クルアーンの対訳 - チェワ語対訳 - Khalid Ibrahim

ページ番号:close

external-link copy
34 : 40

وَلَقَدۡ جَآءَكُمۡ يُوسُفُ مِن قَبۡلُ بِٱلۡبَيِّنَٰتِ فَمَا زِلۡتُمۡ فِي شَكّٖ مِّمَّا جَآءَكُم بِهِۦۖ حَتَّىٰٓ إِذَا هَلَكَ قُلۡتُمۡ لَن يَبۡعَثَ ٱللَّهُ مِنۢ بَعۡدِهِۦ رَسُولٗاۚ كَذَٰلِكَ يُضِلُّ ٱللَّهُ مَنۡ هُوَ مُسۡرِفٞ مُّرۡتَابٌ

Ndithu adakudzerani kale Yûsuf ndi zisonyezo zoonekera poyera (Mûsa asadadze). Koma simudaleke kuzikaikira zimene adadza nazo kwa inu, kufikira pamene adamwalira, mudati: “Allah sadzatumiza mneneri wina pambuyo pake.” Motero Allah amamulekelera kusokera yemwe ali opyola malire poononga, wokaikira kwambiri. info
التفاسير:

external-link copy
35 : 40

ٱلَّذِينَ يُجَٰدِلُونَ فِيٓ ءَايَٰتِ ٱللَّهِ بِغَيۡرِ سُلۡطَٰنٍ أَتَىٰهُمۡۖ كَبُرَ مَقۡتًا عِندَ ٱللَّهِ وَعِندَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْۚ كَذَٰلِكَ يَطۡبَعُ ٱللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ قَلۡبِ مُتَكَبِّرٖ جَبَّارٖ

Amene akutsutsana za zisonyezo za Allah popanda umboni uliwonse umene wawadzera. (Kutsutsa zisonyezo za Allah) nchokwiitsa Allah kwakukulu ndi kwa amene akhulupirira (mwa Allah). Momwemo ndi momwe Allah amadindira pamtima wa aliyense wodzikuza, wodzitukumula. info
التفاسير:

external-link copy
36 : 40

وَقَالَ فِرۡعَوۡنُ يَٰهَٰمَٰنُ ٱبۡنِ لِي صَرۡحٗا لَّعَلِّيٓ أَبۡلُغُ ٱلۡأَسۡبَٰبَ

Ndipo Farawo adati: “E iwe Haamana! Ndimangire chipilala kuti ndikafike kunjira,” info
التفاسير:

external-link copy
37 : 40

أَسۡبَٰبَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ فَأَطَّلِعَ إِلَىٰٓ إِلَٰهِ مُوسَىٰ وَإِنِّي لَأَظُنُّهُۥ كَٰذِبٗاۚ وَكَذَٰلِكَ زُيِّنَ لِفِرۡعَوۡنَ سُوٓءُ عَمَلِهِۦ وَصُدَّ عَنِ ٱلسَّبِيلِۚ وَمَا كَيۡدُ فِرۡعَوۡنَ إِلَّا فِي تَبَابٖ

“Njira za kumwamba kuti ndikamuone Mulungu wa Mûsa. Koma ndithu ine ndikudziwa kuti ameneyu ngonama.” Umo ndi momwe zochita zoipa za Farawo zidakongoletsedwera kwa iye, ndipo adatsekeretsedwa ku njira yoona, ndipo chiwembu cha Farawo sichakanthu, koma choonongeka. info
التفاسير:

external-link copy
38 : 40

وَقَالَ ٱلَّذِيٓ ءَامَنَ يَٰقَوۡمِ ٱتَّبِعُونِ أَهۡدِكُمۡ سَبِيلَ ٱلرَّشَادِ

Ndipo uja adakhulupirira adati: “E inu anthu anga! Nditsatireni; ndikuongolerani ku njira yoongoka.” info
التفاسير:

external-link copy
39 : 40

يَٰقَوۡمِ إِنَّمَا هَٰذِهِ ٱلۡحَيَوٰةُ ٱلدُّنۡيَا مَتَٰعٞ وَإِنَّ ٱلۡأٓخِرَةَ هِيَ دَارُ ٱلۡقَرَارِ

“E inu anthu anga! Ndithu moyo wa pa dziko lapansi ndichisangalalo (chakutha). Ndithu tsiku lachimaliziro ndiye nyumba yokhazikikamo.” info
التفاسير:

external-link copy
40 : 40

مَنۡ عَمِلَ سَيِّئَةٗ فَلَا يُجۡزَىٰٓ إِلَّا مِثۡلَهَاۖ وَمَنۡ عَمِلَ صَٰلِحٗا مِّن ذَكَرٍ أَوۡ أُنثَىٰ وَهُوَ مُؤۡمِنٞ فَأُوْلَٰٓئِكَ يَدۡخُلُونَ ٱلۡجَنَّةَ يُرۡزَقُونَ فِيهَا بِغَيۡرِ حِسَابٖ

“Amene akuchita choipa sadzalipidwa chinachake koma chofanana ndi chomwe adachita. Ndipo yemwe akuchita zabwino, mwamuna kapena mkazi, uku iye ali okhulupirira, iwowo adzalowa ku Minda ya mtendere. Adzapatsidwa zopatsidwa mmenemo zopanda chiwerengero.” info
التفاسير: