Kilniojo Korano reikšmių vertimas - Vertimas į čevų k. - Khalid Ibrahim Bitala

Puslapio numeris:close

external-link copy
10 : 3

إِنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لَن تُغۡنِيَ عَنۡهُمۡ أَمۡوَٰلُهُمۡ وَلَآ أَوۡلَٰدُهُم مِّنَ ٱللَّهِ شَيۡـٔٗاۖ وَأُوْلَٰٓئِكَ هُمۡ وَقُودُ ٱلنَّارِ

Ndithu amene sadakhulupirire, chuma chawo sichidzawathandiza chilichonse ngakhalenso ana awo, ku chilango cha Allah. Ndipo iwo ndi nkhuni za ku Moto. info
التفاسير:

external-link copy
11 : 3

كَدَأۡبِ ءَالِ فِرۡعَوۡنَ وَٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡۚ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا فَأَخَذَهُمُ ٱللَّهُ بِذُنُوبِهِمۡۗ وَٱللَّهُ شَدِيدُ ٱلۡعِقَابِ

(Khalidwe la awa osakhulupiira, amumbadwo wako iwe mneneri Muhammad {s.a.w}, liri) ngati khalidwe la anthu a Farawo ndi amene adalipo pambuyo pawo. (Iwo) adatsutsa zisonyezo Zathu. Choncho, Allah adawakhaulitsa chifukwa cha machimo awo. Ndipo Allah Ngolanga mwaukali. info
التفاسير:

external-link copy
12 : 3

قُل لِّلَّذِينَ كَفَرُواْ سَتُغۡلَبُونَ وَتُحۡشَرُونَ إِلَىٰ جَهَنَّمَۖ وَبِئۡسَ ٱلۡمِهَادُ

Auze amene sadakhulupirire: “Posachedwapa mugonjetsedwa ndi kusonkhanitsidwa ndi kuponyedwa ku Moto. Taonani kuipa kwa malo wokakhazikikamo!”[62] info

[62] Mawu adalandiridwa kuchokera kwa Saîd bun Jubair omwe iye adawalandiranso kuchokera kwa Ikrima pomwe nayenso Ikrima adawalandira kuchokera kwa Ibn Abbas (Allah asangalale nawo onse). Iye adati: “Ndithudi, Mtumiki (s.a.w) pamene adagonjetsa Aquraishi pa nkhondo ya Badri nabwerera ku Madina, adawasonkhanitsa Ayuda mu msika wa Bani Qainuqaa’ nawachenjeza kuti chingawapeze chomwe chidawapeza Aquraish. Iwo adati: “Usanyengedwe ndizimenezo. Ndithudi, iwe unakumana ndi mbuli za anthu zomwe sizidziwa kamenyedwe ka nkhondo. Ndipo nchifukwa chake wawagonjetsa. Ukadamenyana ndi ife ukadadziwa kuti ife ndife anthu.”
Pachifukwa ichi idavumbulutsidwa Ayah (ndime) yakuti: “Nena (kwa iwo iwe Muhammad {s.a.w}): “Inu Ayuda mugonjetsedwa posachedwapa pompano pa dziko lapansi. Chuma chanu ndi ana anu zisakunyengeni. Kupambana sikuli pa chifukwa cha kuchuluka kwanu, koma kuli m’manja mwa Allah Woyera.”
Mawuwa adatsimikizika powapha a Bani Nadhir ndi kugonjetsa mzinda wa Khaibar.

التفاسير:

external-link copy
13 : 3

قَدۡ كَانَ لَكُمۡ ءَايَةٞ فِي فِئَتَيۡنِ ٱلۡتَقَتَاۖ فِئَةٞ تُقَٰتِلُ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِ وَأُخۡرَىٰ كَافِرَةٞ يَرَوۡنَهُم مِّثۡلَيۡهِمۡ رَأۡيَ ٱلۡعَيۡنِۚ وَٱللَّهُ يُؤَيِّدُ بِنَصۡرِهِۦ مَن يَشَآءُۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَعِبۡرَةٗ لِّأُوْلِي ٱلۡأَبۡصَٰرِ

“Ndithudi, padapezeka chisonyezo chachikulu kwa inu m’magulu awiri omwe adakumana (tsiku la nkhondo ya Badri), pomwe gulu limodzi limamenya (nkhondo) pa njira ya Allah, pamene linalo lokanira, (ndipo gululo) linkawaona (Asilamu) kukhala ochuluka kawiri kuposa ilo, poona ndi maso awo. Ndipo Allah amamlimbikitsira mphamvu ndi chipulumutso chake amene wamfuna. Ndithudi, m’zimenezo muli malingaliro (akulu) kwa eni kupenyetsetsa mwanzeru.” info
التفاسير:

external-link copy
14 : 3

زُيِّنَ لِلنَّاسِ حُبُّ ٱلشَّهَوَٰتِ مِنَ ٱلنِّسَآءِ وَٱلۡبَنِينَ وَٱلۡقَنَٰطِيرِ ٱلۡمُقَنطَرَةِ مِنَ ٱلذَّهَبِ وَٱلۡفِضَّةِ وَٱلۡخَيۡلِ ٱلۡمُسَوَّمَةِ وَٱلۡأَنۡعَٰمِ وَٱلۡحَرۡثِۗ ذَٰلِكَ مَتَٰعُ ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَاۖ وَٱللَّهُ عِندَهُۥ حُسۡنُ ٱلۡمَـَٔابِ

Kwakometsedwa kwa anthu kukonda zilakolako (za moyo wawo) monga akazi, ana, milumilu ya chuma cha golide ndi siliva, ndi mahachi oyang’aniridwa bwino, ziweto ndi mbewu. Izo ndi zosangalatsa za moyo wa dziko lapansi (zomwe sizili kanthu). Koma kwa Allah ndiko kuli mabwelero abwino. info
التفاسير:

external-link copy
15 : 3

۞ قُلۡ أَؤُنَبِّئُكُم بِخَيۡرٖ مِّن ذَٰلِكُمۡۖ لِلَّذِينَ ٱتَّقَوۡاْ عِندَ رَبِّهِمۡ جَنَّٰتٞ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ خَٰلِدِينَ فِيهَا وَأَزۡوَٰجٞ مُّطَهَّرَةٞ وَرِضۡوَٰنٞ مِّنَ ٱللَّهِۗ وَٱللَّهُ بَصِيرُۢ بِٱلۡعِبَادِ

Nena: “Kodi ndikuuzeni zomwe zili zabwino kuposa zimenezo? Kwa omwe ali olungama, akapeza kwa Mbuye wawo Minda yomwe pansi pake (ndi patsogolo pake) mitsinje ikuyenda; adzakhala mmenemo nthawi yaitali ndikulandira akazi oyeretsedwa ndi chiyanjo chochokera kwa Allah. Ndipo Allah akuona akapolo ake onse. info
التفاسير: