[271] Allah wapamwamba wayamba Sura iyi ndi malembo awa awiri potchalenja omwe akutsutsa zoti Qur’an idachokera kwa Allah, kuti atalemba yawo Qur’an yomwe malembo ake omwewa omwe iwo akuwadziwa bwino ndipo amawayankhula.
Koma alephera kutalitali kulemba buku ndi nzeru zawo monga ili. Ndipo kulephera kwawo kulemba buku longa ili, ndiumboni kuti bukuli lidachokera kwa Allah.
[272] M’ndime iyi Allah akuuza munthu kuti Iye akudziwa zonse zimene munthu amayankhula mokweza mawu ndi zimene munthu amayankhula ndi anzake mobisa, ngakhalenso zomwe mtima wake umamnong’oneza.
[273] Ibun Abbas adati: “Izi zidali choncho Musa pamene adakwaniritsa chipangano cha nthawi imene adapangana ndi m’neneri Shuaibu chakuti amuwetere mbuzi kwa zaka 8 kapena 10, adachoka ulendo kubwerera kwawo ku Iguputo pamodzi ndi banja lake; ndipo adasokera njira. Udali usiku wamdima wozizira. Adayesa kupekesa moto kuti awothe koma adalephera. Ndipo ali choncho, adangoona moto chapatali kumbali yakumanja kwa njira. Pamene adauona adauganizira kuti ndi moto weniweni, pomwe udali moto woyera wakuunika kwa Allah. Udali kuyaka mu mtengo wamasamba obiriwira. Ndipo adangomva Mbuye wake akumuitana: “E iwe Musa! Ine ndine Mbuye wako. Ndikukuyankhula; vula nsapato zako.”