Traduction des sens du Noble Coran - La traduction tchétchène - Khâlid Ibrâhîm Bîtâlâ

At-Takâthur

external-link copy
1 : 102

أَلۡهَىٰكُمُ ٱلتَّكَاثُرُ

Kwakutangwanitsani kusonkhanitsa (chuma chambiri ndi ana).[477] info

[477] (Ndime 1-2) Ndi chizolowezi cha anthu kupikisana pa chuma ndi pa ana. Choncho, mma Ayah awa: 1-2 Allah akuwauza: Kupikisana kwawo kochuluka, kukonda za m’dziko kwambiri, kwaiwalitsa kutumikira Allah mpaka imfa kuwapeza.

التفاسير:

external-link copy
2 : 102

حَتَّىٰ زُرۡتُمُ ٱلۡمَقَابِرَ

Mpakana mwapita kumanda (mwamwalira ndikukalowa m’manda). info
التفاسير:

external-link copy
3 : 102

كَلَّا سَوۡفَ تَعۡلَمُونَ

Sichoncho! Mudziwa posachedwapa.[478] info

[478] Tanthauzo lake ndilakuti, pamene idzakufikirani imfa mudzadziwa kuti mudali kutaya nthawi ndi zinthu zopanda pake.

التفاسير:

external-link copy
4 : 102

ثُمَّ كَلَّا سَوۡفَ تَعۡلَمُونَ

Ndiponso sichoncho! Mudziwa posachedwapa. info
التفاسير:

external-link copy
5 : 102

كَلَّا لَوۡ تَعۡلَمُونَ عِلۡمَ ٱلۡيَقِينِ

Sichoncho! mukadakhala mukudziwa, kudziwa kwachitsimikizo (sibwenzi mukutangwanika ndi za mdziko). info
التفاسير:

external-link copy
6 : 102

لَتَرَوُنَّ ٱلۡجَحِيمَ

Ndithudi mudzauona Moto. info
التفاسير:

external-link copy
7 : 102

ثُمَّ لَتَرَوُنَّهَا عَيۡنَ ٱلۡيَقِينِ

Kenako mudzauona ndithu ndi diso lachitsimikizo. info
التفاسير:

external-link copy
8 : 102

ثُمَّ لَتُسۡـَٔلُنَّ يَوۡمَئِذٍ عَنِ ٱلنَّعِيمِ

Tsono patsikulo ndithudi mudzafunsidwa za mtendere (omwe munapatsidwa).[479] info

[479] Munthu aliyense ndi chilichonse chimene ali nacho ndi mphatso yochokera kwa Allah. Choncho, pa tsiku lachimaliziro adzafunsidwa za momwe adagwiritsira ntchito mphatso zimenezi, kaya m’njira yoipa kapena yabwino.

التفاسير: