وه‌رگێڕانی ماناكانی قورئانی پیرۆز - وەرگێڕاوی شیشوا - خالد ئیبراهيم بيتالا

ژمارەی پەڕە:close

external-link copy
6 : 2

إِنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ سَوَآءٌ عَلَيۡهِمۡ ءَأَنذَرۡتَهُمۡ أَمۡ لَمۡ تُنذِرۡهُمۡ لَا يُؤۡمِنُونَ

Ndithu amene sadakhulupirire, nchimodzimodzi kwa iwo uwachenjeze kapena usawachenjeze sangakhulupirire. info
التفاسير:

external-link copy
7 : 2

خَتَمَ ٱللَّهُ عَلَىٰ قُلُوبِهِمۡ وَعَلَىٰ سَمۡعِهِمۡۖ وَعَلَىٰٓ أَبۡصَٰرِهِمۡ غِشَٰوَةٞۖ وَلَهُمۡ عَذَابٌ عَظِيمٞ

(Ali ngati kuti) Allah wawadinda chidindo chotseka mitima yawo ndi makutu awo (kotero kuti kuunika kwa chikhulupiliro sikungalowemo), ndipo m’maso mwawo muli chophimba (sangathe kuona zozizwitsa za Allah); choncho iwo adzalandira chilango chachikulu. info
التفاسير:

external-link copy
8 : 2

وَمِنَ ٱلنَّاسِ مَن يَقُولُ ءَامَنَّا بِٱللَّهِ وَبِٱلۡيَوۡمِ ٱلۡأٓخِرِ وَمَا هُم بِمُؤۡمِنِينَ

Pakati pa anthu alipo (anthu achinyengo) amene akunena: “Takhulupirira mwa Allah ndi tsiku lachimaliziro,” pomwe iwo sali okhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
9 : 2

يُخَٰدِعُونَ ٱللَّهَ وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَمَا يَخۡدَعُونَ إِلَّآ أَنفُسَهُمۡ وَمَا يَشۡعُرُونَ

Akufuna kunyenga Allah ndi amene akhulupirira, ndipo sanyenga aliyense koma okha, ndipo iwo sazindikira (kuti akudzinyenga okha). info
التفاسير:

external-link copy
10 : 2

فِي قُلُوبِهِم مَّرَضٞ فَزَادَهُمُ ٱللَّهُ مَرَضٗاۖ وَلَهُمۡ عَذَابٌ أَلِيمُۢ بِمَا كَانُواْ يَكۡذِبُونَ

M’mitima mwawo muli matenda; ndipo Allah wawaonjezera matenda. Choncho iwo adzalandira chilango chopweteka chifukwa cha bodza lawo. info
التفاسير:

external-link copy
11 : 2

وَإِذَا قِيلَ لَهُمۡ لَا تُفۡسِدُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ قَالُوٓاْ إِنَّمَا نَحۡنُ مُصۡلِحُونَ

Ndipo akauzidwa kuti: “Musaononge padziko,” amayankha kuti: “Ife ndife okonza.” info
التفاسير:

external-link copy
12 : 2

أَلَآ إِنَّهُمۡ هُمُ ٱلۡمُفۡسِدُونَ وَلَٰكِن لَّا يَشۡعُرُونَ

Dziwani kuti, ndithudi, iwo ndiwo ali oononga (pa dziko); koma sakuzindikira. info
التفاسير:

external-link copy
13 : 2

وَإِذَا قِيلَ لَهُمۡ ءَامِنُواْ كَمَآ ءَامَنَ ٱلنَّاسُ قَالُوٓاْ أَنُؤۡمِنُ كَمَآ ءَامَنَ ٱلسُّفَهَآءُۗ أَلَآ إِنَّهُمۡ هُمُ ٱلسُّفَهَآءُ وَلَٰكِن لَّا يَعۡلَمُونَ

Ndipo akauzidwa kuti, “Khulupirirani monga momwe anthu ena akhulupirira,” amayankha kuti: “Kodi tikhulupirire monga momwe zakhulupirira zitsiru?” Dziwani kuti, ndithudi, iwo ndi omwe ali zitsiru, koma sakudziwa. info
التفاسير:

external-link copy
14 : 2

وَإِذَا لَقُواْ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ قَالُوٓاْ ءَامَنَّا وَإِذَا خَلَوۡاْ إِلَىٰ شَيَٰطِينِهِمۡ قَالُوٓاْ إِنَّا مَعَكُمۡ إِنَّمَا نَحۡنُ مُسۡتَهۡزِءُونَ

Ndipo akakumana ndi amene akhulupirira, amanena: “Takhulupirira.” Koma akakhala pa okha ndi asatana awo, amati: “Ndithudi ife tili pamodzi nanu. Timangowachita chipongwe basi.” info
التفاسير:

external-link copy
15 : 2

ٱللَّهُ يَسۡتَهۡزِئُ بِهِمۡ وَيَمُدُّهُمۡ فِي طُغۡيَٰنِهِمۡ يَعۡمَهُونَ

Allah adzawalipira chipongwe chawocho, ndipo akuwalekelera akungoyumbayumba (kugwira njakata) m’kusokera kwawo. info
التفاسير:

external-link copy
16 : 2

أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ ٱشۡتَرَوُاْ ٱلضَّلَٰلَةَ بِٱلۡهُدَىٰ فَمَا رَبِحَت تِّجَٰرَتُهُمۡ وَمَا كَانُواْ مُهۡتَدِينَ

Oterewo ndiomwe asinthanitsa chiongoko ndi kusokera, koma malonda awo sadawapindulire chilichonse, tero sadali oongoka. info
التفاسير: