[186] Mmene ilili nthaka yopanda chonde pomeretsa mmera movutikira nchimodzimodzi ndi anthu oipa. Nkovuta kuwaika pa njira yabwino. Koma tisatope ndi kutaya mtima nawo. Tiyesetsebe kuwakokera ku njira yabwino.
[187] Nkhani ya Mneneri Nuh paliponse akuifotokoza motalikitsa. Koma m’sura iyi aifotokoza mwachidule. Ndipo Nuh ndimneneri wakale kwabasi. Iye adali kuwalalikira anthu a ku Iraq. Ndipo m’nthawi imeneyo pafupifupi dziko lonse lapansi chitukuko chidali ku Iraq monga momwe tikuwerengera m’mabuku ambiri yakale.