クルアーンの対訳 - チェワ語対訳 - Khalid Ibrahim

ページ番号:close

external-link copy
96 : 12

فَلَمَّآ أَن جَآءَ ٱلۡبَشِيرُ أَلۡقَىٰهُ عَلَىٰ وَجۡهِهِۦ فَٱرۡتَدَّ بَصِيرٗاۖ قَالَ أَلَمۡ أَقُل لَّكُمۡ إِنِّيٓ أَعۡلَمُ مِنَ ٱللَّهِ مَا لَا تَعۡلَمُونَ

Choncho pamene adadza wotenga nkhani yabwino, adauponya (mkanjo wa Yûsuf) pankhope pake, ndipo pompo adapenya. Adati: “Kodi sindinakuuzeni kuti ine ndikudziwa kupyolera mwa Allah zomwe inu simukuzidziwa?” info
التفاسير:

external-link copy
97 : 12

قَالُواْ يَٰٓأَبَانَا ٱسۡتَغۡفِرۡ لَنَا ذُنُوبَنَآ إِنَّا كُنَّا خَٰطِـِٔينَ

(Iwo) adati: “E bambo wathu! Tipemphereni chikhululuko pa machimo athu. Ndithu ife tidali olakwa.” info
التفاسير:

external-link copy
98 : 12

قَالَ سَوۡفَ أَسۡتَغۡفِرُ لَكُمۡ رَبِّيٓۖ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلۡغَفُورُ ٱلرَّحِيمُ

(Iye) adati: “Posachedwapa (ndikamuona Yûsuf) ndikupempherani chikhululuko kwa Mbuye wanga. Ndithu Iye Ngokhululuka zedi, Ngwachisoni chosatha.” info
التفاسير:

external-link copy
99 : 12

فَلَمَّا دَخَلُواْ عَلَىٰ يُوسُفَ ءَاوَىٰٓ إِلَيۡهِ أَبَوَيۡهِ وَقَالَ ٱدۡخُلُواْ مِصۡرَ إِن شَآءَ ٱللَّهُ ءَامِنِينَ

Ndipo pamene adalowa kwa Yûsuf, adawakumbatira makolo ake ndikunena: “Lowani mu Iguputo, In-shaa-Allah, (Allah akalola) mwamtendere.” info
التفاسير:

external-link copy
100 : 12

وَرَفَعَ أَبَوَيۡهِ عَلَى ٱلۡعَرۡشِ وَخَرُّواْ لَهُۥ سُجَّدٗاۖ وَقَالَ يَٰٓأَبَتِ هَٰذَا تَأۡوِيلُ رُءۡيَٰيَ مِن قَبۡلُ قَدۡ جَعَلَهَا رَبِّي حَقّٗاۖ وَقَدۡ أَحۡسَنَ بِيٓ إِذۡ أَخۡرَجَنِي مِنَ ٱلسِّجۡنِ وَجَآءَ بِكُم مِّنَ ٱلۡبَدۡوِ مِنۢ بَعۡدِ أَن نَّزَغَ ٱلشَّيۡطَٰنُ بَيۡنِي وَبَيۡنَ إِخۡوَتِيٓۚ إِنَّ رَبِّي لَطِيفٞ لِّمَا يَشَآءُۚ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلۡعَلِيمُ ٱلۡحَكِيمُ

Ndipo (pamene adafika kwa Yûsuf), (iye) adawakweza makolo ake ndikuwaika pa chimpando (chake) chachifumu, ndipo onse adagwa kumlambira (monga mwachizolowezi chawo nthawi imeneyo). Ndipo (Yûsuf) adati: “E inu bambo wanga! Ili ndilo tanthauzo (lenileni) la maloto anga akale. Palibe chipeneko Mbuye wanga wawatsimikiza (malotowo). Ndipo adandichitira zabwino ponditulutsa kundende ndi pokubweretsani inu kuchokera kumidzi (Kenani), pambuyo pokhwirizira (chidani) satana pakati pa ine ndi abale anga. Ndithudi Mbuye wanga amadziwa kwambiri chinsinsi cha zomwe wakonza kuti zichitike. Ndithu Iye Ngodziwa, Ngwanzeru. info
التفاسير:

external-link copy
101 : 12

۞ رَبِّ قَدۡ ءَاتَيۡتَنِي مِنَ ٱلۡمُلۡكِ وَعَلَّمۡتَنِي مِن تَأۡوِيلِ ٱلۡأَحَادِيثِۚ فَاطِرَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ أَنتَ وَلِيِّۦ فِي ٱلدُّنۡيَا وَٱلۡأٓخِرَةِۖ تَوَفَّنِي مُسۡلِمٗا وَأَلۡحِقۡنِي بِٱلصَّٰلِحِينَ

(Kenako adathokoza ndi kupempha Allah kuti): “E Mbuye wanga! Ndithu mwandipatsako ufumu ndi kundiphunzitsako kumasulira nkhani (maloto). E Inu Mlengi wa thambo ndi nthaka! Inu ndiye Mtetezi wanga pa dziko lapansi ndi tsiku la chimaliziro. (Ndipo nthawi ya imfa yanga) mudzandipatse imfa ndili Msilamu ndipo kandikumanitseni ndi ochita zabwino.” info
التفاسير:

external-link copy
102 : 12

ذَٰلِكَ مِنۡ أَنۢبَآءِ ٱلۡغَيۡبِ نُوحِيهِ إِلَيۡكَۖ وَمَا كُنتَ لَدَيۡهِمۡ إِذۡ أَجۡمَعُوٓاْ أَمۡرَهُمۡ وَهُمۡ يَمۡكُرُونَ

Izi ndi zina mwa nkhani zamseri (zomwe) tikukuululira iwe. Ndipo siudali nawo pamodzi pamene adatsimika chochita chawo (uku) akuchita chiwembu (chawo) choipa. info
التفاسير:

external-link copy
103 : 12

وَمَآ أَكۡثَرُ ٱلنَّاسِ وَلَوۡ حَرَصۡتَ بِمُؤۡمِنِينَ

Ndipo ambiri mwa anthu sakhulupirira ngakhale utalimbika chotani. info
التفاسير: