クルアーンの対訳 - チェワ語対訳 - Khalid Ibrahim

Ar-Rahmân

external-link copy
1 : 55

ٱلرَّحۡمَٰنُ

(Allah) Wachifundo chochuluka! info
التفاسير:

external-link copy
2 : 55

عَلَّمَ ٱلۡقُرۡءَانَ

Waphunzitsa Qur’an. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 55

خَلَقَ ٱلۡإِنسَٰنَ

Adalenga munthu. info
التفاسير:

external-link copy
4 : 55

عَلَّمَهُ ٱلۡبَيَانَ

Adamphunzitsa kuyankhula. info
التفاسير:

external-link copy
5 : 55

ٱلشَّمۡسُ وَٱلۡقَمَرُ بِحُسۡبَانٖ

Dzuwa ndi mwezi zikuyenda mwachiwerengero. info
التفاسير:

external-link copy
6 : 55

وَٱلنَّجۡمُ وَٱلشَّجَرُ يَسۡجُدَانِ

Zomera zopanda tsinde ndi mitengo, zikulambira (Allah pachilichonse chimene wafuna mwa izo). info
التفاسير:

external-link copy
7 : 55

وَٱلسَّمَآءَ رَفَعَهَا وَوَضَعَ ٱلۡمِيزَانَ

Ndipo thambo adalitukula kumwamba ndipo adakhazikitsa sikelo (ya chilungamo). info
التفاسير:

external-link copy
8 : 55

أَلَّا تَطۡغَوۡاْ فِي ٱلۡمِيزَانِ

Kuti musapyole malire ndi kuchita chinyengo poyesa. info
التفاسير:

external-link copy
9 : 55

وَأَقِيمُواْ ٱلۡوَزۡنَ بِٱلۡقِسۡطِ وَلَا تُخۡسِرُواْ ٱلۡمِيزَانَ

Choncho yesani sikelo mwachilungamo ndipo musapungule muyeso. info
التفاسير:

external-link copy
10 : 55

وَٱلۡأَرۡضَ وَضَعَهَا لِلۡأَنَامِ

Ndipo nthaka adaiyala (ndi kuikonza) kuti ikhale ya zolengedwa. info
التفاسير:

external-link copy
11 : 55

فِيهَا فَٰكِهَةٞ وَٱلنَّخۡلُ ذَاتُ ٱلۡأَكۡمَامِ

M’menemo muli zipatso ndi mitengo ya kanjedza yokhala ndi mapava (a zipatso). info
التفاسير:

external-link copy
12 : 55

وَٱلۡحَبُّ ذُو ٱلۡعَصۡفِ وَٱلرَّيۡحَانُ

Ndi mbewu zamakoko (kuti chikhale chakudya cha inu ndi ziweto zanu), ndipo mulinso m’menemo mmera wafungo labwino. info
التفاسير:

external-link copy
13 : 55

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?) info
التفاسير:

external-link copy
14 : 55

خَلَقَ ٱلۡإِنسَٰنَ مِن صَلۡصَٰلٖ كَٱلۡفَخَّارِ

Adalenga munthu kuchokera ku dongo lolira monga ziwiya zadongo. info
التفاسير:

external-link copy
15 : 55

وَخَلَقَ ٱلۡجَآنَّ مِن مَّارِجٖ مِّن نَّارٖ

Ndipo adalenga ziwanda kuchokera ku malawi a moto (wopanda utsi.) info
التفاسير:

external-link copy
16 : 55

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?) info
التفاسير:

external-link copy
17 : 55

رَبُّ ٱلۡمَشۡرِقَيۡنِ وَرَبُّ ٱلۡمَغۡرِبَيۡنِ

Mbuye wa kuvuma kuwiri ndiponso Mbuye wa kuzambwe kuwiri. info
التفاسير:

external-link copy
18 : 55

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?) info
التفاسير:

external-link copy
19 : 55

مَرَجَ ٱلۡبَحۡرَيۡنِ يَلۡتَقِيَانِ

Adaika nyanja ziwiri zokumana (yamadzi amchere, ndi yamadzi ozizira). info
التفاسير:

external-link copy
20 : 55

بَيۡنَهُمَا بَرۡزَخٞ لَّا يَبۡغِيَانِ

Pakati pake pali chitsekerezo, sizilowana; info
التفاسير:

external-link copy
21 : 55

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?) info
التفاسير:

external-link copy
22 : 55

يَخۡرُجُ مِنۡهُمَا ٱللُّؤۡلُؤُ وَٱلۡمَرۡجَانُ

M’menemo mumatuluka ngale zing’onozing’ono ndi ngale zikuluzikulu. info
التفاسير:

external-link copy
23 : 55

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?) info
التفاسير:

external-link copy
24 : 55

وَلَهُ ٱلۡجَوَارِ ٱلۡمُنشَـَٔاتُ فِي ٱلۡبَحۡرِ كَٱلۡأَعۡلَٰمِ

Ndipo (Iye) ali nazo zombo (zimene zapangidwa ndi manja anu), zoyenda panyanja, zazikuluzikulu ngati mapiri. info
التفاسير:

external-link copy
25 : 55

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?) info
التفاسير:

external-link copy
26 : 55

كُلُّ مَنۡ عَلَيۡهَا فَانٖ

Zonse zili pamenepo (pa dziko) nzakutha. info
التفاسير:

external-link copy
27 : 55

وَيَبۡقَىٰ وَجۡهُ رَبِّكَ ذُو ٱلۡجَلَٰلِ وَٱلۡإِكۡرَامِ

Ndipo idzatsala nkhope ya Mbuye wako yaulemelero ndi mtendere. info
التفاسير:

external-link copy
28 : 55

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?) info
التفاسير:

external-link copy
29 : 55

يَسۡـَٔلُهُۥ مَن فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ كُلَّ يَوۡمٍ هُوَ فِي شَأۡنٖ

(Onse) akumwamba ndi pansi akupempha Iye (zofuna zawo)! Tsiku lililonse Iye ali ndi zochita (monga kupatsa uyu ulemelero, ndi kutsitsa uyu). info
التفاسير:

external-link copy
30 : 55

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

(Inu zolengedwa zamitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?) info
التفاسير:

external-link copy
31 : 55

سَنَفۡرُغُ لَكُمۡ أَيُّهَ ٱلثَّقَلَانِ

Posachedwapa (patsiku la chiweruziro), tidzaikapo mtima pa chiwerengero chanu (cha zochita zanu) inu anthu ndi ziwanda. info
التفاسير:

external-link copy
32 : 55

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?) info
التفاسير:

external-link copy
33 : 55

يَٰمَعۡشَرَ ٱلۡجِنِّ وَٱلۡإِنسِ إِنِ ٱسۡتَطَعۡتُمۡ أَن تَنفُذُواْ مِنۡ أَقۡطَارِ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ فَٱنفُذُواْۚ لَا تَنفُذُونَ إِلَّا بِسُلۡطَٰنٖ

E inu ziwanda ndi anthu! Ngati mungathe kutuluka m’mphepete mwa thambo ndi nthaka (pothawa Allah), tulukani! Simungathe kutuluka pokhapokha ndi mphamvu. (Koma inu simungathe kutero.) info
التفاسير:

external-link copy
34 : 55

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?) info
التفاسير:

external-link copy
35 : 55

يُرۡسَلُ عَلَيۡكُمَا شُوَاظٞ مِّن نَّارٖ وَنُحَاسٞ فَلَا تَنتَصِرَانِ

Mudzathiridwa malawi a moto ndi mtovu wa moto wosungunuka ndipo simungathe kupulumuka (ku chilango chimenechi). info
التفاسير:

external-link copy
36 : 55

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?) info
التفاسير:

external-link copy
37 : 55

فَإِذَا ٱنشَقَّتِ ٱلسَّمَآءُ فَكَانَتۡ وَرۡدَةٗ كَٱلدِّهَانِ

(Kumbuka) pamene thambo lidzang’ambika ndi kukhala lofiira ngati chikopa chofiira (kapena ngati mafuta oyaka). info
التفاسير:

external-link copy
38 : 55

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?) info
التفاسير:

external-link copy
39 : 55

فَيَوۡمَئِذٖ لَّا يُسۡـَٔلُ عَن ذَنۢبِهِۦٓ إِنسٞ وَلَا جَآنّٞ

Ndipo patsikulo munthu ndi chiwanda, sadzafunsidwa (aliyense) za tchimo lake. info
التفاسير:

external-link copy
40 : 55

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?) info
التفاسير:

external-link copy
41 : 55

يُعۡرَفُ ٱلۡمُجۡرِمُونَ بِسِيمَٰهُمۡ فَيُؤۡخَذُ بِٱلنَّوَٰصِي وَٱلۡأَقۡدَامِ

Adzadziwika oipa (pakati pa anthu ndi ziwanda) ndi zizindikiro zawo (zowazindikiritsa). Ndipo adzagwidwa maliombo awo ndi mapazi awo (ndi kuponyedwa ku Jahena). info
التفاسير:

external-link copy
42 : 55

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

((Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?) info
التفاسير:

external-link copy
43 : 55

هَٰذِهِۦ جَهَنَّمُ ٱلَّتِي يُكَذِّبُ بِهَا ٱلۡمُجۡرِمُونَ

(Kudzanenedwa mowadandaulitsa): Iyi ndi Jahannam yomwe adali kuitsutsa oipa. info
التفاسير:

external-link copy
44 : 55

يَطُوفُونَ بَيۡنَهَا وَبَيۡنَ حَمِيمٍ ءَانٖ

Adzakhala akuyenda pakati pa moto ndi pakati pa madzi owira, otentha kwambiri. info
التفاسير:

external-link copy
45 : 55

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?) info
التفاسير:

external-link copy
46 : 55

وَلِمَنۡ خَافَ مَقَامَ رَبِّهِۦ جَنَّتَانِ

Koma amene waopa kuti adzaimitsidwa kwa Mbuye wake (pa nthawi ya chiweruziro), adzalandira minda iwiri (yaikulu yamtendere). info
التفاسير:

external-link copy
47 : 55

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?) info
التفاسير:

external-link copy
48 : 55

ذَوَاتَآ أَفۡنَانٖ

(Minda ya mitengo) yanthambi zofwanthamuka. info
التفاسير:

external-link copy
49 : 55

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?) info
التفاسير:

external-link copy
50 : 55

فِيهِمَا عَيۡنَانِ تَجۡرِيَانِ

M’menemo muli akasupe awiri, omwe akuyenda. info
التفاسير:

external-link copy
51 : 55

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?) info
التفاسير:

external-link copy
52 : 55

فِيهِمَا مِن كُلِّ فَٰكِهَةٖ زَوۡجَانِ

M’menemo muli zipatso za mtundu uliwonse, mitundu iwiri iwiri. info
التفاسير:

external-link copy
53 : 55

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?) info
التفاسير:

external-link copy
54 : 55

مُتَّكِـِٔينَ عَلَىٰ فُرُشِۭ بَطَآئِنُهَا مِنۡ إِسۡتَبۡرَقٖۚ وَجَنَى ٱلۡجَنَّتَيۡنِ دَانٖ

Atatsamira pa zoyala, mkati mwake mosokelera veleveti wochindikala; ndipo zipatso zam’minda iwiriyi nzapafupi (kuzithyola). info
التفاسير:

external-link copy
55 : 55

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?) info
التفاسير:

external-link copy
56 : 55

فِيهِنَّ قَٰصِرَٰتُ ٱلطَّرۡفِ لَمۡ يَطۡمِثۡهُنَّ إِنسٞ قَبۡلَهُمۡ وَلَا جَآنّٞ

M’mindamo muli akazi oyang’ana amuna awo okha basi, (mawuthu) omwe sadakhalepo malo amodzi ndi munthu kapena chiwanda asadakumane ndi iwo. info
التفاسير:

external-link copy
57 : 55

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?) info
التفاسير:

external-link copy
58 : 55

كَأَنَّهُنَّ ٱلۡيَاقُوتُ وَٱلۡمَرۡجَانُ

Kukongola kwake (akaziwo) kuli ngati ngale zikuluzikulu ndi zing’onozing’ono. info
التفاسير:

external-link copy
59 : 55

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?) info
التفاسير:

external-link copy
60 : 55

هَلۡ جَزَآءُ ٱلۡإِحۡسَٰنِ إِلَّا ٱلۡإِحۡسَٰنُ

Malipiro a ntchito zabwino ndikulandira zabwino basi. info
التفاسير:

external-link copy
61 : 55

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?) info
التفاسير:

external-link copy
62 : 55

وَمِن دُونِهِمَا جَنَّتَانِ

Ndipo kuonjezera paminda iwiri (ija) palinso minda ina iwiri. info
التفاسير:

external-link copy
63 : 55

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?) info
التفاسير:

external-link copy
64 : 55

مُدۡهَآمَّتَانِ

Yobiriwira, kwambiri. info
التفاسير:

external-link copy
65 : 55

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?) info
التفاسير:

external-link copy
66 : 55

فِيهِمَا عَيۡنَانِ نَضَّاخَتَانِ

M’menemo muli akasupe awiri ofwamphuka madzi mwaphamvu. info
التفاسير:

external-link copy
67 : 55

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?) info
التفاسير:

external-link copy
68 : 55

فِيهِمَا فَٰكِهَةٞ وَنَخۡلٞ وَرُمَّانٞ

Mmenemo muli zipatso, mitengo yakanjedza ndi yamikangaza. info
التفاسير:

external-link copy
69 : 55

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?) info
التفاسير:

external-link copy
70 : 55

فِيهِنَّ خَيۡرَٰتٌ حِسَانٞ

M’menemo muli akazi amakhalidwe abwino, owala nkhope. info
التفاسير:

external-link copy
71 : 55

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?) info
التفاسير:

external-link copy
72 : 55

حُورٞ مَّقۡصُورَٰتٞ فِي ٱلۡخِيَامِ

Okongola maso, achikhalire m’mahema (m’matenti) awo. info
التفاسير:

external-link copy
73 : 55

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?) info
التفاسير:

external-link copy
74 : 55

لَمۡ يَطۡمِثۡهُنَّ إِنسٞ قَبۡلَهُمۡ وَلَا جَآنّٞ

Amene sadakhalepo malo amodzi ndi munthu kapena chiwanda asadakumane ndi iwo. info
التفاسير:

external-link copy
75 : 55

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?) info
التفاسير:

external-link copy
76 : 55

مُتَّكِـِٔينَ عَلَىٰ رَفۡرَفٍ خُضۡرٖ وَعَبۡقَرِيٍّ حِسَانٖ

Uku atatsamira misamiro yawofuwofu yokutidwa ndi zobiriwira; ndi zoyala zokongola, zakapangidwe kabwino. info
التفاسير:

external-link copy
77 : 55

فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ

(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake?) info
التفاسير:

external-link copy
78 : 55

تَبَٰرَكَ ٱسۡمُ رَبِّكَ ذِي ٱلۡجَلَٰلِ وَٱلۡإِكۡرَامِ

Latukuka ndi kudalitsika dzina la Mbuye wako Mwini ulemelero ndi ufulu. info
التفاسير: