クルアーンの対訳 - チェワ語対訳 - Khalid Ibrahim

Al-’Alaq

external-link copy
1 : 96

ٱقۡرَأۡ بِٱسۡمِ رَبِّكَ ٱلَّذِي خَلَقَ

Werenga! (Iwe Mneneri (s.a.w), zomwe zikuvumbulutsidwa) mdzina la Mbuye wako Yemwe adalenga (zolengedwa zonse).[460] info

[460] Tanena kale mndemanga 7 yamu surat - Dhuha kuti Mneneri Muhammad (s.a.w) asadapatsidwe uneneri wake ndi Allah adali kudandaula kwambiri poona anthu ake ali osokera ndiponso poona kuti iye sadali kudziwa momwe angawaongolere. Pambuyo pake adali kumapita ku mapiri amene adali pafupi ndi Mzinda wa Makka. Kumeneko adali kupemphera ndi kumalingalira ndi kupempha Allah kuti amusonyeze njira ya chiongoko. Choncho tsiku lina pamene adali ku phanga la Hiraa, pafupi ndi Makka ali mkati mopemphera, Mngelo adamuonekera mwadzidzidzi nati: “Iwe Muhammad! Ine ndine Jiburil (Gabrie!) ndipo iwe ndiwe Mtumiki wa Allah kwa zolengedwa zonse!” Pambuyo pake adamuuza kuti: “werenga!” Mneneri adayankha: “Ine sindidziwa kuwerenga.” Jiburil uja adamgwira ndi kumpana mwamphamvu mpaka adavutika kwambiri. Adamsiyanso ndi kumuuza: “werenga!” Mneneri adayankha monga adamuyankhira poyamba mpaka kadakwana katatu akumuchita zokhazokhazo. Kenaka adamuwerengera ma Ayah kuchokera 1 mpaka 5. Ma Ayah amenewa ndiwo oyamba kuvumbulutsidwa m’Qur’an.

التفاسير:

external-link copy
2 : 96

خَلَقَ ٱلۡإِنسَٰنَ مِنۡ عَلَقٍ

Adalenga munthu kuchokera ku magazi owundana.[461] info

[461] Madzi ambewu ya munthu, pambuyo pokhazikika mchiberekero kwa masiku makumi anayi, amatembenuka ndikukhala magazi. Ili ndilo tanthauzo la Ayah imeneyi.

التفاسير:

external-link copy
3 : 96

ٱقۡرَأۡ وَرَبُّكَ ٱلۡأَكۡرَمُ

Werenga! Ndipo Mbuye wako ndi Wopereka kwambiri.[462] info

[462] Ayah 3 ndi 5 Mtumiki (s.a.w) akuyankhidwa pa kunena kwake kwa kuti: “Ine sindidziwa kuwerenga.” Choncho Allah akumuuza kuti Iye ndi Mfulu weniweni, ndi Yemwe adawaphunzitsa anthu kulemba ndi cholembera ndi zonse zomwe sadali kuzidziwa. Kwa ufulu Wake wochuluka ndi mphamvu Zake pa chilichonse, sichovuta kwa Iye (Allah) kumphunzitsa Mtumiki Wake kuwerenga molakatula.

التفاسير:

external-link copy
4 : 96

ٱلَّذِي عَلَّمَ بِٱلۡقَلَمِ

Yemwe waphunzitsa (munthu kulemba) ndi cholembera. info
التفاسير:

external-link copy
5 : 96

عَلَّمَ ٱلۡإِنسَٰنَ مَا لَمۡ يَعۡلَمۡ

Waphunzitsa munthu zinthu (zambiri) zomwe (iye) sadali kuzidziwa. info
التفاسير:

external-link copy
6 : 96

كَلَّآ إِنَّ ٱلۡإِنسَٰنَ لَيَطۡغَىٰٓ

Zoona ndithu koma munthu akupyola malire (podzikweza). info
التفاسير:

external-link copy
7 : 96

أَن رَّءَاهُ ٱسۡتَغۡنَىٰٓ

Chifukwa chodziona kuti walemera. info
التفاسير:

external-link copy
8 : 96

إِنَّ إِلَىٰ رَبِّكَ ٱلرُّجۡعَىٰٓ

Palibe chikaiko, (iwe Mneneri (s.a.w) kobwerera (onse) nkwa Mbuye wako basi; (adzawaukitsa).[463] info

[463] Tanthauzo lake nkuti musanyengedwe ndi chumacho chifukwa chakuti, popanda chikaiko, mubwerera kwa Mbuye wanu ndipo chumacho sichidzakuthandizani chilichonse pa maso Pake.

التفاسير:

external-link copy
9 : 96

أَرَءَيۡتَ ٱلَّذِي يَنۡهَىٰ

Kodi wamuona yemwe akuletsa, info
التفاسير:

external-link copy
10 : 96

عَبۡدًا إِذَا صَلَّىٰٓ

Kapolo (wa Allah) akamapemphera? info
التفاسير:

external-link copy
11 : 96

أَرَءَيۡتَ إِن كَانَ عَلَى ٱلۡهُدَىٰٓ

Tandiuza ngati ali pachiongoko? info
التفاسير:

external-link copy
12 : 96

أَوۡ أَمَرَ بِٱلتَّقۡوَىٰٓ

Kapena kuti akulamulira zoopa Allah? info
التفاسير:

external-link copy
13 : 96

أَرَءَيۡتَ إِن كَذَّبَ وَتَوَلَّىٰٓ

Tandiuza (za woletsayo) ngati akutsutsa (zimene wadza nazo Mneneri) ndikunyoza (chikhulupiliro ndi ntchito yabwino)? info
التفاسير:

external-link copy
14 : 96

أَلَمۡ يَعۡلَم بِأَنَّ ٱللَّهَ يَرَىٰ

Kodi sakudziwa kuti Allah akuona (machitidwe ake. Ndipo adzamlipira)? info
التفاسير:

external-link copy
15 : 96

كَلَّا لَئِن لَّمۡ يَنتَهِ لَنَسۡفَعَۢا بِٱلنَّاصِيَةِ

Ayi ndithu ngati sasiya timukoka tsitsi lapatsumba (tiligwira mwamphamvu tsumba lake ndikukamponya ku Moto). info
التفاسير:

external-link copy
16 : 96

نَاصِيَةٖ كَٰذِبَةٍ خَاطِئَةٖ

Tsumba labodza (ndiponso) lamachimo. info
التفاسير:

external-link copy
17 : 96

فَلۡيَدۡعُ نَادِيَهُۥ

Basi aliitane gulu lakelo, (la amene amakhala nawo pabwalo kuti amthandize pano pa dziko kapena tsiku lachimaliziro), info
التفاسير:

external-link copy
18 : 96

سَنَدۡعُ ٱلزَّبَانِيَةَ

Nafe tiitana azabaniya (angelo a ku Moto). info
التفاسير:

external-link copy
19 : 96

كَلَّا لَا تُطِعۡهُ وَٱسۡجُدۡۤ وَٱقۡتَرِب۩

Ayi ndithu usamumvere (pa zimene akukuletsazo); koma gwetsa nkhope yako pansi, ndipo dziyandikitse kwa Mbuye wako. info
التفاسير: