Traduzione dei Significati del Sacro Corano - Traduzione chicheŵa - Khalid Ibrahim Betyala

Numero di pagina:close

external-link copy
80 : 4

مَّن يُطِعِ ٱلرَّسُولَ فَقَدۡ أَطَاعَ ٱللَّهَۖ وَمَن تَوَلَّىٰ فَمَآ أَرۡسَلۡنَٰكَ عَلَيۡهِمۡ حَفِيظٗا

Yemwe angamvere Mtumiki ndiye kuti wamvera Allah, (chifukwa chakuti zonse zomwe iye akulamula nzotumidwa ndi Allah). Ndipo amene atembenukire kutali (kunyoza iwe, ndiye kuti zoipa zili pa iye mwini). Sitidakutumize iweyo kukhala muyang’anili pa iwo. info
التفاسير:

external-link copy
81 : 4

وَيَقُولُونَ طَاعَةٞ فَإِذَا بَرَزُواْ مِنۡ عِندِكَ بَيَّتَ طَآئِفَةٞ مِّنۡهُمۡ غَيۡرَ ٱلَّذِي تَقُولُۖ وَٱللَّهُ يَكۡتُبُ مَا يُبَيِّتُونَۖ فَأَعۡرِضۡ عَنۡهُمۡ وَتَوَكَّلۡ عَلَى ٱللَّهِۚ وَكَفَىٰ بِٱللَّهِ وَكِيلًا

Amati: “Tikumvera.” Koma akachoka kwa iwe, gulu lina la iwo limapangana usiku zosagwirizana ndi zomwe ukunena (pamaso pawo). Koma Allah akulemba zonse zomwe akupangana. Choncho apatukire ndipo yadzamira kwa Allah. Ndipo Allah wakwanira kukhala Mtetezi. info
التفاسير:

external-link copy
82 : 4

أَفَلَا يَتَدَبَّرُونَ ٱلۡقُرۡءَانَۚ وَلَوۡ كَانَ مِنۡ عِندِ غَيۡرِ ٱللَّهِ لَوَجَدُواْ فِيهِ ٱخۡتِلَٰفٗا كَثِيرٗا

Kodi bwanji sakuilingalira Qur’an? Ndipo ikadakhala kuti siikuchokera kwa Allah, ndithudi, mmenemo akadapeza kusiyana kwambiri.[134] info

[134] M’ndime iyi akuti Qur’an iyi mawu ake ngolingana. Siotsutsana ayi. Ndipo palibe amene angabweretse mtsutso wakuti mawu ena omwe ali m’bukuli ngabodza pa chifukwa chakutichakuti. Palibe buku lomwe munthu adalemba lomwe lidabweretsa mtsutso weniweni wakuti Qur’an simawu a Allah pachifukwa chakutichakuti. Ndipo silidzapezeka buku lotero mpaka dziko lapansi lidzatha. Koma mwina anthu akhoza kumayankhula chabe popanda kubwera ndi mtsutso weniweni wokhala ndi umboni wooneka. Kuona kwa Qur’an kwatsimikizika pa zinthu izi:- Qur’an idafotokoza nkhani zakale zomwe zidachitika Mtumiki Muhammad (s.a.w) asanabadwe pomwe iye sankadziwa kulemba ndi kuwerenga mabuku. Quran idafotokozanso zamtsogolo. Ndipo zina mwa izo zaonekera kale poyera: Qur’an idati: (1) “Chinthu chilichonse pali chachimuna ndi chachikazi”. Yang’anani ndime ya 36 ya Sûrat Yasin. (2) Kuti dziko lapansili lidalumikizana ndi kumwamba monga ikufotokozera Sûrat Anbiyaa ndime ya 30. (3) Kuti moyo umadalira madzi, monga momwe ndime ya 30 ya m’Sûrat Anbiyaa ikulongosolera. (4) Kuti anthu amene ali kutali kwambiri adzatha kumva zimene anthu ena akutali akunena. Monga momwe yafotokozera ndime ya 44 ya m’Sûrat Aaraf. (5) Ndi kuti anthu adzakwera kumwamba monga momwe ikulongosolera ndime ya 13 ya m’Sûrat Jathiya. Mu Qur’an muli zambiri zimene adafotokoza kuti zidzachitika mtsogolo. Ndipo zambiri mwa izo zachitikadi, anthu aziona. Ndipo zonsezi zikutsimikizira kuti Qur’an ndi mawu a Allah.

التفاسير:

external-link copy
83 : 4

وَإِذَا جَآءَهُمۡ أَمۡرٞ مِّنَ ٱلۡأَمۡنِ أَوِ ٱلۡخَوۡفِ أَذَاعُواْ بِهِۦۖ وَلَوۡ رَدُّوهُ إِلَى ٱلرَّسُولِ وَإِلَىٰٓ أُوْلِي ٱلۡأَمۡرِ مِنۡهُمۡ لَعَلِمَهُ ٱلَّذِينَ يَسۡتَنۢبِطُونَهُۥ مِنۡهُمۡۗ وَلَوۡلَا فَضۡلُ ٱللَّهِ عَلَيۡكُمۡ وَرَحۡمَتُهُۥ لَٱتَّبَعۡتُمُ ٱلشَّيۡطَٰنَ إِلَّا قَلِيلٗا

Ndipo chikawadzera chinthu chilichonse chokhuza chitetezo kapena mantha, amachifalitsa. Koma akadachibwezera kwa Mtumiki ndi kwa omwe ali ndi udindo pa iwo, akadachidziwa omwe amafufuzafufuza zinthu mwa iwo (kuti kodi nzoyenera kuzifalitsa kapena ayi). Pakadapanda ubwino wa Allah ndi chifundo chake pa inu, ndithudi, mukadamtsatira satana kupatula ochepa. info
التفاسير:

external-link copy
84 : 4

فَقَٰتِلۡ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِ لَا تُكَلَّفُ إِلَّا نَفۡسَكَۚ وَحَرِّضِ ٱلۡمُؤۡمِنِينَۖ عَسَى ٱللَّهُ أَن يَكُفَّ بَأۡسَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْۚ وَٱللَّهُ أَشَدُّ بَأۡسٗا وَأَشَدُّ تَنكِيلٗا

Choncho menya nkhondo pa njira ya Allah, suukukakamizidwa (za anthu ena) koma iwe mwini, ndipo akhwirizire Asilamu. Ndithu Allah angatsekereze mtopola wa omwe sadakhulupirire. Ndipo Allah Ngwaukali kwambiri pomenya nkhondo ndiponso Wolanga kwabasi. info
التفاسير:

external-link copy
85 : 4

مَّن يَشۡفَعۡ شَفَٰعَةً حَسَنَةٗ يَكُن لَّهُۥ نَصِيبٞ مِّنۡهَاۖ وَمَن يَشۡفَعۡ شَفَٰعَةٗ سَيِّئَةٗ يَكُن لَّهُۥ كِفۡلٞ مِّنۡهَاۗ وَكَانَ ٱللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ مُّقِيتٗا

Amene angampemphere (mnzake) pempho labwino (lothandizira pa zabwino) adzapeza gawo mmenemo. Ndipo amene angampemphelere pemphero loipa, adzapeza gawo m’zoipazo. Ndipo Allah Ngodziwa chilichonse.[135] info

[135] M’ndime iyi akuwalangiza anthu kuti azithandizana pa zabwino zokha. Azithandizana pa zochita ndi zonena. Munthu akokere anzake kuzinthu zabwino mmene angathere. lyenso mwini athandize ena pazinthu zabwino. Akachita izi adzalandira mphoto yaikulu kwa Allah.

التفاسير:

external-link copy
86 : 4

وَإِذَا حُيِّيتُم بِتَحِيَّةٖ فَحَيُّواْ بِأَحۡسَنَ مِنۡهَآ أَوۡ رُدُّوهَآۗ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٍ حَسِيبًا

Ndipo pamene mwalonjeredwa; kulonjeredwa kwamtundu uliwonse (Salam) vomerani ndi malonje abwino oposa amenewo, kapena bwezani ofanana nawo. Ndithudi, Allah Ngowerengera chinthu chilichonse. info
التفاسير: