[118] Apa akuletsa kudyerana chuma m’njira yachinyengo. Koma kugulitsana malonda mwachimvano onse awiri nkomwe kukuloledwa. Ndipo Allah pomwe wanena kuti musadziphe, m’mawu amenewa mukutanthauza munthu kudzipha yekha, ndi kupha msilamu mnzake poti msilamu ndi msilamu mnzake ali ngati thupi limodzi. Ndipo ngakhale yemwe sali msilamu saloledwa kumupha. Mawu oti “kupha” akutanthauza kupha munthu nkuferatu nthawi yomweyo. Mawuwa akutanthauzanso kuchita chinthu chomwe chingamchititse munthu uja kuonongeka mwapang’onopang’ono mpaka mathero ake nkuferatu. Izi zili monga amene akumwa mowa wakachasu kapena wina uliwonse, akudzipha yekha. Kapenanso kuchita chinthu china chilichonse chomwe mathero ake chimamupha munthu. Ndipo nayenso amene akuthandizira zimenezi, ali m’gulu lakupha munthu.
[119] Apa akuti ngati tipewa machimo akuluakulu, Allah adzatikhululukira timachimo ting’onoting’ono. Munthu nkovuta kuupewa uchimo ung’onoung’ono. Uchimotu suli wofanana. Pali wina waukulu. Palinso wina wokulitsitsa. Ndipo pali waung’ono ndi wina wochepetsetsa.
Machimo akuluakulu ali ngati awa: (a) Kuphatikiza Allah ndi mafano. (b) Kupha munthu wosalakwa. (c) Kuba. (d) Kuchita malonda akatapira (riba). (e) Kumwa zoledzeretsa. (f) Kuchita chiwerewere ndi zina zotero.
Tsono uchimo waung’ono uli monga: Kunena mawu osafunika ndi kuchiyang’ana chinthu choletsedwa ndi zina zotero zomwe nzovuta munthu kuzipewa. Choncho, munthu akapewa machimo akuluakulu ndiye kuti adzamkhululukira machimo ang’onoang’ono ngati sakuwachita mochulukitsa.
Enanso mwa machimo akuluakulu ndikusiya kutsata malamulo a Allah, monga (a) Kusiya kupemphera Swala zisanu. (b) Kusiya kupereka Zakaat ndi zithandizo zina zofunika. (c) Kusiya kumanga m’mwezi wa Ramadan. (d) Kusiya kuchita Hajj. (e) Kusiya kuyang’anira makolo ndi zina zotero.
[120] Apa akuletsa anthu kuchitirana dumbo. Koma chofunika nkuti munthu alimbike kugwira ntchito kuti nayenso apeze chomwe mnzake wapeza. Osati kumchitira dumbo ndi kumuda, pakuti iye palibe chimene wakulanda. Adagwira ntchito molimbika ndipo Allah wampatsa. Iwenso limbikira kugwira ntchito Allah akupatsa. Wopemphedwa ndi kupatsa ndiyemweyo Allah wathu.
[121] Nthawi ya umbuli, munthu ankati akatenga mwana wa munthu wina nkumulera ankamuyesa mwana wake weniweni pomulowera chokolo pa chilichonse ngati mwanayo atafa. Ngakhale makolo ake enieni ndi abale ake atakhalapo sadali kuwagawira chilichonse. Tsono Chisilamu chidathetsa mchitidwe umenewu ponena kuti munthu aliyense azimlowa chokolo ndi abale ake.