Traduzione dei Significati del Sacro Corano - Traduzione chicheŵa - Khalid Ibrahim Betyala

Al-Fath

external-link copy
1 : 48

إِنَّا فَتَحۡنَا لَكَ فَتۡحٗا مُّبِينٗا

Ndithu takugonjetsera (iwe Mtumiki{s.a.w}mzinda wa Makka) kugonjetsa kwakukulu koonekera poyera.[346] info

[346] M’chaka cha chisanu ndi chimodzi chisamukire Mtumiki (s.a.w), Mtumiki (s.a.w) adapita ku Makka kuchokera ku Madina pamodzi ndi omtsatira ake kuti akachite Umrah imene ndi Hajj yaing’ono. Koma atayandikira ku Makka, Aquraish adamuletsa kulowa mu mzindamo kuti asachite mapemphero a Umrah. Ndipo atakambiranakambirana adamvana mfundo zingapo, zina mwa izo ndi:-
(i) Asamenyane nthawi imeneyo.
(ii) Abwelere ndipo adzabwere chaka chotsatiracho mwezi wonga umenewo kudzachita mapemphero. Panthawiyo sadzawaletsa kulowa mu mzindawo.
(iii) Asiye kumenyana pakati pawo kwa zaka khumi, ndi kumayenderana m’mene angafunire; Aquraish azipita ku Madina ngati atafuna, popanda kuzunzidwa.
(iv) Mafuko ena a Arabu adaloledwa kulowa nawo m’pangano limeneli kuti asamthire nkhondo Mtumiki (s.a.w), ndipo iyenso asawathire nkhondo.

التفاسير:

external-link copy
2 : 48

لِّيَغۡفِرَ لَكَ ٱللَّهُ مَا تَقَدَّمَ مِن ذَنۢبِكَ وَمَا تَأَخَّرَ وَيُتِمَّ نِعۡمَتَهُۥ عَلَيۡكَ وَيَهۡدِيَكَ صِرَٰطٗا مُّسۡتَقِيمٗا

Kuti Allah akukhululukire zolakwa zako zapatsogolo ndi zapambuyo, ndi kukukwaniritsira mtendere Wake, ndi kukuongolera kunjira yolunjika. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 48

وَيَنصُرَكَ ٱللَّهُ نَصۡرًا عَزِيزًا

Ndikuti Allah akuteteze ndi chitetezo champhamvu. info
التفاسير:

external-link copy
4 : 48

هُوَ ٱلَّذِيٓ أَنزَلَ ٱلسَّكِينَةَ فِي قُلُوبِ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ لِيَزۡدَادُوٓاْ إِيمَٰنٗا مَّعَ إِيمَٰنِهِمۡۗ وَلِلَّهِ جُنُودُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ وَكَانَ ٱللَّهُ عَلِيمًا حَكِيمٗا

Iye ndiamene adatsitsa chikhazikiko (kudekha) m’mitima mwa okhulupirira kuti awonjezera chikhulupiliro pachikhulupiro chawo. Makamu ankhondo akumwamba ndi pansi, nga Allah, (monga angelo, ziwanda, nyama ziphaliwali, mphepo yamkuntho ndi zivomerezi ndi zina zotero); ndipo Allah Ngodziwa chilichonse, ndiponso Wanzeru zakuya. info
التفاسير:

external-link copy
5 : 48

لِّيُدۡخِلَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ وَٱلۡمُؤۡمِنَٰتِ جَنَّٰتٖ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ خَٰلِدِينَ فِيهَا وَيُكَفِّرَ عَنۡهُمۡ سَيِّـَٔاتِهِمۡۚ وَكَانَ ذَٰلِكَ عِندَ ٱللَّهِ فَوۡزًا عَظِيمٗا

(Wachita izi) kuti okhulupirira aamuna ndi aakazi akawalowetse m’minda yomwe pansi pake ikuyenda mitsinje; adzakhala nthawi yaitali mmenemo, ndi kuti awafafanizire zolakwa zawo; kumeneko, kwa Allah ndiko kupambana kwakukulu. info
التفاسير:

external-link copy
6 : 48

وَيُعَذِّبَ ٱلۡمُنَٰفِقِينَ وَٱلۡمُنَٰفِقَٰتِ وَٱلۡمُشۡرِكِينَ وَٱلۡمُشۡرِكَٰتِ ٱلظَّآنِّينَ بِٱللَّهِ ظَنَّ ٱلسَّوۡءِۚ عَلَيۡهِمۡ دَآئِرَةُ ٱلسَّوۡءِۖ وَغَضِبَ ٱللَّهُ عَلَيۡهِمۡ وَلَعَنَهُمۡ وَأَعَدَّ لَهُمۡ جَهَنَّمَۖ وَسَآءَتۡ مَصِيرٗا

Ndi kuti awalange achiphamaso aamuna ndi aakazi ndi omphatikiza Allah aamuna ndi aakazi oganizira Allah maganizo achabe. Kutembenuka koipa kuli kwa iwo ndipo Allah wawakwiyira ndiponso wawatembelera ndi kuwakonzera Jahannamu. Ndipo kumeneko nkobwerera koipa. info
التفاسير:

external-link copy
7 : 48

وَلِلَّهِ جُنُودُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ وَكَانَ ٱللَّهُ عَزِيزًا حَكِيمًا

Ndipo magulu ankhondo akumwamba ndi pansi nga Allah; ndipo Allah ndi Wamphamvu zoposa, Wa nzeru zakuya. info
التفاسير:

external-link copy
8 : 48

إِنَّآ أَرۡسَلۡنَٰكَ شَٰهِدٗا وَمُبَشِّرٗا وَنَذِيرٗا

Ndithu takutumiza kuti ukhale mboni ndi wolengeza nkhani zabwino ndiponso mchenjezi. info
التفاسير:

external-link copy
9 : 48

لِّتُؤۡمِنُواْ بِٱللَّهِ وَرَسُولِهِۦ وَتُعَزِّرُوهُ وَتُوَقِّرُوهُۚ وَتُسَبِّحُوهُ بُكۡرَةٗ وَأَصِيلًا

Ncholinga choti mumkhulupirire Allah ndi Mtumiki Wake, ndi kuti mumtukule ndi kumulemekeza (Mtumiki) ndi kutinso mumtamande (Allah) m’mawa ndi madzulo. info
التفاسير: