[379] (Ndime 1-5) M’Qur’an nthawi zambiri Allah amalumbilira zolengedwa Zake; zamoyo ndi zopanda moyo, zooneka ndi zosaoneka. Cholinga ndikutilimbikitsa kuti tikhale olingalira luso Lake pa chinthu chilichonse chimene wachilumbilira kuti tizindikire ulemelero Wake ndi mphamvu Zake zoposa.
[380] Kuyambira Ayah iyi mpaka Ayah 26 Allah akumtonthoza mneneri Wake pomuuza nkhani ya Mneneri Musa momwe Farawo adamkanira, ndikuti asaganize kuti vutoli lampeza iye yekha koma kuti aneneri enanso akale lidawaonekeranso. Ndiponso m’ma Ayah amenewa muli chenjezo kwa akafiri kuti aope Allah kuti asawalange monga adamulangira Farawo ndi anthu ake amene adali kutsutsana ndi Allah.