[455] Allah wakukweza kutchulidwa kwa Mtumiki Muhammad (s.a.w) pakumpatsa uneneri kumchitira zabwino kuposa aneneri ena, kuchipanga chipembedzo chake kukhala chotsiriza chosafafanizidwa ndi Mtumiki wina. Ndipo ndichopambana kuposa zipembedzo zonse zomwe zidatsogola, ndiponso ndi chomwe chingawathandize anthu onse osiyana mitundu, pa nyengo zonse ndi pamalo paliponse.
[456] Tanthauzo lake nkuti: “Ukamaliza ntchito yako yolalikira kwa anthu zomwe Allah wakutuma kuti ulalikire, chita mapemphero ambiri. Umthokoze Mbuye wako pa chisomo Chake chimene wakudalitsa nacho.” Mneneri (s.a.w) adali kulimbikira kwambiri pochita mapemphero mwakuti amaima ndi kumapemphera kufikira miyendo yake kutupa. Amagwetsa mphumi pansi (sijida) mpaka kuganiziridwa kuti wafa chifukwa cha kutalika kwa nthawi yopempherayo.