira mapazi awo.” info
التفاسير: