Traducción de los significados del Sagrado Corán - Traducción al Chewa - Khaled Ibrahim Betala

Al-Ahqâf

external-link copy
1 : 46

حمٓ

۞ Hâ-Mîm. info
التفاسير:

external-link copy
2 : 46

تَنزِيلُ ٱلۡكِتَٰبِ مِنَ ٱللَّهِ ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡحَكِيمِ

Chivumbulutso cha bukuli nchochokera kwa Allah Wamphamvu zoposa, Wanzeru zakuya. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 46

مَا خَلَقۡنَا ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ وَمَا بَيۡنَهُمَآ إِلَّا بِٱلۡحَقِّ وَأَجَلٖ مُّسَمّٗىۚ وَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ عَمَّآ أُنذِرُواْ مُعۡرِضُونَ

Sitidangolenga thambo ndi nthaka ndiponso zonse zapakati pa izo koma mwachoonadi ndi nyengo yoikidwa (yodziwika). Koma amene akana kukhulupirira (Allah) ngonyozera zimene achenjezedwa. info
التفاسير:

external-link copy
4 : 46

قُلۡ أَرَءَيۡتُم مَّا تَدۡعُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ أَرُونِي مَاذَا خَلَقُواْ مِنَ ٱلۡأَرۡضِ أَمۡ لَهُمۡ شِرۡكٞ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِۖ ٱئۡتُونِي بِكِتَٰبٖ مِّن قَبۡلِ هَٰذَآ أَوۡ أَثَٰرَةٖ مِّنۡ عِلۡمٍ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ

Nena: Tandiuzani amene mukuwapembedza ndi kumusiya Allah, ndisonyezeni chimene adalenga panthaka? Kapena ali ndi gawo la kuthangata polenga thambo? Ndibweretsereni buku limene lidadza kale, ili lisanadze, kapena zizindikiro zanzeru, ngati inu mukunena zoona. info
التفاسير:

external-link copy
5 : 46

وَمَنۡ أَضَلُّ مِمَّن يَدۡعُواْ مِن دُونِ ٱللَّهِ مَن لَّا يَسۡتَجِيبُ لَهُۥٓ إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِ وَهُمۡ عَن دُعَآئِهِمۡ غَٰفِلُونَ

Kodi ndindani amene ali osokera kwambiri kuposa amene akupembedza zina kusiya Allah zomwe sizingathe kumuyankha mpaka tsiku la chiweruziro ndipo izo (zimafano) sizikuzindikira za mapemphero awo. info
التفاسير: