クルアーンの対訳 - チェワ語対訳 - Khalid Ibrahim

Sâd

external-link copy
1 : 38

صٓۚ وَٱلۡقُرۡءَانِ ذِي ٱلذِّكۡرِ

Sad, ndikulumbira Qur’an (iyi) ya ulaliki (wothandiza). info
التفاسير:

external-link copy
2 : 38

بَلِ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ فِي عِزَّةٖ وَشِقَاقٖ

Koma amene sadakhulupirire ali mkudzitukumula ndi makani. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 38

كَمۡ أَهۡلَكۡنَا مِن قَبۡلِهِم مِّن قَرۡنٖ فَنَادَواْ وَّلَاتَ حِينَ مَنَاصٖ

Kodi ndimibadwo ingati taiwononga patsogolo pawo? Adakuwa kuitana (panthawi imeneyo), koma nthawi yopulumuka idali itatha. info
التفاسير:

external-link copy
4 : 38

وَعَجِبُوٓاْ أَن جَآءَهُم مُّنذِرٞ مِّنۡهُمۡۖ وَقَالَ ٱلۡكَٰفِرُونَ هَٰذَا سَٰحِرٞ كَذَّابٌ

Ndipo anadabwa atawadzera mchenjezi wochokera mwa iwo. Ndipo osakhulupirira adati: “Uyu ndiwamatsenga; ngwabodza lamkunkhuniza!” info
التفاسير:

external-link copy
5 : 38

أَجَعَلَ ٱلۡأٓلِهَةَ إِلَٰهٗا وَٰحِدًاۖ إِنَّ هَٰذَا لَشَيۡءٌ عُجَابٞ

Ha! Waichita milungu yambirimbiri ija kuti ikhale Mulungu Mmodzi Yekha? Ndithu ichi nchinthu chodabwitsa.” info
التفاسير:

external-link copy
6 : 38

وَٱنطَلَقَ ٱلۡمَلَأُ مِنۡهُمۡ أَنِ ٱمۡشُواْ وَٱصۡبِرُواْ عَلَىٰٓ ءَالِهَتِكُمۡۖ إِنَّ هَٰذَا لَشَيۡءٞ يُرَادُ

Ndipo adanyamuka akuluakulu a mwa iwo nati: “Nyamukani muzikapitiriza kupembedza milungu yanu. Ndithu chinthu ichi (nchoipa); chikulinga ife (kuti tisiyane ndi milungu yathu).” info
التفاسير:

external-link copy
7 : 38

مَا سَمِعۡنَا بِهَٰذَا فِي ٱلۡمِلَّةِ ٱلۡأٓخِرَةِ إِنۡ هَٰذَآ إِلَّا ٱخۡتِلَٰقٌ

“Sitidamve zimenezi (zakuti Mulungu Ndimmodzi ngakhale) m’chipembedzo chakale (Chikhrisitu). Ichi sikanthu, koma ndibodza lopeka.” info
التفاسير:

external-link copy
8 : 38

أَءُنزِلَ عَلَيۡهِ ٱلذِّكۡرُ مِنۢ بَيۡنِنَاۚ بَلۡ هُمۡ فِي شَكّٖ مِّن ذِكۡرِيۚ بَل لَّمَّا يَذُوقُواْ عَذَابِ

“Kodi uthengawo (wakuti Mulungu Ndimmodzi) wavumbulutsidwa kwa iye pakati pathu?” Koma iwo akukaika ndi ulaliki Wanga. Koma sadalawebe chilango Changa. info
التفاسير:

external-link copy
9 : 38

أَمۡ عِندَهُمۡ خَزَآئِنُ رَحۡمَةِ رَبِّكَ ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡوَهَّابِ

Kodi iwo ali nazo nkhokwe za chifundo cha Mbuye wako, Wamphamvu zoposa, Wopatsa mochuluka? info
التفاسير:

external-link copy
10 : 38

أَمۡ لَهُم مُّلۡكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَاۖ فَلۡيَرۡتَقُواْ فِي ٱلۡأَسۡبَٰبِ

Kapena ufumu wa kumwamba ndi pansi ndi zapakati pake, ngwawo. Ngati zili choncho atakwera makwelero (kuti akafike pamalo poti akalamulire zimene akufuna, ngati angathe kutero). info
التفاسير:

external-link copy
11 : 38

جُندٞ مَّا هُنَالِكَ مَهۡزُومٞ مِّنَ ٱلۡأَحۡزَابِ

Awa (Aquraish kuonjezera pa kudzitama kwawo), nkagulu kochepa ndi kofooka. Kagonjetsedwa monga makamu ankhondo (omwe adagonjetsedwa kale omwe amatsutsana ndi aneneri akale). info
التفاسير:

external-link copy
12 : 38

كَذَّبَتۡ قَبۡلَهُمۡ قَوۡمُ نُوحٖ وَعَادٞ وَفِرۡعَوۡنُ ذُو ٱلۡأَوۡتَادِ

Patsogolo pawo, anthu a Nuh, Âdi ndi Farawo, mwini nyumba zitalizitali (Pyramid), adatsutsa (aneneri awo). info
التفاسير:

external-link copy
13 : 38

وَثَمُودُ وَقَوۡمُ لُوطٖ وَأَصۡحَٰبُ لۡـَٔيۡكَةِۚ أُوْلَٰٓئِكَ ٱلۡأَحۡزَابُ

Ndi Asamudu, ndi anthu a Luti ndi (anthu a Shuaib) eni mitengo yambiri yothothana, amenewo ndiwo makamu. info
التفاسير:

external-link copy
14 : 38

إِن كُلٌّ إِلَّا كَذَّبَ ٱلرُّسُلَ فَحَقَّ عِقَابِ

Onsewa adatsutsa atumiki; basi chilango Changa chidatsimikizika (pa iwo). info
التفاسير:

external-link copy
15 : 38

وَمَا يَنظُرُ هَٰٓؤُلَآءِ إِلَّا صَيۡحَةٗ وَٰحِدَةٗ مَّا لَهَا مِن فَوَاقٖ

Ndipo awa (Aquraish), sayembekeza china koma mkuwe umodzi wosabwereza. (Ndipo ukadzachitika, onse adzafa). info
التفاسير:

external-link copy
16 : 38

وَقَالُواْ رَبَّنَا عَجِّل لَّنَا قِطَّنَا قَبۡلَ يَوۡمِ ٱلۡحِسَابِ

Ndipo akunena (mwachipongwe): “E Mbuye wathu! Tipatsirenitu gawo la chilango chathu lisanafike tsiku lachiwerengero.” info
التفاسير: