[156] Nyama imene aizinga ndi cholinga china, osati ncholinga cha Allah monga:-
(1) Nyama imene aizinga chifukwa chotsirika nyumba kuti ziwanda zisamavutitsemo, kapena nyama imene aizinga pofuna kutsirika mudzi, kapena kuti chaka chino tikapanda kuzinga nyama kubwera matsoka akutiakuti
(2) Nyama imene aizinga pofuna kusangalatsa chiwanda cham’nyumba kapena cham’munda.
(3) Nyama imene aizinga pofuna kutsirika ukwati kuti ulimbe kapena pofuna kutsirika yemwe wabwera kuulendo kuti asamlodze.
(4) Nyama imene aizinga ncholinga choti akataye bwino maliro, ndi kuti mzimu wamalirowo usavutitse anthu pamudzi; nyama zonse zimene zazingidwa ndizolinga monga izi tatchulazi, nzoletsedwa kuzidya. Ndipo kunena koti: “Chimene chafa ndikumenyedwa ncholetsedwa koma pokhapokha mutachipeza chili moyobe nimuchizinga,” tanthauzo lake nkuti nyama imene imadyedwa ngati itafa pazifukwa zina zilizonse, monga kugundidwa ndi galimoto ndi zina zotero ndipo nyamayo sinaferetu kotero kuti nkutheka kuizinga, nyama yotero njololedwa kudya.
[157] Mbalame ndi nyama zimene zaloledwa kuzisaka mwaulenje kupyolera mwambalame kapena mwanyama zinzake zomwe anaziphunzitsa kusaka, ndipo mbalamezo kapena nyamazo nkufa chifukwa chakulumidwa ndi mbalame kapena nyama zosakazo, zikuloledwa kuzidya ngakhale kuti sanazizinge. Koma ngati atazipeza zikalipobe ndi moyo, azizinge.
[158] Chakudya chozingidwa sichingakhale chovomerezeka kwa Asilamu pokhapokha chitazingidwa ndi Asilamu. Izi zili ngati atatsatira malamulo akazingidwe, osati kupotokola khosi, kapena kumenya ndimyala kapena chibonga. Tsono chakudya chozingidwa nchovomerezeka kwa Msilamu kuchidya ngakhale chitakonzedwa ndi achikunja (akafiri) ngati:- (a) simudaone kuti athiramo najisi (uve) (b) Sichili chakudya choletsedwa. Nkovomerezeka kwa mwamuna wa Chisilamu kukwatira:- (a) Mkazi wa Chiyuda (b) Mkazi wa Chikhrisitu ngati makolo awo adali Ayuda kapena Akhrisitu chisilamu chisanadze.
N.B! Koma awa a Mishoni omwe alowa m’Chikhrisitu posachedwapa nkosaloledwa kuwakwatira pokhapokha atayamba alowa m’Chisilamu Tsono mkazi wa Chisilamu nkosaloledwa kukwatiwa ndi myuda kapena mkhrisitu. Ndipo apa apitirizanso machitidwe achiwerewere chomangira nyumba ndi chapatchire. Munthu akafuna kukwatira mkazi atsate mfundo zikudzazi kuti ukwati wakewo ukhale wovomerezeka pa malamulo a Chisilamu:- (a) Mkazi alole kukwatiwa ndi mwamunayo. (b) Myang’aniri wa wamkazi apereke kwa munthu chilolezo choti akwatitsire mkazi uja, kapena amkwatitse iye mwini pomuuza mkwati kuti “Ndakukwatitsa uje mwana wa uje.’’ (c) Mkwati avomereze kuti: “Ndavomera kumkwatira uje, mwana wa uje’.’ (d) Pakhale anthu aamuna oikira umboni osachepera pa awiri. Anthuwo akhale aulemu wawo pamaso pa anthu. (e) Chiperekedwe chiongo. (f) Iwerengedwe khutba ya ukwati.