Traducción de los significados del Sagrado Corán - Traducción al Chewa - Khaled Ibrahim Betala

external-link copy
106 : 5

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ شَهَٰدَةُ بَيۡنِكُمۡ إِذَا حَضَرَ أَحَدَكُمُ ٱلۡمَوۡتُ حِينَ ٱلۡوَصِيَّةِ ٱثۡنَانِ ذَوَا عَدۡلٖ مِّنكُمۡ أَوۡ ءَاخَرَانِ مِنۡ غَيۡرِكُمۡ إِنۡ أَنتُمۡ ضَرَبۡتُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ فَأَصَٰبَتۡكُم مُّصِيبَةُ ٱلۡمَوۡتِۚ تَحۡبِسُونَهُمَا مِنۢ بَعۡدِ ٱلصَّلَوٰةِ فَيُقۡسِمَانِ بِٱللَّهِ إِنِ ٱرۡتَبۡتُمۡ لَا نَشۡتَرِي بِهِۦ ثَمَنٗا وَلَوۡ كَانَ ذَا قُرۡبَىٰ وَلَا نَكۡتُمُ شَهَٰدَةَ ٱللَّهِ إِنَّآ إِذٗا لَّمِنَ ٱلۡأٓثِمِينَ

E inu amene mwakhulupirira! Pamene chamfikira mmodzi wa inu chisonyezo cha imfa, ndipo akufuna kusiya chilawo (wasiya) funani mboni ponena mawuwo. Aikire umboni awiri olungama mwa inu (Asilamu) kapena apadera ngati muli pa ulendo, ndipo zisonyezo za imfa zitaonekera. Ngati mutazikaikira zitsekerezeni (kuti zisachoke) mboni ziwiri pambuyo pa Swala (yomwe amasonkhana anthu ambiri), ndipo zilumbilire m’dzina la Allah kunena (kuti): “Sitikusinthanitsa malumbirowa ndi china chake ngakhale chitakhala chothandiza kwa ife kapena mmodzi mwa abale athu. Sitikubisa umboni umene Allah watilamula kuti tiupereke moona. Ife ngati titabisa umboni (kapena kuyankhula chonama), ndithudi tikhala mwa anthu ochimwa.” info
التفاسير: