Translation of the Meanings of the Noble Qur'an - Chewa translation - Khaled Ibrahim Batyala

external-link copy
20 : 7

فَوَسۡوَسَ لَهُمَا ٱلشَّيۡطَٰنُ لِيُبۡدِيَ لَهُمَا مَا وُۥرِيَ عَنۡهُمَا مِن سَوۡءَٰتِهِمَا وَقَالَ مَا نَهَىٰكُمَا رَبُّكُمَا عَنۡ هَٰذِهِ ٱلشَّجَرَةِ إِلَّآ أَن تَكُونَا مَلَكَيۡنِ أَوۡ تَكُونَا مِنَ ٱلۡخَٰلِدِينَ

Choncho satana adawanong’oneza (zoipa) kuti awaonetsere zomwe zidabisika kwa iwo za maliseche awo. Ndipo (satana) adati: “Mbuye wanu sadakuletseni mtengo uwu, koma pachifukwa chakuti mungasanduke angelo awiri, kapena kuti mungakhale okhala nthawi yaitali.” info
التفاسير: