Kilniojo Korano reikšmių vertimas - Vertimas į čevų k. - Khalid Ibrahim Bitala

Puslapio numeris:close

external-link copy
46 : 11

قَالَ يَٰنُوحُ إِنَّهُۥ لَيۡسَ مِنۡ أَهۡلِكَۖ إِنَّهُۥ عَمَلٌ غَيۡرُ صَٰلِحٖۖ فَلَا تَسۡـَٔلۡنِ مَا لَيۡسَ لَكَ بِهِۦ عِلۡمٌۖ إِنِّيٓ أَعِظُكَ أَن تَكُونَ مِنَ ٱلۡجَٰهِلِينَ

(Allah) adati: “E iwe Nuh! Ndithu iyeyo si (mwana) wa m’banja lako. Iye zochita zake sizili zabwino. Choncho usandipemphe zomwe siukuzidziwa, Ine ndikukulangiza kuti usakhale m’gulu la osazindikira (mbuli).” info
التفاسير:

external-link copy
47 : 11

قَالَ رَبِّ إِنِّيٓ أَعُوذُ بِكَ أَنۡ أَسۡـَٔلَكَ مَا لَيۡسَ لِي بِهِۦ عِلۡمٞۖ وَإِلَّا تَغۡفِرۡ لِي وَتَرۡحَمۡنِيٓ أَكُن مِّنَ ٱلۡخَٰسِرِينَ

(Nuh) adati: “E Mbuye wanga! Ndikudziteteza mwa Inu kuti ndisakupempheninso zomwe sindikuzidziwa. Ngati simundikhululukira ndi kundichitira chifundo, ndikhala mwa anthu otaika.” info
التفاسير:

external-link copy
48 : 11

قِيلَ يَٰنُوحُ ٱهۡبِطۡ بِسَلَٰمٖ مِّنَّا وَبَرَكَٰتٍ عَلَيۡكَ وَعَلَىٰٓ أُمَمٖ مِّمَّن مَّعَكَۚ وَأُمَمٞ سَنُمَتِّعُهُمۡ ثُمَّ يَمَسُّهُم مِّنَّا عَذَابٌ أَلِيمٞ

Kudanenedwa: “E iwe Nuh! Tsika (pa nthaka youma) mwamtendere wochokera kwa Ife, ndipo madalitso ambiri akhale pa iwe ndi pa anthu omwe ali nawe; ndipo kudzakhala mibadwo ina (yoipa pambuyo pako) yomwe tidzaisangalatsa, ndipo kenako chidzaikhudza chilango chowawa chochokera kwa Ife.” info
التفاسير:

external-link copy
49 : 11

تِلۡكَ مِنۡ أَنۢبَآءِ ٱلۡغَيۡبِ نُوحِيهَآ إِلَيۡكَۖ مَا كُنتَ تَعۡلَمُهَآ أَنتَ وَلَا قَوۡمُكَ مِن قَبۡلِ هَٰذَاۖ فَٱصۡبِرۡۖ إِنَّ ٱلۡعَٰقِبَةَ لِلۡمُتَّقِينَ

Izi ndi zina mwa nkhani zobisika zomwe tikukuululira iwe. Siudali kuzidziwa, iwe ngakhale anthu ako, patsogolo pa ichi, (Qur’an isadadze). Choncho, pirira. Ndithu mathero abwino adzakhala kwa anthu oopa Allah. info
التفاسير:

external-link copy
50 : 11

وَإِلَىٰ عَادٍ أَخَاهُمۡ هُودٗاۚ قَالَ يَٰقَوۡمِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ مَا لَكُم مِّنۡ إِلَٰهٍ غَيۡرُهُۥٓۖ إِنۡ أَنتُمۡ إِلَّا مُفۡتَرُونَ

Ndipo anthu (amtundu) wa Âdi, tidawatumizira m’bale wawo Hûd. Adati: “E inu anthu anga! Pembedzani Allah! (Siyani kupembedza mafano). Mulibe mulungu wina koma Iye. Inu simuli kanthu koma ndinu opeka bodza (m’kunena kwanu kwakuti mafano ndi anzake a Allah).” info
التفاسير:

external-link copy
51 : 11

يَٰقَوۡمِ لَآ أَسۡـَٔلُكُمۡ عَلَيۡهِ أَجۡرًاۖ إِنۡ أَجۡرِيَ إِلَّا عَلَى ٱلَّذِي فَطَرَنِيٓۚ أَفَلَا تَعۡقِلُونَ

“E inu anthu anga! Sindikukupemphani malipiro pa ichi (uthengawu). Palibe Malipiro anga koma ali kwaYemwe adandilenga. Kodi mulibe nzeru?” info
التفاسير:

external-link copy
52 : 11

وَيَٰقَوۡمِ ٱسۡتَغۡفِرُواْ رَبَّكُمۡ ثُمَّ تُوبُوٓاْ إِلَيۡهِ يُرۡسِلِ ٱلسَّمَآءَ عَلَيۡكُم مِّدۡرَارٗا وَيَزِدۡكُمۡ قُوَّةً إِلَىٰ قُوَّتِكُمۡ وَلَا تَتَوَلَّوۡاْ مُجۡرِمِينَ

“Ndipo E inu anthu anga! Pemphani chikhululuko kwa Mbuye wanu, (pa machimo omwe mwakhala mukuchita), kenako lapani kwa Iye. Akutumizirani mitambo yodzetsa mvula yambiri, ndipo akuonjezerani mphamvu pa mphamvu zanu (zomwe muli nazo). Choncho, musatembenuke kukhala oipa.” info
التفاسير:

external-link copy
53 : 11

قَالُواْ يَٰهُودُ مَا جِئۡتَنَا بِبَيِّنَةٖ وَمَا نَحۡنُ بِتَارِكِيٓ ءَالِهَتِنَا عَن قَوۡلِكَ وَمَا نَحۡنُ لَكَ بِمُؤۡمِنِينَ

(Iwo) adati: “E iwe Hûd! Sudatibweretsere chisonyezo chooneka (chosonyeza kuti ndiwe Mneneri), ndipo ife sitisiya (kupembedza) milungu yathu chifukwa cha zoyankhula zakozo. Ndipo ife sitikukhulupirira.” info
التفاسير: