وه‌رگێڕانی ماناكانی قورئانی پیرۆز - وەرگێڕاوی شیشوا - خالد ئیبراهيم بيتالا

ژمارەی پەڕە:close

external-link copy
73 : 22

يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ ضُرِبَ مَثَلٞ فَٱسۡتَمِعُواْ لَهُۥٓۚ إِنَّ ٱلَّذِينَ تَدۡعُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ لَن يَخۡلُقُواْ ذُبَابٗا وَلَوِ ٱجۡتَمَعُواْ لَهُۥۖ وَإِن يَسۡلُبۡهُمُ ٱلذُّبَابُ شَيۡـٔٗا لَّا يَسۡتَنقِذُوهُ مِنۡهُۚ ضَعُفَ ٱلطَّالِبُ وَٱلۡمَطۡلُوبُ

E inu anthu! Fanizo laperekedwa; choncho limvereni. Ndithu amene mukuwapembedza m’malo mwa Allah, sangathe kulenga ntchentche ngakhale Atasonkhana (kuti athandizane) pachimenechi. Ndipo ngati ntchenche itawalanda chinthu, sangathe kuchilanda kuntchentcheyo. Wafooka kwenikweni wopempha ndi wopemphedwa. info
التفاسير:

external-link copy
74 : 22

مَا قَدَرُواْ ٱللَّهَ حَقَّ قَدۡرِهِۦٓۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَقَوِيٌّ عَزِيزٌ

Sadamlemekeze Allah, kulemekeza komuyenera. Ndithu Allah Ngwamphamvu Ngogonjetsa chilichonse. info
التفاسير:

external-link copy
75 : 22

ٱللَّهُ يَصۡطَفِي مِنَ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةِ رُسُلٗا وَمِنَ ٱلنَّاسِۚ إِنَّ ٱللَّهَ سَمِيعُۢ بَصِيرٞ

Allah amasankha atumiki mwa angelo ndi mwa anthu. Ndithu Allah Ngwakumva; Ngopenya. info
التفاسير:

external-link copy
76 : 22

يَعۡلَمُ مَا بَيۡنَ أَيۡدِيهِمۡ وَمَا خَلۡفَهُمۡۚ وَإِلَى ٱللَّهِ تُرۡجَعُ ٱلۡأُمُورُ

Akudziwa zimene zili patsogolo pawo ndi zimene zili pambuyo pawo; kwa Allah Yekha ndiko kobwerera zinthu. info
التفاسير:

external-link copy
77 : 22

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ ٱرۡكَعُواْ وَٱسۡجُدُواْۤ وَٱعۡبُدُواْ رَبَّكُمۡ وَٱفۡعَلُواْ ٱلۡخَيۡرَ لَعَلَّكُمۡ تُفۡلِحُونَ۩

E inu amene mwakhulupirira! Weramani ndikugwetsa nkhope zanu pansi ndipo mpembedzeni Mbuye wanu ndikuchita zabwino kuti mupambane. info
التفاسير:

external-link copy
78 : 22

وَجَٰهِدُواْ فِي ٱللَّهِ حَقَّ جِهَادِهِۦۚ هُوَ ٱجۡتَبَىٰكُمۡ وَمَا جَعَلَ عَلَيۡكُمۡ فِي ٱلدِّينِ مِنۡ حَرَجٖۚ مِّلَّةَ أَبِيكُمۡ إِبۡرَٰهِيمَۚ هُوَ سَمَّىٰكُمُ ٱلۡمُسۡلِمِينَ مِن قَبۡلُ وَفِي هَٰذَا لِيَكُونَ ٱلرَّسُولُ شَهِيدًا عَلَيۡكُمۡ وَتَكُونُواْ شُهَدَآءَ عَلَى ٱلنَّاسِۚ فَأَقِيمُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَءَاتُواْ ٱلزَّكَوٰةَ وَٱعۡتَصِمُواْ بِٱللَّهِ هُوَ مَوۡلَىٰكُمۡۖ فَنِعۡمَ ٱلۡمَوۡلَىٰ وَنِعۡمَ ٱلنَّصِيرُ

Ndipo menyerani chipembedzo cha Allah, kumenyera kwa choonadi; Iye ndi Amene adakusankhani (kuti mukhale mpingo wabwino;) ndipo sadaike pa inu zinthu zolemera pa chipembedzo, ndi chipembedzo cha tate wanu Ibrahim. Iye (Allah) adakutchani Asilamu kuyambira kale (m’mabuku akale) ndi mu iyi, (Qur’an) kuti Mtumiki akhale mboni pa inu, inunso kuti mukhale mboni pa anthu. Choncho pempherani Swala moyenera, perekani Zakaat ndipo gwirizanani chifukwa cha Allah. Iye ndiye Mbuye wanu, Mbuye wabwino zedi, ndi Mthandizi wabwino zedi. info
التفاسير: