Traduction des sens du Noble Coran - La traduction tchétchène - Khâlid Ibrâhîm Bîtâlâ

Numéro de la page:close

external-link copy
13 : 67

وَأَسِرُّواْ قَوۡلَكُمۡ أَوِ ٱجۡهَرُواْ بِهِۦٓۖ إِنَّهُۥ عَلِيمُۢ بِذَاتِ ٱلصُّدُورِ

Ndipo bisani mawu anu, kapena aonetseni poyera; (zonsezi nchimodzimodzi kwa Allah) ndithudi Iye Ngodziwa zobisika za m’mitima. info
التفاسير:

external-link copy
14 : 67

أَلَا يَعۡلَمُ مَنۡ خَلَقَ وَهُوَ ٱللَّطِيفُ ٱلۡخَبِيرُ

Kodi asadziwe amene adalenga (zinthu zonse)? Pomwe Iye Ngodziwa zinthu zingo’nozing’no kwambiri mmene zilili (ndiponso) Ngodziwa nkhani zonse. info
التفاسير:

external-link copy
15 : 67

هُوَ ٱلَّذِي جَعَلَ لَكُمُ ٱلۡأَرۡضَ ذَلُولٗا فَٱمۡشُواْ فِي مَنَاكِبِهَا وَكُلُواْ مِن رِّزۡقِهِۦۖ وَإِلَيۡهِ ٱلنُّشُورُ

Iye ndi Amene wakupangirani nthaka kuti ikhale yogonjera (pa chilichonse chimene mufuna). Choncho yendani mbali zake zonse; ndipo idyani rizq lake, (limene Allah akukutulutsirani). Ndipo kwa Iye Yekha ndiko kobwerera kwanu (nonse mutapatsidwa moyo wachiwiri). info
التفاسير:

external-link copy
16 : 67

ءَأَمِنتُم مَّن فِي ٱلسَّمَآءِ أَن يَخۡسِفَ بِكُمُ ٱلۡأَرۡضَ فَإِذَا هِيَ تَمُورُ

Kodi muli m’chitetezo kwa Amene ali kumwamba kuti sangakukwilireni m’nthaka (ndikukudzidzimutsani) pamene nthaka ikugwedezeka molimba? info
التفاسير:

external-link copy
17 : 67

أَمۡ أَمِنتُم مَّن فِي ٱلسَّمَآءِ أَن يُرۡسِلَ عَلَيۡكُمۡ حَاصِبٗاۖ فَسَتَعۡلَمُونَ كَيۡفَ نَذِيرِ

Kapena muli m’chitetezo kwa Amene ali kumwamba kuti sangakutumizireni mphepo yamkuntho ya miyala (ndi kukuonongani ndi miyalayo?) Choncho mdzadziwa mmene lilili chenjezo Langa (pa inu). info
التفاسير:

external-link copy
18 : 67

وَلَقَدۡ كَذَّبَ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡ فَكَيۡفَ كَانَ نَكِيرِ

Ndithudi amene adalipo kale iwo asanabadwe adakana mithenga yawo. Nanga udali bwanji mkwiyo Wanga pa iwo (pakuwaononga onse)! info
التفاسير:

external-link copy
19 : 67

أَوَلَمۡ يَرَوۡاْ إِلَى ٱلطَّيۡرِ فَوۡقَهُمۡ صَٰٓفَّٰتٖ وَيَقۡبِضۡنَۚ مَا يُمۡسِكُهُنَّ إِلَّا ٱلرَّحۡمَٰنُۚ إِنَّهُۥ بِكُلِّ شَيۡءِۭ بَصِيرٌ

Kodi, sadaone mbalame pamwamba pawo mmene zikutambasulira (mapiko ake) ndi kuwafumbata. Palibe amene akuzigwira kuti zisagwe koma (Allah) Wachifundo chambiri; ndithudi Iye pachilichonse Ngopenya. info
التفاسير:

external-link copy
20 : 67

أَمَّنۡ هَٰذَا ٱلَّذِي هُوَ جُندٞ لَّكُمۡ يَنصُرُكُم مِّن دُونِ ٱلرَّحۡمَٰنِۚ إِنِ ٱلۡكَٰفِرُونَ إِلَّا فِي غُرُورٍ

Kodi ndani amene ali asilikali anu okutetezani kuchilango posakhala (Allah) Wachifimdo chambiri? Ndithudi osakhulupirira ali mkunyengeka (pa zimene akuganizira). info
التفاسير:

external-link copy
21 : 67

أَمَّنۡ هَٰذَا ٱلَّذِي يَرۡزُقُكُمۡ إِنۡ أَمۡسَكَ رِزۡقَهُۥۚ بَل لَّجُّواْ فِي عُتُوّٖ وَنُفُورٍ

Kodi ndani uyo amene angakupatseni rizq (limene mungakhalire ndi moyo ndi kupezera mtendere) ngati Iye atatsekereza rizq Lake (kwa inu)? Koma Akafiri akupitiriza kudzikweza kwawo, ndi kudziika kutali ndi choonadi. info
التفاسير:

external-link copy
22 : 67

أَفَمَن يَمۡشِي مُكِبًّا عَلَىٰ وَجۡهِهِۦٓ أَهۡدَىٰٓ أَمَّن يَمۡشِي سَوِيًّا عَلَىٰ صِرَٰطٖ مُّسۡتَقِيمٖ

Kodi amene akuyenda mozyolika ndi nkhope yake angakhale wolungama kapena amene akuyenda moongoka panjira yosakhota? info
التفاسير:

external-link copy
23 : 67

قُلۡ هُوَ ٱلَّذِيٓ أَنشَأَكُمۡ وَجَعَلَ لَكُمُ ٱلسَّمۡعَ وَٱلۡأَبۡصَٰرَ وَٱلۡأَفۡـِٔدَةَۚ قَلِيلٗا مَّا تَشۡكُرُونَ

Nena: “Iye ndi Amene adakulengani (pomwe simudali kanthu) ndipo adakupatsani makutu, maso ndi mitima, (zimene mukhoza kupeza nazo mtendere). Koma kuyamika kwanu (kwa Yemwe adakupatsani zimenezi) nkochepa kwambiri. info
التفاسير:

external-link copy
24 : 67

قُلۡ هُوَ ٱلَّذِي ذَرَأَكُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَإِلَيۡهِ تُحۡشَرُونَ

Nena: “Iye ndi amene adakuchulukitsani pa dziko ndipo kwa Iye (Yekha) ndiko mudzasonkhanitsidwa (kuti adzakuwerengereni ndi kukulipirani). info
التفاسير:

external-link copy
25 : 67

وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هَٰذَا ٱلۡوَعۡدُ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ

Akunena (monyada osakhulupirira za kuuka): “Ndiliti (lidzakwaniritsidwa) lonjezo ili ngati inu muli owona?” info
التفاسير:

external-link copy
26 : 67

قُلۡ إِنَّمَا ٱلۡعِلۡمُ عِندَ ٱللَّهِ وَإِنَّمَآ أَنَا۠ نَذِيرٞ مُّبِينٞ

Nena (iwe Mtumiki{s.a.w}): “Ndithu kudziwa (kwa izi) nkwa Allah yekha, ndipo ndithudi ine, ndine mchenjezi wowonekera.” info
التفاسير: