[452] M’masiku oyamba pa chiyambi cha Usilamu, padapita masiku angapo Mtumiki (s.a.w) osamutsikira chivumbulutso. Iye poona izi adali kukaika ndi kudandaula kwakukulu, nao okanira a pa Makka adali kumchita chipongwe. Adali kumunena kuti: “Kodi Mbuye wako wakusiya kapena wakukwiira?’’ Basi apa Allah akumutonthoza Mneneri Wake, pamodzi ndi kuwayankha okanira aja kuti: “Sadamusiye ndipo sadakwiye naye.”
[453] Zopatsidwa zomwe adalonjezedwa apa ndi Allah, ndi zapadziko mpaka kumwamba (Akhera). Padziko lapansi adampatsa chilichonse chimene adali kuchilakalaka monga kuwaongola anthu ake, kuchilemekeza chipembedzo chake ndi kuwagonjetsa adani ake. Zonsezi Allah adamchitira mnyengo yochepa modabwitsa.
[454] Mneneri Muhammad (s.a.w) asanapatsidwe uneneri wake ndi Allah anali kudandaula kwambiri poona anthu ake ali osokera ndiponso poona kuti iye sadali kudziwa momwe angawaongolere. Pambuyo pake adali kumapita ku mapiri amene adali pafupi ndi mzinda wa Makka. Kumeneko adali kupemphera ndi kumalingalira ndi kupempha Allah kuti amusonyeze njira yachiongoko.