Terjemahan makna Alquran Alkarim - Terjemahan Berbahasa Chichewa - Khalid Ibrahim Betala

Al-Mursalât

external-link copy
1 : 77

وَٱلۡمُرۡسَلَٰتِ عُرۡفٗا

Ndikulumbilira mphepo yomwe ikuomba motsatizana. info
التفاسير:

external-link copy
2 : 77

فَٱلۡعَٰصِفَٰتِ عَصۡفٗا

Ndi mphepo yamkuntho ikamakuntha. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 77

وَٱلنَّٰشِرَٰتِ نَشۡرٗا

Ndi mphepo yobalalitsa mitambo ndi mvula. info
التفاسير:

external-link copy
4 : 77

فَٱلۡفَٰرِقَٰتِ فَرۡقٗا

Ndi ma Ayah osiyanitsa pakati pachoona ndi chonama; info
التفاسير:

external-link copy
5 : 77

فَٱلۡمُلۡقِيَٰتِ ذِكۡرًا

Ndi angelo opereka chivumbulutso kwa aneneri. info
التفاسير:

external-link copy
6 : 77

عُذۡرًا أَوۡ نُذۡرًا

Kuti chichotse madandaulo kapena chikhale chenjezo; info
التفاسير:

external-link copy
7 : 77

إِنَّمَا تُوعَدُونَ لَوَٰقِعٞ

Ndithu zimene mukulonjezedwa (kuti chimaliziro chidzakhalapo) zidzachitikadi (popanda chipeneko), info
التفاسير:

external-link copy
8 : 77

فَإِذَا ٱلنُّجُومُ طُمِسَتۡ

Pamene nyenyezi zidzafafanizidwa (kuwala kwake ndi kuchotsedwa m’malo mwake). info
التفاسير:

external-link copy
9 : 77

وَإِذَا ٱلسَّمَآءُ فُرِجَتۡ

Ndiponso pamene thambo lidzang‘ambidwa. info
التفاسير:

external-link copy
10 : 77

وَإِذَا ٱلۡجِبَالُ نُسِفَتۡ

Ndi pamenenso mapiri adzachotsedwa m’malo mwake ndi kuperedwa (kukhala fumbi). info
التفاسير:

external-link copy
11 : 77

وَإِذَا ٱلرُّسُلُ أُقِّتَتۡ

Ndi pamene atumiki adzasonkhanitsidwa pa nthawi yake, (kuti apereke umboni ku mibadwo yawo). info
التفاسير:

external-link copy
12 : 77

لِأَيِّ يَوۡمٍ أُجِّلَتۡ

Kodi nditsiku lanji azichedwetsera (zinthu zikuluzikulu kuti zidzachitike)? info
التفاسير:

external-link copy
13 : 77

لِيَوۡمِ ٱلۡفَصۡلِ

Nditsiku loweruza (pakati pa zolengedwa). info
التفاسير:

external-link copy
14 : 77

وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا يَوۡمُ ٱلۡفَصۡلِ

Nchiyani chingakudziwitse za tsiku la chiweruzirolo? info
التفاسير:

external-link copy
15 : 77

وَيۡلٞ يَوۡمَئِذٖ لِّلۡمُكَذِّبِينَ

Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (lonjezo Lathu lakuuka ku imfa). info
التفاسير:

external-link copy
16 : 77

أَلَمۡ نُهۡلِكِ ٱلۡأَوَّلِينَ

Kodi sitidawaononge (anthu) akale (chifukwa cha machimo awo, monga anthu a Nuh, Âdi ndi Samudu)? info
التفاسير:

external-link copy
17 : 77

ثُمَّ نُتۡبِعُهُمُ ٱلۡأٓخِرِينَ

Kenako titsatiza ena (okana Allah m’kuonongekako monga tidawachitira oyamba), info
التفاسير:

external-link copy
18 : 77

كَذَٰلِكَ نَفۡعَلُ بِٱلۡمُجۡرِمِينَ

Chomwecho tiwachitiranso ochimwa. info
التفاسير:

external-link copy
19 : 77

وَيۡلٞ يَوۡمَئِذٖ لِّلۡمُكَذِّبِينَ

Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (lonjezo Lathu lakuuka ku imfa). info
التفاسير: