وه‌رگێڕانی ماناكانی قورئانی پیرۆز - وەرگێڕاوی شیشوا - خالد ئیبراهيم بيتالا

ژمارەی پەڕە:close

external-link copy
105 : 17

وَبِٱلۡحَقِّ أَنزَلۡنَٰهُ وَبِٱلۡحَقِّ نَزَلَۗ وَمَآ أَرۡسَلۡنَٰكَ إِلَّا مُبَشِّرٗا وَنَذِيرٗا

Ndipo chifukwa chobweretsa choonadi pa dziko tidaitumiza (Qur’an); ndipo mwachoonadi, yavumbulutsidwa. Ndipo sitidakutume (ndi china) koma kuti ukhale wouza (okhulupirira) nkhani zabwino, ndi wochenjeza (osakhulupirira). info
التفاسير:

external-link copy
106 : 17

وَقُرۡءَانٗا فَرَقۡنَٰهُ لِتَقۡرَأَهُۥ عَلَى ٱلنَّاسِ عَلَىٰ مُكۡثٖ وَنَزَّلۡنَٰهُ تَنزِيلٗا

Ndipo Qur’an iyi taigawa (m’zigawo zosiyanasiyana poivumbulutsa pang’onopang’ono) kuti uwawerengere anthu mwa chifatse ndipo taivumbulutsa pang’onopang’ono. info
التفاسير:

external-link copy
107 : 17

قُلۡ ءَامِنُواْ بِهِۦٓ أَوۡ لَا تُؤۡمِنُوٓاْۚ إِنَّ ٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡعِلۡمَ مِن قَبۡلِهِۦٓ إِذَا يُتۡلَىٰ عَلَيۡهِمۡ يَخِرُّونَۤ لِلۡأَذۡقَانِۤ سُجَّدٗاۤ

Nena (kwa osakhulupirira a m’Makka mowachenjeza): “Ikhulupirireni (iyi Qur’an) kapena musaikhulupirire, (zonse zili m’chifuniro chanu.) Ndithu amene adapatsidwa nzeru kale (yozindikira za m’mabuku a Allah Qur’an isanadze) ikamalakatulidwa kwa iwo (Qur’aniyi) amagwa ndi zibwano zawo molambira. info
التفاسير:

external-link copy
108 : 17

وَيَقُولُونَ سُبۡحَٰنَ رَبِّنَآ إِن كَانَ وَعۡدُ رَبِّنَا لَمَفۡعُولٗا

Ndipo amanena: “Mbuye wathu Ngoyera! Ndithu lonjezo la Mbuye wathu ndi lokwaniritsidwa!” info
التفاسير:

external-link copy
109 : 17

وَيَخِرُّونَ لِلۡأَذۡقَانِ يَبۡكُونَ وَيَزِيدُهُمۡ خُشُوعٗا۩

Ndipo amagwa ndi zibwano zawo uku akulira, ndipo (Qur’an) imawaonjezera kudzichepetsa. info
التفاسير:

external-link copy
110 : 17

قُلِ ٱدۡعُواْ ٱللَّهَ أَوِ ٱدۡعُواْ ٱلرَّحۡمَٰنَۖ أَيّٗا مَّا تَدۡعُواْ فَلَهُ ٱلۡأَسۡمَآءُ ٱلۡحُسۡنَىٰۚ وَلَا تَجۡهَرۡ بِصَلَاتِكَ وَلَا تُخَافِتۡ بِهَا وَٱبۡتَغِ بَيۡنَ ذَٰلِكَ سَبِيلٗا

Nena (kwa Amushirikina): “Mpempheni Allah, m’dzina la Allah kapena mpempheni m’dzina la Rahman; (dzina) lililonse, limene mungamtchulire (zithandizabe); Iye ali nawo maina abwino. Ndipo usawerenge (Qur’an) pa Swala yako ndi mawu okweza, ndiponso usatsitse mawu kwambiri, koma tsata njira yolingana pakati pa zimenezo (pokweza kwambiri kapena kutsitsa zedi).” info
التفاسير:

external-link copy
111 : 17

وَقُلِ ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ ٱلَّذِي لَمۡ يَتَّخِذۡ وَلَدٗا وَلَمۡ يَكُن لَّهُۥ شَرِيكٞ فِي ٱلۡمُلۡكِ وَلَمۡ يَكُن لَّهُۥ وَلِيّٞ مِّنَ ٱلذُّلِّۖ وَكَبِّرۡهُ تَكۡبِيرَۢا

Ndipo nena: “Kutamandidwa kwabwino nkwa Allah, yemwe saadadzipangire mwana, ndipo alibe m’phatikizi mu ufumu (Wake); ndipo alibe mthandizi (womthandiza) mkufooka; ndipo mkuzeni, kumkuza kwakukulu!” info
التفاسير: