وه‌رگێڕانی ماناكانی قورئانی پیرۆز - وەرگێڕاوی شیشوا - خالد ئیبراهيم بيتالا

ژمارەی پەڕە: 147:128 close

external-link copy
147 : 6

فَإِن كَذَّبُوكَ فَقُل رَّبُّكُمۡ ذُو رَحۡمَةٖ وَٰسِعَةٖ وَلَا يُرَدُّ بَأۡسُهُۥ عَنِ ٱلۡقَوۡمِ ٱلۡمُجۡرِمِينَ

Ngati akukutsutsa (pa zimene zavumbulutsidwa), auze (mowachenjeza): “Mbuye wanu (Yemwe ngofunika kum’khulupirira ndi kutsatira malamulo ake) Ngwachifundo chambiri (kwa yemwe akumumvera, ndi yemwe akumunyoza pano pa dziko lapansi). Komatu chilango chake sichibwezedwa kwa anthu oipa.” info
التفاسير:

external-link copy
148 : 6

سَيَقُولُ ٱلَّذِينَ أَشۡرَكُواْ لَوۡ شَآءَ ٱللَّهُ مَآ أَشۡرَكۡنَا وَلَآ ءَابَآؤُنَا وَلَا حَرَّمۡنَا مِن شَيۡءٖۚ كَذَٰلِكَ كَذَّبَ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡ حَتَّىٰ ذَاقُواْ بَأۡسَنَاۗ قُلۡ هَلۡ عِندَكُم مِّنۡ عِلۡمٖ فَتُخۡرِجُوهُ لَنَآۖ إِن تَتَّبِعُونَ إِلَّا ٱلظَّنَّ وَإِنۡ أَنتُمۡ إِلَّا تَخۡرُصُونَ

Amene akuphatikiza (Allah ndi mafano) anena: “Ngati Allah akadafuna, sitikadam’phatikiza, ife ngakhale makolo athu. Ndipo sitikadaletsa chilichonse. (Choncho, izi zomwe tikuchita, Allah akuziyanja). Momwemonso adatsutsa omwe adalipo patsogolo pawo kufikira adalawa chilango chathu. Nena: “Kodi muli nako kudziwa (kokutsimikizirani zimenezi), koti mungatitulutsire (umboni wake wotsimikizira kuti Allah adakulamulani zimenezi)? Inu simutsatira china, koma zongoganizira basi. Ndipo Simukunena china koma zabodza basi.” info
التفاسير:

external-link copy
149 : 6

قُلۡ فَلِلَّهِ ٱلۡحُجَّةُ ٱلۡبَٰلِغَةُۖ فَلَوۡ شَآءَ لَهَدَىٰكُمۡ أَجۡمَعِينَ

Nena: “Allah ndi Yemwe ali ndi umboni wokwanira. Choncho akadafuna, akadakuongolani nonsenu.” info
التفاسير:

external-link copy
150 : 6

قُلۡ هَلُمَّ شُهَدَآءَكُمُ ٱلَّذِينَ يَشۡهَدُونَ أَنَّ ٱللَّهَ حَرَّمَ هَٰذَاۖ فَإِن شَهِدُواْ فَلَا تَشۡهَدۡ مَعَهُمۡۚ وَلَا تَتَّبِعۡ أَهۡوَآءَ ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا وَٱلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ بِٱلۡأٓخِرَةِ وَهُم بِرَبِّهِمۡ يَعۡدِلُونَ

Nena: “Tabweretsani mboni zanuzo zomwe zingapereke umboni kuti Allah adaletsa izi.” Choncho ngati zitapereka umboni, (mboni zawozo) usaikire nawo umboni pamodzi ndi iwo. Ndipo usatsate zofuna za omwe atsutsa zizindikiro zathu ndi amene sakhulupirira tsiku lachimaliziro; omwenso akufanizira Mbuye wawo ndi milungu yabodza. info
التفاسير:

external-link copy
151 : 6

۞ قُلۡ تَعَالَوۡاْ أَتۡلُ مَا حَرَّمَ رَبُّكُمۡ عَلَيۡكُمۡۖ أَلَّا تُشۡرِكُواْ بِهِۦ شَيۡـٔٗاۖ وَبِٱلۡوَٰلِدَيۡنِ إِحۡسَٰنٗاۖ وَلَا تَقۡتُلُوٓاْ أَوۡلَٰدَكُم مِّنۡ إِمۡلَٰقٖ نَّحۡنُ نَرۡزُقُكُمۡ وَإِيَّاهُمۡۖ وَلَا تَقۡرَبُواْ ٱلۡفَوَٰحِشَ مَا ظَهَرَ مِنۡهَا وَمَا بَطَنَۖ وَلَا تَقۡتُلُواْ ٱلنَّفۡسَ ٱلَّتِي حَرَّمَ ٱللَّهُ إِلَّا بِٱلۡحَقِّۚ ذَٰلِكُمۡ وَصَّىٰكُم بِهِۦ لَعَلَّكُمۡ تَعۡقِلُونَ

Nena: “Idzani kuno, ndikuwerengereni zomwe Mbuye wanu wakuletsani. Musamphatikize ndi chilichonse, ndipo achitireni zabwino makolo anu; musaphe ana anu chifukwa chakuopa umphawi; ife tikupatsani rizq inu pamodzi ndi iwo; musayandikire zoyipa, zoonekera ndi zobisika; ndipo musaphe munthu yemwe Allah adaletsa (kumupha) kupatula ikapezeka njira yoyenereza (kumupha). Akukulangizani izi kuti muziike mu nzeru zanu.” info
التفاسير: