[40] Ngati udamkwatira mkazi ndipo nkulekana naye usanalowane naye, umpatse theka lachiwongo chomwe chidatchulidwa. Ngati udampatsa chiwongo chonse, ndiye kuti akubwezere theka lake. Koma ndibwino kwa mwamuna kumpatsa mkazi chiwongo chonse ngati anali asanampatse. Ngati anampatsa asaitanitsenso chiwongocho. Ndibwinonso kwa mkazi kubweza chiwongo chonse ngati adampatsa chonse, kapena kukana kuti asampatse ngati anali asanapatsidwe. Aliyense mwa awiriwa asakhale ndi chibaba chofuna kupeza ndalama pakutha pa ukwatiwo. Malamulo tanenawa amagwira ntchito ngati chiwongo chidatchulidwa kuchuluka kwake pomwe ankafunsira ukwati. Koma ngati chiwongocho sanachitchule kuchuluka kwake kotero kuti sadagwirizane za chiwongocho kuti adzapereka mwakutimwakuti, pamenepa ndiye kuti ampatse chinthu cholekanira choti chimsangalatse. Ili ndilo tanthauzo la zomwe zatchulidwa m’ndime ya 236.
Ndithudi apa akutilangiza mwamphamvu kuti tizichitirana zabwino ngakhale panthawi yolekana ukwati. Anthu asaiwale ubwino ndi chikondi zomwe ankachitirana pakati pawo.