Traduzione dei Significati del Sacro Corano - Traduzione chicheŵa - Khalid Ibrahim Betyala

Numero di pagina:close

external-link copy
98 : 10

فَلَوۡلَا كَانَتۡ قَرۡيَةٌ ءَامَنَتۡ فَنَفَعَهَآ إِيمَٰنُهَآ إِلَّا قَوۡمَ يُونُسَ لَمَّآ ءَامَنُواْ كَشَفۡنَا عَنۡهُمۡ عَذَابَ ٱلۡخِزۡيِ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا وَمَتَّعۡنَٰهُمۡ إِلَىٰ حِينٖ

Kodi udalipo mudzi (ndi umodzi womwe pakati pa midzi mwa yomwe tidaiwononga), umene udalapa ndi kukhulupirira (pambuyo poona chilango kotero kuti) chikhulupiliro chake nkuuthandiza pa nthawi imeneyo, osati kupatula anthu a Yunus okha? Pamene adakhulupirira, tidawachotsera chilango choyalutsa m’moyo wa padziko lapansi, ndipo tidawasangalatsa kufikira nthawi yawo (yofera). info
التفاسير:

external-link copy
99 : 10

وَلَوۡ شَآءَ رَبُّكَ لَأٓمَنَ مَن فِي ٱلۡأَرۡضِ كُلُّهُمۡ جَمِيعًاۚ أَفَأَنتَ تُكۡرِهُ ٱلنَّاسَ حَتَّىٰ يَكُونُواْ مُؤۡمِنِينَ

Ndipo Mbuye wako akadafuna (kuwakakamiza anthu mwamphamvu kuti akhulupirire), onse ali m’dziko lapansi akadakhulupirira (sipakadatsala ndi mmodzi yemwe. Koma Allah safuna kukakamiza anthu mwamphamvu). Nanga kodi iwe uwakakamiza anthu kuti akhale okhulupirira? info
التفاسير:

external-link copy
100 : 10

وَمَا كَانَ لِنَفۡسٍ أَن تُؤۡمِنَ إِلَّا بِإِذۡنِ ٱللَّهِۚ وَيَجۡعَلُ ٱلرِّجۡسَ عَلَى ٱلَّذِينَ لَا يَعۡقِلُونَ

Ndipo palibe munthu angakhulupirire popanda chilolezo cha Allah. Iye amaachitira ukali amene alibe nzeru (amene sagwiritsa ntchito nzeru zawo). info
التفاسير:

external-link copy
101 : 10

قُلِ ٱنظُرُواْ مَاذَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ وَمَا تُغۡنِي ٱلۡأٓيَٰتُ وَٱلنُّذُرُ عَن قَوۡمٖ لَّا يُؤۡمِنُونَ

Nena: “Yang’anani nchiyani chikupezeka kumwamba ndi pansi!” Ndipo zisonyezo zonsezi ndi machenjezo onsewa sangawakwanire (ndi kuwapindulira kanthu) anthu osakhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
102 : 10

فَهَلۡ يَنتَظِرُونَ إِلَّا مِثۡلَ أَيَّامِ ٱلَّذِينَ خَلَوۡاْ مِن قَبۡلِهِمۡۚ قُلۡ فَٱنتَظِرُوٓاْ إِنِّي مَعَكُم مِّنَ ٱلۡمُنتَظِرِينَ

Kodi chiliponso chimene akudikira posakhala (kuwadzera) monga masiku (azilango zomwe zidawapeza) amene adapita kale (iwo asadafike)? Nena: “Dikirani nanenso ndili pamodzi nanu mwa odikira.” info
التفاسير:

external-link copy
103 : 10

ثُمَّ نُنَجِّي رُسُلَنَا وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْۚ كَذَٰلِكَ حَقًّا عَلَيۡنَا نُنجِ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ

Kenako tidzawapulumutsa atumiki Athu ndi amene adakhulupirira. Chotere nkoyenera kwa Ife kuwapulumutsa okhulupirira. info
التفاسير:

external-link copy
104 : 10

قُلۡ يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ إِن كُنتُمۡ فِي شَكّٖ مِّن دِينِي فَلَآ أَعۡبُدُ ٱلَّذِينَ تَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ وَلَٰكِنۡ أَعۡبُدُ ٱللَّهَ ٱلَّذِي يَتَوَفَّىٰكُمۡۖ وَأُمِرۡتُ أَنۡ أَكُونَ مِنَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ

Nena: “E inu anthu! Ngati inu muli ndi chipeneko pa chipembedzo changa, (dziwani kuti) sindingapembedze zimene mukuzipembedza kusiya Allah; koma ine ndipembedza Allah (Mmodzi yekha) Yemwe amakupatsani imfa (ndi moyo). Ndipo ndalamulidwa kukhala mmodzi wa okhulupirira.” info
التفاسير:

external-link copy
105 : 10

وَأَنۡ أَقِمۡ وَجۡهَكَ لِلدِّينِ حَنِيفٗا وَلَا تَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡمُشۡرِكِينَ

“Ndiponso (ndauzidwa kuti): ‘Lungamitsa nkhope yako kuchipembedzo momuyeretsera Allah mapemphero Ake, ndipo usakhale mmodzi mwa ophatikiza (Allah ndi zinthu zina).’ info
التفاسير:

external-link copy
106 : 10

وَلَا تَدۡعُ مِن دُونِ ٱللَّهِ مَا لَا يَنفَعُكَ وَلَا يَضُرُّكَۖ فَإِن فَعَلۡتَ فَإِنَّكَ إِذٗا مِّنَ ٱلظَّٰلِمِينَ

‘Ndipo (kuti), usapembedze chimene sichingakupindulitsire zabwino, kapena kukubweretsera masautso, kusiya Allah. Ngati utero ndiye kuti iwe ndi mmodzi wa oipa.” info
التفاسير: