クルアーンの対訳 - チェワ語対訳 - Khalid Ibrahim

Al-Qalam

external-link copy
1 : 68

نٓۚ وَٱلۡقَلَمِ وَمَا يَسۡطُرُونَ

Nûn. Ndikulumbilira cholembera (chimene akulembera angelo), ndi zimene amalemba. info
التفاسير:

external-link copy
2 : 68

مَآ أَنتَ بِنِعۡمَةِ رَبِّكَ بِمَجۡنُونٖ

Pa chisomo cha Mbuye wako iwe sindiwe wamisala (pokupatsa uneneri). info
التفاسير:

external-link copy
3 : 68

وَإِنَّ لَكَ لَأَجۡرًا غَيۡرَ مَمۡنُونٖ

Ndipo ndithu udzakhala ndi malipiro akulu osaduka, (onkerankera mtsogolo chifukwa cha mavuto amene ukukumana nawo pofikitsa uthenga). info
التفاسير:

external-link copy
4 : 68

وَإِنَّكَ لَعَلَىٰ خُلُقٍ عَظِيمٖ

Ndipo ndithu uli nawo makhalidwe abwino kwambiri (omwe Allah adakulenga nawo). info
التفاسير:

external-link copy
5 : 68

فَسَتُبۡصِرُ وَيُبۡصِرُونَ

Basi, posachedwapa uona, iwonso aona. info
التفاسير:

external-link copy
6 : 68

بِأَييِّكُمُ ٱلۡمَفۡتُونُ

Kuti ndani mwa inu wamisala (iwe kapena iwo)? info
التفاسير:

external-link copy
7 : 68

إِنَّ رَبَّكَ هُوَ أَعۡلَمُ بِمَن ضَلَّ عَن سَبِيلِهِۦ وَهُوَ أَعۡلَمُ بِٱلۡمُهۡتَدِينَ

Ndithu Mbuye wako akum’dziwa bwino amene wasokera panjira yake. Ndiponso akuwadziwa bwino amene ali oongoka. info
التفاسير:

external-link copy
8 : 68

فَلَا تُطِعِ ٱلۡمُكَذِّبِينَ

Choncho, usawamvere otsutsa; (usasiye zimene uli nazo ngakhale sakugwirizana nazo). info
التفاسير:

external-link copy
9 : 68

وَدُّواْ لَوۡ تُدۡهِنُ فَيُدۡهِنُونَ

Akufuna kuti ukadakhala wofewa kwa iwo (pa zinthu zina) nawo akadakhala ofewa (kwa iwe). info
التفاسير:

external-link copy
10 : 68

وَلَا تُطِعۡ كُلَّ حَلَّافٖ مَّهِينٍ

Ndipo usamumvere aliyense wochulukitsa kulumbira, woyaluka. info
التفاسير:

external-link copy
11 : 68

هَمَّازٖ مَّشَّآءِۭ بِنَمِيمٖ

Wojeda, woyenda ndi ukazitape (ndi cholinga choononga umodzi wawo). info
التفاسير:

external-link copy
12 : 68

مَّنَّاعٖ لِّلۡخَيۡرِ مُعۡتَدٍ أَثِيمٍ

Wotsekereza zabwino, wamtopola, wamachimo ambiri. info
التفاسير:

external-link copy
13 : 68

عُتُلِّۭ بَعۡدَ ذَٰلِكَ زَنِيمٍ

Wouma mtima; pamwamba pa izi ndi wodzipachika mu mtundu wa ena (pomwe iye sali m’menemo). info
التفاسير:

external-link copy
14 : 68

أَن كَانَ ذَا مَالٖ وَبَنِينَ

Chifukwa choti iye ndi mwini chuma ndi ana (ndi zimene ali kunyadira). info
التفاسير:

external-link copy
15 : 68

إِذَا تُتۡلَىٰ عَلَيۡهِ ءَايَٰتُنَا قَالَ أَسَٰطِيرُ ٱلۡأَوَّلِينَ

Zikawerengedwa kwa iye Ayah Zathu amanena: “Izi ndi nthano za akale (ndi zabodza zawo, zopeka).” info
التفاسير:

external-link copy
16 : 68

سَنَسِمُهُۥ عَلَى ٱلۡخُرۡطُومِ

Timuika pamphuno pake chizindikiro (chosasiyana nacho kuti ayaluke nacho pamaso pa anthu). info
التفاسير:

external-link copy
17 : 68

إِنَّا بَلَوۡنَٰهُمۡ كَمَا بَلَوۡنَآ أَصۡحَٰبَ ٱلۡجَنَّةِ إِذۡ أَقۡسَمُواْ لَيَصۡرِمُنَّهَا مُصۡبِحِينَ

Ndithu ife tidawayesa (eni mzinda wa Makka ndi mtendere omwe udali pa iwo, koma adakana monga) momwe tidawayesera eni munda, pamene adalumbira kuti akathyola (zipatso za m’munda wawozo) mbandakucha (kuti osauka asawaone angawapemphe). info
التفاسير:

external-link copy
18 : 68

وَلَا يَسۡتَثۡنُونَ

Ndipo sadapatule (ngakhale wosauka ndi m’modzi yemwe ponena kuti uje timpatse, uje tisampatse, kapena sadanene kuti: “Ngati Allah afuna).” info
التفاسير:

external-link copy
19 : 68

فَطَافَ عَلَيۡهَا طَآئِفٞ مِّن رَّبِّكَ وَهُمۡ نَآئِمُونَ

Mliri woopsa wochokera kwa Mbuye wako udauzinga (mundawo nthawi yausiku) iwo ali mtulo. info
التفاسير:

external-link copy
20 : 68

فَأَصۡبَحَتۡ كَٱلصَّرِيمِ

Choncho udakhala ngati wokololedwa (chifukwa cha mliri uja). info
التفاسير:

external-link copy
21 : 68

فَتَنَادَوۡاْ مُصۡبِحِينَ

Tero adaitanizana nthawi ya mbandakucha. info
التفاسير:

external-link copy
22 : 68

أَنِ ٱغۡدُواْ عَلَىٰ حَرۡثِكُمۡ إِن كُنتُمۡ صَٰرِمِينَ

“Lawilirani kumunda wanu kuja ngati mukufuna kukolola (kuopera kuti angakuoneni osauka).” info
التفاسير:

external-link copy
23 : 68

فَٱنطَلَقُواْ وَهُمۡ يَتَخَٰفَتُونَ

Adanyamuka uku akunong’ onezana. info
التفاسير:

external-link copy
24 : 68

أَن لَّا يَدۡخُلَنَّهَا ٱلۡيَوۡمَ عَلَيۡكُم مِّسۡكِينٞ

(Akunena kuti): “Asakulowelereni wosauka lero mmenemo.” info
التفاسير:

external-link copy
25 : 68

وَغَدَوۡاْ عَلَىٰ حَرۡدٖ قَٰدِرِينَ

Ndipo adalawilira ali ndi chitsimikizo choti atha kuwamana (osauka). info
التفاسير:

external-link copy
26 : 68

فَلَمَّا رَأَوۡهَا قَالُوٓاْ إِنَّا لَضَآلُّونَ

Choncho pamene adauona, adanena (uku akunjenjemera): “Ndithu ife tasokera (sikuno ayi, munda wathu uja siuno).” info
التفاسير:

external-link copy
27 : 68

بَلۡ نَحۡنُ مَحۡرُومُونَ

“Iyayi, ndiwomwewu; koma tamanidwa zinthu zake.” info
التفاسير:

external-link copy
28 : 68

قَالَ أَوۡسَطُهُمۡ أَلَمۡ أَقُل لَّكُمۡ لَوۡلَا تُسَبِّحُونَ

Wolungama mwa iwo adanena: “Kodi sindinakuuzeni (pamene mudali kulangizana zomana osowa) kuti bwanji osamkumbukira Allah (ndi kusintha cholinga chanu)?” info
التفاسير:

external-link copy
29 : 68

قَالُواْ سُبۡحَٰنَ رَبِّنَآ إِنَّا كُنَّا ظَٰلِمِينَ

(Iwo) adanena: “Alemekezeke Mbuye wathu ndithu ife tidali achinyengo (chifukwa cha kuipa kwa cholinga chathu).” info
التفاسير:

external-link copy
30 : 68

فَأَقۡبَلَ بَعۡضُهُمۡ عَلَىٰ بَعۡضٖ يَتَلَٰوَمُونَ

Ndipo adatembenukirana ndikuyamba kudzudzulana. info
التفاسير:

external-link copy
31 : 68

قَالُواْ يَٰوَيۡلَنَآ إِنَّا كُنَّا طَٰغِينَ

Adati: “E chionongeko chathu! Ndithu Ife tidapyola malire (m’chinyengo chathu).” info
التفاسير:

external-link copy
32 : 68

عَسَىٰ رَبُّنَآ أَن يُبۡدِلَنَا خَيۡرٗا مِّنۡهَآ إِنَّآ إِلَىٰ رَبِّنَا رَٰغِبُونَ

“Mwina Mbuye wathu angatipatse zabwino m’malo mwa munda wathuwu. Ndithu ife tikufunitsitsa kwa Mbuye wathu (chikhululuko Chake).” info
التفاسير:

external-link copy
33 : 68

كَذَٰلِكَ ٱلۡعَذَابُۖ وَلَعَذَابُ ٱلۡأٓخِرَةِ أَكۡبَرُۚ لَوۡ كَانُواْ يَعۡلَمُونَ

Umo ndi mmene chimakhalira chilango (Changa chomwe ndimachitsitsa pa dziko lapansi kwa amene chamuyenera); koma chilango cha tsiku lachimaliziro nchachikulu zedi, akadakhala akudziwa. info
التفاسير:

external-link copy
34 : 68

إِنَّ لِلۡمُتَّقِينَ عِندَ رَبِّهِمۡ جَنَّٰتِ ٱلنَّعِيمِ

Ndithu oopa Allah adzakhala ndi Minda ya mtendere kwa Mbuye wawo. info
التفاسير:

external-link copy
35 : 68

أَفَنَجۡعَلُ ٱلۡمُسۡلِمِينَ كَٱلۡمُجۡرِمِينَ

Kodi tiwachite Asilamu monga ochimwa. info
التفاسير:

external-link copy
36 : 68

مَا لَكُمۡ كَيۡفَ تَحۡكُمُونَ

Kodi nchiyani chakupezani! Nanga mukuweruza bwanji (maweruzo opanda chilungamo)? info
التفاسير:

external-link copy
37 : 68

أَمۡ لَكُمۡ كِتَٰبٞ فِيهِ تَدۡرُسُونَ

Kapena muli ndi buku limene mukuwerenga. info
التفاسير:

external-link copy
38 : 68

إِنَّ لَكُمۡ فِيهِ لَمَا تَخَيَّرُونَ

Kuti ndithu mulinazo mmenemo zomwe mukudzisankhira. info
التفاسير:

external-link copy
39 : 68

أَمۡ لَكُمۡ أَيۡمَٰنٌ عَلَيۡنَا بَٰلِغَةٌ إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِ إِنَّ لَكُمۡ لَمَا تَحۡكُمُونَ

Kapena muli nawo mapangano ndi Ife okafika mpaka tsiku lachimaliziro akuti inu mudzapeza zimene mukudziweruzira? info
التفاسير:

external-link copy
40 : 68

سَلۡهُمۡ أَيُّهُم بِذَٰلِكَ زَعِيمٌ

Afunse (iwe Mtumiki) ndani mwa iwo amene ali mtsogoleri (pa malamulo amenewa)? info
التفاسير:

external-link copy
41 : 68

أَمۡ لَهُمۡ شُرَكَآءُ فَلۡيَأۡتُواْ بِشُرَكَآئِهِمۡ إِن كَانُواْ صَٰدِقِينَ

Kapena iwo ali nawo othandidzana nawo (pa mau awa)? Chomwecho atabweretsa othandizana nawo ngati akunena zowona! info
التفاسير:

external-link copy
42 : 68

يَوۡمَ يُكۡشَفُ عَن سَاقٖ وَيُدۡعَوۡنَ إِلَى ٱلسُّجُودِ فَلَا يَسۡتَطِيعُونَ

(Akumbukire) tsiku la mavuto okhwima, ndipo adzaitanidwa (akafiri) kuti achite sijida (polambira Allah) koma sadzatha. info
التفاسير:

external-link copy
43 : 68

خَٰشِعَةً أَبۡصَٰرُهُمۡ تَرۡهَقُهُمۡ ذِلَّةٞۖ وَقَدۡ كَانُواْ يُدۡعَوۡنَ إِلَى ٱلسُّجُودِ وَهُمۡ سَٰلِمُونَ

Maso awo adzangoti pansi zyoli, manyazi ndi kunyozeka kudzawaphimba; chikhalirecho adali kuitanidwa (pa dziko lapansi) kuti agwetse nkhope pansi pomwe iwo adali ndi moyo wa ngwiro (koma ankakana). info
التفاسير:

external-link copy
44 : 68

فَذَرۡنِي وَمَن يُكَذِّبُ بِهَٰذَا ٱلۡحَدِيثِۖ سَنَسۡتَدۡرِجُهُم مِّنۡ حَيۡثُ لَا يَعۡلَمُونَ

Choncho ndisiye, (iwe Mtumiki), ndi amene akukanira nkhani iyi tiwakokera kuchilango pang’onopang’ono pamene iwo sakudziwa (mmene chiti chiwadzere chilangochi). info
التفاسير:

external-link copy
45 : 68

وَأُمۡلِي لَهُمۡۚ إِنَّ كَيۡدِي مَتِينٌ

Ndipo ndikuwalekelera (pochedwetsa chilango); ndithudi makonzedwe Anga ngokhwima, (palibe angapulumuke mmenemo). info
التفاسير:

external-link copy
46 : 68

أَمۡ تَسۡـَٔلُهُمۡ أَجۡرٗا فَهُم مِّن مَّغۡرَمٖ مُّثۡقَلُونَ

Kapena ukuwapempha malipiro (pofikitsa uthenga) kotero kuti iwo akulemedwa ndi kulipira? info
التفاسير:

external-link copy
47 : 68

أَمۡ عِندَهُمُ ٱلۡغَيۡبُ فَهُمۡ يَكۡتُبُونَ

Kapena ali nazo (nzeru) zobisika kotero kuti iwo akulemba (zimene akuweruzazo)! info
التفاسير:

external-link copy
48 : 68

فَٱصۡبِرۡ لِحُكۡمِ رَبِّكَ وَلَا تَكُن كَصَاحِبِ ٱلۡحُوتِ إِذۡ نَادَىٰ وَهُوَ مَكۡظُومٞ

Choncho pirira ndi lamulo la Mbuye wako (chifukwa chowalekelera ndi kuchedwetsa chipulumutso chako); ndipo usakhale ngati mwini nsomba (Yunusu pa changu ndi mkwiyo kwa anthu ake) pamene adaitana (Mbuye wake) uku ali wodzazidwa ndi mkwiyo (kupempha kuti chidze mwachangu chilango kwa anthu ake). info
التفاسير:

external-link copy
49 : 68

لَّوۡلَآ أَن تَدَٰرَكَهُۥ نِعۡمَةٞ مِّن رَّبِّهِۦ لَنُبِذَ بِٱلۡعَرَآءِ وَهُوَ مَذۡمُومٞ

Chikadapanda kumfikira chisomo chochokera kwa Mbuye wake (ndi kuvomera kulapa kwake), akadaponyedwa (kuchokera m’mimba mwa chinsomba chija) pagombe (popanda kanthu) ali wodzudzulidwa. info
التفاسير:

external-link copy
50 : 68

فَٱجۡتَبَٰهُ رَبُّهُۥ فَجَعَلَهُۥ مِنَ ٱلصَّٰلِحِينَ

Koma adamsankha Mbuye wake (povomera kulapa kwake) ndipo adamchita kukhala mmodzi wa anthu abwino. info
التفاسير:

external-link copy
51 : 68

وَإِن يَكَادُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لَيُزۡلِقُونَكَ بِأَبۡصَٰرِهِمۡ لَمَّا سَمِعُواْ ٱلذِّكۡرَ وَيَقُولُونَ إِنَّهُۥ لَمَجۡنُونٞ

Ndithudi anthu amene sadakhulupirire adayandikira kukuteleretsa ndi kunyogodola kwa maso awo (chifukwa chachidani ndi mkwiyo) pamene adamva chikumbutso (Qur’an), ndipo akunena kuti iyeyo ngwamisala. info
التفاسير:

external-link copy
52 : 68

وَمَا هُوَ إِلَّا ذِكۡرٞ لِّلۡعَٰلَمِينَ

Ndipo ichi sichina, koma (ndi phunziro, ndi nzeru) ndi chikumbutso kwa zolengedwa zonse. info
التفاسير: