[411] Buruj ndi nyenyezi zomwe zimakhala m’magulumagulu ndipo gulu lililonse limatchedwa Buruj. Ndipo Buruj zonse zilipo khumi ndi ziwiri (12). Zisanu ndi imodzi zili kumpoto kwa “Equator”, pomwe zisanu ndi imodzi zili kumwera kwake.
[412] “Woikira umboni ndi woikiridwa umboni” angathe kukhala aliyense woikira umboni ndi woikiridwa umboni pa tsiku lachimaliziro, monga aneneri adzaikira umboni anthu pa zabwino kapena zoipa; pa malo pochitira mapemphero padzamuikira umboni wazabwino yemwe adali kupempherapo. Ndipo pamalo pomwe padali kuchitikira zoipa padzawachitira umboni anthu oipa za machimo awo: ngakhale ziwalo ndi khungu nazonso pa tsiku limenelo zidzaikira umboni kwa mwini ziwalozo. Basi munthu akatsimikiza kuchita machimo akumbukire kuti ali nazo mboni zambiri zomwe zikumuona ndipo pa tsiku la chiweruziro zidzaima pa maso pa Allah kupereka umboni wokhudza munthuyo.
[413] Pamene Ayuda a ku Najrani adalowa m’Chikhristu, (Chisilamu chisadafike ndiponso Chikhristu chisadaonongeke), idamufika nkhaniyi mfumu yawo dzina lake Dhu-Nuwas; adabwera ku Najrani ndi gulu lankhondo lalikulu; adawakakamizira anthu ku Chiyuda koma iwo adakana. Nayamba kuwapha anthu okhulupilirawo powaponya m’ngalande za moto.
[414] Tanthauzo la “kuwazunza” apa ndiko kuwavutitsa ndi kuwathetsa mphamvu kuti asiye chikhulupiliro chawo; asakhulupirire mwa Allah. Mawuwa ngakhale akukhudzana ndi eni ngalande za moto, akukhudzanso akafiri a m’Makka omwe adali kuzunza Asilamu ndi mazunzo osiyanasiyana kuti abwelere kuchipembedzo cha mafano. Ndipo zimenezi zikhudzanso aliyense.
[415] (Ndime 12-16) Allah pambuyo powatonthoza Asilamu pakuwauza zomwe zidawaonekera abale awo amene adatsogola, tsopanonso akuwatonthoza ndi ufumu Wake wolemekezeka kuti adziwe kuti awo akafiri omwe akudziona kuti ali ndi mphamvu zolangira anzawo, Iye sangamuthe. Akafuna adzawalanga ndi chilango cha dziko lapansi ndi cha tsiku lachimaliziro, kapena chimodzi mwa zilangozi; pakuti Iye Ngokhululuka kwambiri ndiponso Ngwachikondi zedi, awatembenula mitima yawo kuti achikhulupirire chimene adachikana. Chifukwa cha mphamvu Zake zoposa, Allah, adachita zonsezi ziwiri. Patapita zaka zochepa adawapatsa mphamvu omwe adali opanda mphamvu, kenaka adayamba kuwalanga osakhulupilira aja chilango cha padziko, monga Abu Jahl ndi anzake omwe adali kumutsutsa kwambiri Mtumiki (s.a.w) pamodzi ndi omutsatira ake. Ndipo ena adawatembenula mitima yawo nkulowa mchipembedzo cha Chisilamu; adaima ndikuchiteteza Chisilamu popereka nsembe ya mizimu yawo ndi chuma chawo.