Terjemahan makna Alquran Alkarim - Terjemahan Berbahasa Chichewa - Khalid Ibrahim Betala

Ad-Duhâ

external-link copy
1 : 93

وَٱلضُّحَىٰ

Ndikulumbilira mmawa dzuwa litakwera (imene ili nthawi yantchito), info
التفاسير:

external-link copy
2 : 93

وَٱلَّيۡلِ إِذَا سَجَىٰ

Ndi usiku pamene ukuvindikira. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 93

مَا وَدَّعَكَ رَبُّكَ وَمَا قَلَىٰ

Sadakusiye Mbuye wako (iwe Mneneri) (s.a.w) ndiponso sadakude.[452] info

[452] M’masiku oyamba pa chiyambi cha Usilamu, padapita masiku angapo Mtumiki (s.a.w) osamutsikira chivumbulutso. Iye poona izi adali kukaika ndi kudandaula kwakukulu, nao okanira a pa Makka adali kumchita chipongwe. Adali kumunena kuti: “Kodi Mbuye wako wakusiya kapena wakukwiira?’’ Basi apa Allah akumutonthoza Mneneri Wake, pamodzi ndi kuwayankha okanira aja kuti: “Sadamusiye ndipo sadakwiye naye.”

التفاسير:

external-link copy
4 : 93

وَلَلۡأٓخِرَةُ خَيۡرٞ لَّكَ مِنَ ٱلۡأُولَىٰ

Ndithu moyo watsiku lirimkudza ndi wabwino kwa iwe kuposa umoyo woyambawu. info
التفاسير:

external-link copy
5 : 93

وَلَسَوۡفَ يُعۡطِيكَ رَبُّكَ فَتَرۡضَىٰٓ

Ndithu posachedwapa akupatsa Mbuye wako (zabwino zamdziko lapansi ndi tsiku lachimaliziro) ndipo ukondwera.[453] info

[453] Zopatsidwa zomwe adalonjezedwa apa ndi Allah, ndi zapadziko mpaka kumwamba (Akhera). Padziko lapansi adampatsa chilichonse chimene adali kuchilakalaka monga kuwaongola anthu ake, kuchilemekeza chipembedzo chake ndi kuwagonjetsa adani ake. Zonsezi Allah adamchitira mnyengo yochepa modabwitsa.

التفاسير:

external-link copy
6 : 93

أَلَمۡ يَجِدۡكَ يَتِيمٗا فَـَٔاوَىٰ

Kodi sadakupeze uli wa masiye ndipo adakupatsa pokhala pabwino? info
التفاسير:

external-link copy
7 : 93

وَوَجَدَكَ ضَآلّٗا فَهَدَىٰ

Ndipo adakupeza uli wosazindikira (Qur’an) nakuongola (pokuzindikiritsa Qur’aniyo ndi malamulo a chipembedzo)?[454] info

[454] Mneneri Muhammad (s.a.w) asanapatsidwe uneneri wake ndi Allah anali kudandaula kwambiri poona anthu ake ali osokera ndiponso poona kuti iye sadali kudziwa momwe angawaongolere. Pambuyo pake adali kumapita ku mapiri amene adali pafupi ndi mzinda wa Makka. Kumeneko adali kupemphera ndi kumalingalira ndi kupempha Allah kuti amusonyeze njira yachiongoko.

التفاسير:

external-link copy
8 : 93

وَوَجَدَكَ عَآئِلٗا فَأَغۡنَىٰ

Ndiponso adakupeza uli wosauka nakulemeretsa? info
التفاسير:

external-link copy
9 : 93

فَأَمَّا ٱلۡيَتِيمَ فَلَا تَقۡهَرۡ

Basi, wamasiye usamchitire nkhanza. info
التفاسير:

external-link copy
10 : 93

وَأَمَّا ٱلسَّآئِلَ فَلَا تَنۡهَرۡ

Ndiponso wopempha usamukalipire. info
التفاسير:

external-link copy
11 : 93

وَأَمَّا بِنِعۡمَةِ رَبِّكَ فَحَدِّثۡ

Tsono mtendere wa Mbuye wako uwutchule (pothokoza ndi kugwira ntchito zabwino). info
التفاسير: