[175] Chisilamu kuti chikamthandize munthu nkofunika kuti achigwiritsire ntchito pa moyo wake wonse. Chisilamu chokha popanda kuchigwiritsira ntchito sichikwanira ndiponso sichingamtchinjirize munthu kuchilango cha Moto. Ndipo yemwe sali msilamu kuti Chisilamu chikamthandize nkofunika kuti alowe m’Chisilamu ali ndi moyo, osati pamene imfa yamufika. Ndipo nayenso msilamu wochita zoipa, akalapa imfa itamufika kale kulapa kwakeko sikungamthandize. Koma alape pamene ali ndi moyo wangwiro. Pamenepo ndiye kuti Allah alandira kulapa kwake. Osati kulapa uku imfa akuiona ndi maso ake.
[176] China mwa chifundo cha Allah pa zolengedwa zake ndiko kuti adzamulipira munthu pa tsiku la chimaliziro mosiyanitsa pakati pa chabwino ndi choipa. Ngati adachita chabwino chimodzi, adzamulipira mphoto ya zinthu khumi zoposera pa chabwino chimodzicho ndipo ngati adachita choipa, sadzamuonjezera malipiro a choipacho koma adzamulipira chofanana ndi choipacho. Tanthauzo lake nkuti chabwino chimodzi malipiro ake ndi zabwino khumi; pomwe choipa chimodzi mphoto yake ndi choipanso chimodzi.
[177] Ndime iyi ikusonyeza kuti kukhupuka ndi ulemelero, sindizo zizindikiro zosonyeza kuti munthuyo ngofunika kwa Allah. Ndiponso kusauka ndi kunyozeka sizizindikiro kuti munthuyo ngosafunika kwa Allah kapena wonyozeka kwa Allah. Koma kulemera, ulemelero, kusauka ndi kunyozeka.zonsezi amazipereka m’njira ya mayeso.