وه‌رگێڕانی ماناكانی قورئانی پیرۆز - وەرگێڕاوی شیشوا - خالد ئیبراهيم بيتالا

ژمارەی پەڕە:close

external-link copy
23 : 12

وَرَٰوَدَتۡهُ ٱلَّتِي هُوَ فِي بَيۡتِهَا عَن نَّفۡسِهِۦ وَغَلَّقَتِ ٱلۡأَبۡوَٰبَ وَقَالَتۡ هَيۡتَ لَكَۚ قَالَ مَعَاذَ ٱللَّهِۖ إِنَّهُۥ رَبِّيٓ أَحۡسَنَ مَثۡوَايَۖ إِنَّهُۥ لَا يُفۡلِحُ ٱلظَّٰلِمُونَ

Ndipo mkazi uja yemwe m’nyumba mwake mudali iye adamlakalaka (Yûsuf) popanda iye kufuna. Ndipo (mkaziyo) adatseka zitseko nati: “Bwera kuno.” (Yûsuf) adati: “Ndikudzitchinjiriza ndi Allah (kuchita tchimolo). Ndithu iye (mwamuna wako) ndi bwana wanga. Wandikonzera bwino pokhala panga (m’nyumba mwakemu, ndipo sindichita chinyengo chotere). Ndithu achinyengo siziwayendera bwino.” info
التفاسير:

external-link copy
24 : 12

وَلَقَدۡ هَمَّتۡ بِهِۦۖ وَهَمَّ بِهَا لَوۡلَآ أَن رَّءَا بُرۡهَٰنَ رَبِّهِۦۚ كَذَٰلِكَ لِنَصۡرِفَ عَنۡهُ ٱلسُّوٓءَ وَٱلۡفَحۡشَآءَۚ إِنَّهُۥ مِنۡ عِبَادِنَا ٱلۡمُخۡلَصِينَ

Ndipo (mkaziyo) adaikira mtima pa iye (kuti achite naye kanthu), ndipo naye (Yûsuf) adaikira mtima pa iye (kuti ammenye). Pakadapanda kuona chisonyezo cha Mbuye wake (chakumzindikiritsa kuti asatero, akadammenya. Koma adamthawa). Tidachita izi kuti timchotsere chinthu choipa ndi chauve; ndithudi, iye adali mwa akapolo athu oyeretsedwa.[231] info

[231] Musamchitire choipa amene wakuchitirani chabwino, ngakhalenso amene wakuchitrani choipa kumene. Makamaka amene sadakuchitireni choipa (ndiye chisimu). Koma alipo anthu ena oipitsitsa zedi amene amachitira zoipa yemwe akuwachitira zabwino. Anthu otero ngoipitsitsa kuposa nyama zamtchire, ndipo oterewa Allah adzawakhaulitsa koopsa. Ndipo machitidwe okhala mwamuna ndi mkazi kuseri kwaokha ngoletsedwa m’shariya ya Chisilamu chifukwa mwamuna kukhala ndi mkazi amene sali mnyazi wake kumalakwitsa. Musati awa ndi alamu ndikhoza kukhala nawo pawokha. Kukhala ndi mlamu wako kuseri, ndi ngozi imeneyo!

التفاسير:

external-link copy
25 : 12

وَٱسۡتَبَقَا ٱلۡبَابَ وَقَدَّتۡ قَمِيصَهُۥ مِن دُبُرٖ وَأَلۡفَيَا سَيِّدَهَا لَدَا ٱلۡبَابِۚ قَالَتۡ مَا جَزَآءُ مَنۡ أَرَادَ بِأَهۡلِكَ سُوٓءًا إِلَّآ أَن يُسۡجَنَ أَوۡ عَذَابٌ أَلِيمٞ

Ndipo (onse awiri) adathamangitsana kukhomo (uku Yûsuf akuthawa) ndipo (mkaziyo) adang’amba mkanjo wake chakumbuyo. Ndipo awiriwa adampeza bwana wake (wa mkaziyo yemwe ndimwamuna wake) pakhomo; mkaziyo adati (kwa mwamuna wake mwaugogodi): “Palibe mphoto kwa yemwe akufuna kuchita choipa ndi mkazi wako koma kumponya kundende, kapena kupatsidwa chilango chowawa.” info
التفاسير:

external-link copy
26 : 12

قَالَ هِيَ رَٰوَدَتۡنِي عَن نَّفۡسِيۚ وَشَهِدَ شَاهِدٞ مِّنۡ أَهۡلِهَآ إِن كَانَ قَمِيصُهُۥ قُدَّ مِن قُبُلٖ فَصَدَقَتۡ وَهُوَ مِنَ ٱلۡكَٰذِبِينَ

(Yûsuf) adati (podziteteza): “(Mkazi) uyu ndi yemwe wandifuna popanda ine kumufuna.” Ndipo mboni yochokera ku banja la mkaziyo idaikira umboni; (idati): “Ngati mkanjo wake wang’ambidwa cha kutsogolo, ndiye kuti (mkazi uyu) akunena zoona, ndipo iye (Yûsuf) ndi mmodzi mwa onena zabodza.” info
التفاسير:

external-link copy
27 : 12

وَإِن كَانَ قَمِيصُهُۥ قُدَّ مِن دُبُرٖ فَكَذَبَتۡ وَهُوَ مِنَ ٱلصَّٰدِقِينَ

“Koma ngati mkanjo wake wang’ambidwa chakumbuyo ndiye kuti (mkazi uyu) wanena bodza ndipo iye (Yûsuf) ndi mmodzi mwa onena zoona.” info
التفاسير:

external-link copy
28 : 12

فَلَمَّا رَءَا قَمِيصَهُۥ قُدَّ مِن دُبُرٖ قَالَ إِنَّهُۥ مِن كَيۡدِكُنَّۖ إِنَّ كَيۡدَكُنَّ عَظِيمٞ

Choncho (mwamuna uja) pamene adaona mkanjo wake (wa Yûsuf) utang’ambidwa chakumbuyo, (adadziwa kuti Yûsuf ndi amene amafuna kugwiliridwa), adati: “Ndithudi, izi ndi ndale zanu akazi. Ndithu ndale zanu ndi zazikulu (iwe mkazi wanga ndi amene udatsimikiza kuchita choipa ndi mnyamatayu).” info
التفاسير:

external-link copy
29 : 12

يُوسُفُ أَعۡرِضۡ عَنۡ هَٰذَاۚ وَٱسۡتَغۡفِرِي لِذَنۢبِكِۖ إِنَّكِ كُنتِ مِنَ ٱلۡخَاطِـِٔينَ

“Yûsuf! Zisiye izi (usauze aliyense). Ndipo (iwe mkazi) pempha chikhululuko ku tchimo lako. Ndithu iwe ndiwe mmodzi mwa olakwa!” info
التفاسير:

external-link copy
30 : 12

۞ وَقَالَ نِسۡوَةٞ فِي ٱلۡمَدِينَةِ ٱمۡرَأَتُ ٱلۡعَزِيزِ تُرَٰوِدُ فَتَىٰهَا عَن نَّفۡسِهِۦۖ قَدۡ شَغَفَهَا حُبًّاۖ إِنَّا لَنَرَىٰهَا فِي ضَلَٰلٖ مُّبِينٖ

Ndipo akazi a mu mzindamo (ataimva nkhaniyi) anati: “Mkazi wa nduna akulakalaka m’nyamata wake popanda kulakalakidwa ndi iye; ndithu chikondi chamufooketsa zedi; ndithudi, ife tikumuona (mkaziyu kuti) ali m’kusokera koonekera.” info
التفاسير: