クルアーンの対訳 - チェワ語対訳 - Khalid Ibrahim

ページ番号:close

external-link copy
34 : 14

وَءَاتَىٰكُم مِّن كُلِّ مَا سَأَلۡتُمُوهُۚ وَإِن تَعُدُّواْ نِعۡمَتَ ٱللَّهِ لَا تُحۡصُوهَآۗ إِنَّ ٱلۡإِنسَٰنَ لَظَلُومٞ كَفَّارٞ

Ndipo wakupatsani mu zonse zomwe mwampempha (ndi zimene simudam’pemphe). Ngati mutayesa kuwerenga madalitso a Allah, simungathe kuwawerenga. Ndithu munthu ngwachinyengo chachikulu, ngosathokoza. info
التفاسير:

external-link copy
35 : 14

وَإِذۡ قَالَ إِبۡرَٰهِيمُ رَبِّ ٱجۡعَلۡ هَٰذَا ٱلۡبَلَدَ ءَامِنٗا وَٱجۡنُبۡنِي وَبَنِيَّ أَن نَّعۡبُدَ ٱلۡأَصۡنَامَ

Ndipo (kumbukani) pamene Ibrahim adanena: “Mbuye wanga! Uchiteni mzinda uwu (wa Makka) kukhala wa mtendere; ndipo ndipatuleni ine ndi ana anga ku machitidwe opembedza mafano.” info
التفاسير:

external-link copy
36 : 14

رَبِّ إِنَّهُنَّ أَضۡلَلۡنَ كَثِيرٗا مِّنَ ٱلنَّاسِۖ فَمَن تَبِعَنِي فَإِنَّهُۥ مِنِّيۖ وَمَنۡ عَصَانِي فَإِنَّكَ غَفُورٞ رَّحِيمٞ

“Mbuye wanga! Ndithu (mafano) awa asokeretsa anthu ambiri. Choncho amene wanditsata, ndithu iyeyo ali mwa ine (mudzamulipira chabwino monga mwandilonjeza), ndipo amene wandinyoza (mutha kumukhululukira) ndithu Inu Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni.” info
التفاسير:

external-link copy
37 : 14

رَّبَّنَآ إِنِّيٓ أَسۡكَنتُ مِن ذُرِّيَّتِي بِوَادٍ غَيۡرِ ذِي زَرۡعٍ عِندَ بَيۡتِكَ ٱلۡمُحَرَّمِ رَبَّنَا لِيُقِيمُواْ ٱلصَّلَوٰةَ فَٱجۡعَلۡ أَفۡـِٔدَةٗ مِّنَ ٱلنَّاسِ تَهۡوِيٓ إِلَيۡهِمۡ وَٱرۡزُقۡهُم مِّنَ ٱلثَّمَرَٰتِ لَعَلَّهُمۡ يَشۡكُرُونَ

“Mbuye wanga! Ndithu ine ndaikhazika ina mwa mbumba yanga (mwana wanga Ismail) pachigwa ichi (cha Makka) chopanda zomera pa Nyumba Yanu Yopatulika (Al-Ka’ba); Mbuye wathu (aloleni) kuti akhale opemphera Swala; choncho ichiteni mitima ya anthu kukhala yopendekera kwa iwo (akonde kudzakhala malo amenewo), ndipo apatseni zipatso kuti athokoze.” info
التفاسير:

external-link copy
38 : 14

رَبَّنَآ إِنَّكَ تَعۡلَمُ مَا نُخۡفِي وَمَا نُعۡلِنُۗ وَمَا يَخۡفَىٰ عَلَى ٱللَّهِ مِن شَيۡءٖ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَلَا فِي ٱلسَّمَآءِ

“Mbuye wathu! Ndithu Inu mukudziwa zimene tikubisa ndi zomwe tikuonetsa poyera. Ndipo palibe chilichonse chobisika kwa Allah, m’dziko kapena kumwamba. info
التفاسير:

external-link copy
39 : 14

ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ ٱلَّذِي وَهَبَ لِي عَلَى ٱلۡكِبَرِ إِسۡمَٰعِيلَ وَإِسۡحَٰقَۚ إِنَّ رَبِّي لَسَمِيعُ ٱلدُّعَآءِ

“Kuyamikidwa konse nkwa Allah Yemwe wandipatsa ine ku ukulu Ismail ndi Ishâq. Ndithu Mbuye wanga Ngwakumva pempho (la kapolo Wake).” info
التفاسير:

external-link copy
40 : 14

رَبِّ ٱجۡعَلۡنِي مُقِيمَ ٱلصَّلَوٰةِ وَمِن ذُرِّيَّتِيۚ رَبَّنَا وَتَقَبَّلۡ دُعَآءِ

“Mbuye wanga! Ndichiteni kukhala wopemphera Swala pamodzi ndi mbumba yanga. Mbuye wathu! Landirani zopempha zanga.” info
التفاسير:

external-link copy
41 : 14

رَبَّنَا ٱغۡفِرۡ لِي وَلِوَٰلِدَيَّ وَلِلۡمُؤۡمِنِينَ يَوۡمَ يَقُومُ ٱلۡحِسَابُ

“Mbuye wathu! Ndikhululukireni ine ndi makolo anga ndi amene akhulupirira, (makamaka) patsiku la chiwerengero (Qiyâma)!” info
التفاسير:

external-link copy
42 : 14

وَلَا تَحۡسَبَنَّ ٱللَّهَ غَٰفِلًا عَمَّا يَعۡمَلُ ٱلظَّٰلِمُونَۚ إِنَّمَا يُؤَخِّرُهُمۡ لِيَوۡمٖ تَشۡخَصُ فِيهِ ٱلۡأَبۡصَٰرُ

Ndipo usaganize kuti Allah waiwala zomwe akuchita oipa. Ndithudi, Iye akuwalekelera chabe mpaka tsiku lomwe maso awo adzatong’oke (chifukwa cha mantha).[243] info

[243] Ndithudi machitidwe a Allah nkuwalekelera oipa pamene akuchita zoipa. Sawalanga mwachangu. Koma akafuna kuwalanga amawakhaulitsa ndi chilango choopsa. Choncho munthu asanyengeke pamene akulakwira Allah namulekelera osamulanga.

التفاسير: