[347] Arabu adali ndi chizolowezi chakupatukana ndi mkazi ponena mawu akuti: “Ndikukuyerekeza ngati mayi wanga.” Choncho amangokhala naye mkazi uja, osamkhudza ndiponso osamulola kuti akwatiwe ndi mwamuna wina. Samamchitiranso zimene munthu amachitira mkazi wake monga kumveka ndi kumdyetsa. Msilamu wina adamsiya mkazi masiyidwe onga amenewa ndipo mkazi uja adapita kukakambirana naye Mtumiki (s.a.w). Choncho Chisilamu chidaletsa machitidwe onga amenewa.
[348] M’ndime iyi, Allah akutichenjeza kuti pamene tikuchita kalikonse tisamaganizire kuti Allah sakutiona. Palibe chimene chingabisike kwa Allah cha m’dziko lapansi kapena kumwamba; m’zoyankhula kapena m’zochitachita.
[349] Ayuda amamlonjera Mtumiki ndi mawu akuti: “Saamu alayikumu” kutanthauza kuti: Imfa ikhale pa inu. Amayankhula mokhotetsa lirime kuti ampusitse Mtumiki kuti aganizire kuti akumlonjera moyenera kuti: “Asalamu alayikumu.”
[350] Kuvumbulutsidwa kwa ndime iyi pali mawu akuti: Mtumiki (s.a.w) amaikira mtima kwambiri pa anthu amene adamenya nkhondo ya Badir; amgulu la Amuhajirina ndi Answari. Ndipo ena mwa iwowa adadza pa bwalo la Mtumiki ndi kupeza anthu ena atakhala kale adakhala chiimire chifukwa chosowa pokhala uku akuyembekezera kuti anzawo aja awapatseko pokhala; koma anthu adakhala kale aja sadalabadireko chilichonse. Mtumiki ataona izi zidamuwawa mu mtima ndipo adawauza omwe adakhala kale aja kuti aimilire apereke malo kwa anzawo. Achiphamaso adayamba kum’dzudzula Mtumiki (s.a.w) kuti bwanji akuchotsa anthu okhalakhala pamalo chifukwa cha anthu obwera mochedwa; sikupanda chilungamo kumeneko? Adatero achiphamaso aja. Ndipo poyankha zimenezi Allah adati: “E inu okhulupilira! Mukauzidwa kuti perekani malo kwa anzanu mupereke.” Ndipo mukauzidwa kuti imilirani, muimilire.”
M’ndime imeneyi Allah akutiphunzitsa kuti timvere Mtumiki (s.a.w) pa chilichonse chimene watilangiza popanda kuwiringula.
[351] Tanthauzo la “Kulumbira kwawo adakuchita chodzitetezera” ndiko kuti achiphamaso amadziteteza kwa Asilamu pakungosonyeza Chisilamu chachiphamaso, chapakamwa pokha pomwe mitima yawo siimakhulupilira. Amatero pakuopa kuti Asilamu angawachitire zimene amawachitira anthu osakhulupilira monga kuwathira nkhondo akaputidwa.
[352] M’ndime imeneyi Allah akunenetsa kuti: ‘‘Amene akukhulupilira mwa Allah ndi tsiku lachimaliziro, asapalane ubwenzi ndi munthu wodana ndi Allah ndi Mthenga Wake ngakhale wodana ndi Allah yo atakhala bambo wake, mwana wake ndi wina aliyense; apatukane nawo ndithu; chifukwa kupanda kutero akusonyeza kufooka kwa chikhulupiliro. Mtumiki (s.a.w) adati: “Munthu adzakhala ndi amene amamkonda pa tsiku la chiweruziro.”