Traduction des sens du Noble Coran - La traduction tchétchène - Khâlid Ibrâhîm Bîtâlâ

Numéro de la page:close

external-link copy
61 : 43

وَإِنَّهُۥ لَعِلۡمٞ لِّلسَّاعَةِ فَلَا تَمۡتَرُنَّ بِهَا وَٱتَّبِعُونِۚ هَٰذَا صِرَٰطٞ مُّسۡتَقِيمٞ

Ndipo iye (Isa (Yesu) adzakhala chizindikiro cha Qiyâma (kuti yayandikira). Choncho musaikaikire, koma nditsatireni. Imeneyi ndi njira yolunjika. info
التفاسير:

external-link copy
62 : 43

وَلَا يَصُدَّنَّكُمُ ٱلشَّيۡطَٰنُۖ إِنَّهُۥ لَكُمۡ عَدُوّٞ مُّبِينٞ

Asakutsekerezeni satana; iye kwa inu ndi mdani woonekera. info
التفاسير:

external-link copy
63 : 43

وَلَمَّا جَآءَ عِيسَىٰ بِٱلۡبَيِّنَٰتِ قَالَ قَدۡ جِئۡتُكُم بِٱلۡحِكۡمَةِ وَلِأُبَيِّنَ لَكُم بَعۡضَ ٱلَّذِي تَخۡتَلِفُونَ فِيهِۖ فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ

Ndipo pamene Isa (Yesu) adadza ndi zisonyezo zoonekera poyera, adati: “Ndakudzerani ndi nzeru (yopindulitsa), ndikuti ndikulongosolereni zina zimene mudali kusiyana mu izo; choncho, muopeni Allah ndiponso ndimvereni.” info
التفاسير:

external-link copy
64 : 43

إِنَّ ٱللَّهَ هُوَ رَبِّي وَرَبُّكُمۡ فَٱعۡبُدُوهُۚ هَٰذَا صِرَٰطٞ مُّسۡتَقِيمٞ

“Ndithu Allah ndiye Mbuye wanga ndi Mbuye wanunso; choncho mupembedzeni; imeneyi ndiyo njira yolunjika.” info
التفاسير:

external-link copy
65 : 43

فَٱخۡتَلَفَ ٱلۡأَحۡزَابُ مِنۢ بَيۡنِهِمۡۖ فَوَيۡلٞ لِّلَّذِينَ ظَلَمُواْ مِنۡ عَذَابِ يَوۡمٍ أَلِيمٍ

Koma magulu adasemphana pakati pawo. Ndipo kuonongeka kuchokera mu chilango cha tsiku lowawa kudzakhala pa amene adzichitira okha zoipa. info
التفاسير:

external-link copy
66 : 43

هَلۡ يَنظُرُونَ إِلَّا ٱلسَّاعَةَ أَن تَأۡتِيَهُم بَغۡتَةٗ وَهُمۡ لَا يَشۡعُرُونَ

Palibe chimene akuyembekeza, koma Qiyâma basi yomwe iwadzera mwadzidzidzi pomwe iwo sakuzindikira (ali otanganidwa ndi za m’dziko). info
التفاسير:

external-link copy
67 : 43

ٱلۡأَخِلَّآءُ يَوۡمَئِذِۭ بَعۡضُهُمۡ لِبَعۡضٍ عَدُوٌّ إِلَّا ٱلۡمُتَّقِينَ

Abwenzi tsiku limenelo adzakhala odana, wina ndi mnzake, (chifukwa chakuti adali kuthandizana pa zinthu zosalungama ndi zamachimo) kupatula oopa Allah (amene adachita chibwenzi mwa Allah, pothandizana kukwaniritsa malamulo a Allah ndi kusiya zimene Allah waletsa). info
التفاسير:

external-link copy
68 : 43

يَٰعِبَادِ لَا خَوۡفٌ عَلَيۡكُمُ ٱلۡيَوۡمَ وَلَآ أَنتُمۡ تَحۡزَنُونَ

(Allah adzati): E inu akapolo Anga (abwino)! Palibe kuopa kwa inu lerolino ndiponso simudandaula. info
التفاسير:

external-link copy
69 : 43

ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ بِـَٔايَٰتِنَا وَكَانُواْ مُسۡلِمِينَ

Amene adakhulupirira zisonyezo Zathu ndipo adali Asilamu (ogonjera Allah). info
التفاسير:

external-link copy
70 : 43

ٱدۡخُلُواْ ٱلۡجَنَّةَ أَنتُمۡ وَأَزۡوَٰجُكُمۡ تُحۡبَرُونَ

Lowani ku Munda wamtendere, inu ndi akazi anu musangalatsidwa. info
التفاسير:

external-link copy
71 : 43

يُطَافُ عَلَيۡهِم بِصِحَافٖ مِّن ذَهَبٖ وَأَكۡوَابٖۖ وَفِيهَا مَا تَشۡتَهِيهِ ٱلۡأَنفُسُ وَتَلَذُّ ٱلۡأَعۡيُنُۖ وَأَنتُمۡ فِيهَا خَٰلِدُونَ

Adzakhala akupititsidwa mbale zagolide ndi matambula (agolide); zonse zokomera moyo zidzakhala mmenemo ndi zokomera maso, ndipo inu mudzakhala mmenemo nthawi yaitali. info
التفاسير:

external-link copy
72 : 43

وَتِلۡكَ ٱلۡجَنَّةُ ٱلَّتِيٓ أُورِثۡتُمُوهَا بِمَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ

Ndipo umeneo ndi munda umene mwapatsidwa chifukwa cha (zabwino) zimene munkachita. info
التفاسير:

external-link copy
73 : 43

لَكُمۡ فِيهَا فَٰكِهَةٞ كَثِيرَةٞ مِّنۡهَا تَأۡكُلُونَ

Inu mupeza mmenemo zipatso zambiri zomwe muzidya. info
التفاسير: