[287] Munthu amene ali ndi chikaiko za kuuka ku imfa, pafunika kuti aganizire zomwe zili m’ndime iyi yolemekezeka kuti aone komwe wachokera ndi komwe wafika. Kenako aone nthaka polingalira mozama momwe imakhalira yachilala. Koma mvula ikaivumbwira ndikudzuka, kuti adziwe kuti amene akuchita zimenezi palibe chomwe angalephere.