[114] (Ndime 15-16) Izi ndi ndime zimene zikufotokoza za zilango zolanga nazo awa:-
a) Akazi amene amachitana ukwati akazi okhaokha
b) Amuna amene amachitana ukwati amuna okhaokha
c) Akazi ndi amuna amene akuchitana ukwati pamalo achabe a pathupi. Zinthu zonsezi nzoipa kwabasi.
[115] Ndime iyi ikusonyeza kuti Allah amalandira kulapa kuchokera kwa aliyense amene walapa. Komatu kuti kulapako kuvomerezeke, pafunika zinthu ziwiri:-
a) Akachita uchimo alape mwachangu. Osati azingopitiriza kulakwako mpaka akadzaona kuti ali pafupi kufa ndiye nkuyamba kulapa, zoterezi iyayi.
b) Uchimowo ukhale kuti adauchita chifukwa cha umbuli. Apa zikutanthauza kuti panthawiyo iye adadzazidwa ndi zilakolako za uchimo ndipo zidamchititsa kuti achimwe. Koma osati tchimolo likhale lolichita tsiku ndi tsiku popanda kulabadira chilichonse. Kulapa kwa uchimo wotero Allah sangakulandire. Ndipo mmalo mwake akamulanga ndi chilango chaukali.
[116] Nthawi ya umbuli, chikhalidwe cha Arabu chidali chonchi:- Tate wa munthu akamwalira ana ake amamlowera chokolo akazi ake omwe sadabereke anawo. Mwana aliyense amalowa chokolo mwa mkazi watate wake yemwe sadali mayi wake wom’bala.
a) Akafuna kumkwatira adali kumtenga.
b) Ndipo akafuna kumkwatitsa kwa mwamuna wina, amamlamula ndalama mwamunayo iye natenga ndalamazo.
c) Kapena amangomuvutitsavutitsa kuti akafuna adziombole yekha pomlipira ndalama mwanayo.
d) Kapena amangommanga kuti asakwatiwenso mpaka imfa yake. Choncho apa Allah akuletsa machitidwe oipawa.